-
Mateyu 6:25-30Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
25 Pa chifukwa chimenechi, ndikukuuzani kuti: Siyani kudera nkhawa za moyo wanu,+ kuti mudzadya chiyani kapena kuti mudzamwa chiyani kapenanso kudera nkhawa za matupi anu kuti mudzavala chiyani.+ Kodi moyo si wofunika kwambiri kuposa chakudya ndipo kodi thupi si lofunika kwambiri kuposa chovala?+ 26 Yangʼanitsitsani mbalame zamumlengalenga,+ pajatu sizifesa mbewu kapena kukolola kapenanso kusunga chakudya mʼnyumba zosungiramo zinthu. Koma Atate wanu wakumwamba amazidyetsa. Kodi inu si amtengo wapatali kuposa mbalame? 27 Ndi ndani wa inu amene angatalikitse moyo wake pangʼono pokha* chifukwa cha kuda nkhawa?+ 28 Komanso nʼchifukwa chiyani mukudera nkhawa nkhani ya zovala? Phunzirani mmene maluwa akutchire amakulira. Sagwira ntchito ndiponso sawomba nsalu. 29 Komatu ndikukuuzani kuti ngakhale Solomo+ mu ulemerero wake wonse sanavalepo zokongola ngati lililonse la maluwa amenewa. 30 Ndiye ngati Mulungu amaveka chonchi zomera zakutchire, zimene zimangokhalapo lero lokha mawa nʼkuzisonkheza pamoto, kodi iye sadzakuvekani kuposa pamenepo achikhulupiriro chochepa inu?
-