-
Oweruza 9:1, 2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Patapita nthawi, Abimeleki+ mwana wa Yerubaala, anapita ku Sekemu kwa azichimwene awo a mayi ake. Ndipo anauza amalume akewo komanso banja lonse la bambo a mayi ake kuti: 2 “Chonde funsani atsogoleri* onse a ku Sekemu kuti, ‘Chabwino nʼchiyani kwa inu, kuti ana onse 70 a Yerubaala+ azikulamulirani, ndi kuti azikulamulirani munthu mmodzi? Ndipo musaiwale kuti ine ndi inu ndife magazi amodzi.’”*
-