Kodi Mungasonyeze Kuleza Mtima?
YEHOVA anauza Abramu kuti: “Tuluka iwe m’dziko lako, . . . kumka ku dziko limene ndidzakusonyeza iwe; ndipo ndidzakuyesa iwe mtundu waukulu, ndipo ndidzakudalitsa iwe, ndi kubukitsa dzina lako.” (Genesis 12:1, 2) Panthaŵiyo Abramu anali wazaka zakubadwa 75. Iye anamvera ndipo anasonyeza mwanzeru kuleza mtima m’moyo wake wonse, akumayembekezera pa Yehova.
Potsirizira pake, Mulungu anachita pangano limeneli ndi Abrahamu (Abramu) woleza mtima ameneyu kuti: “Kudalitsatu ndidzakudalitsa iwe, ndipo kuchulukitsa ndidzakuchulukitsa iwe.” Mtumwi Paulo anawonjezera kuti: “Ndipo potero atapirira analandira lonjezanolo.”—Ahebri 6:13-15.
Kodi kuleza mtima n’chiyani? Madikishonale amakufotokoza monga mkhalidwe wa kukhoza “kuyembekezera kanthu kena mwabata” kapena kusonyeza “kudziletsa pakuputidwa kapena kupsinjika.” Chotero kuleza mtima kwanu kumayesedwa pamene mufunikira kuyembekezera munthu wina kapena kanthu kena, kapena pamene muputidwa kapena pamene muli pansi pa chitsenderezo. M’mikhalidwe yotero munthu woleza mtima amakhalabe wabata; munthu wosaleza mtima amakhala waphuma ndi wa mtima wapachala.
Dziko Lathu Lamakono Losaleza Mtima
Makamaka m’madera ambiri a m’tauni, chigogomezero chachikulu sichimaikidwa pakuleza mtima koma kufulumira. Kwa mamiliyoni a anthu okhala m’mizinda ya anthu ambiri, tsiku lililonse limayamba pamene belu lammaŵa la koloko lilira. Limenelo limayambitsa mpikisano waukulu—kufika kwinakwake, kukaonana ndi winawake, kukapeza kanthu kenakake. Kodi nzodabwitsa kuti ambiri amakhala omangika thupi ndi osaleza mtima?
Kodi inu mumakwiya pamene muyang’anizana ndi zophophonya za ena? “Ndimadana ndi kusasunga nthaŵi,” akutero Albert. Ambiri angavomereze kuti kuyembekezera munthu wina amene wachedwa nkovutitsa maganizo, makamaka ngati mwapangana nthaŵi. Ponena za Duke of Newcastle, wandale wina wa ku Britain wa m’zaka za zana la 18, kunanenedwa za iye kuti: ‘Iye amachedwa ndi theka la ola m’maŵa, limene limampangitsa kuthamangathamanga pambuyo pake m’tsiku lonselo popanda kuwongolera mkhalidwewo.’ Ngati mukanati mudalire pamunthu wotero tsiku ndi tsiku, kodi mukanakhala woleza mtima?
Poyendetsa galimoto, kodi mumapsa mtima mofulumira, wosafuna kuyembekezera, kapena kulakalaka kuyendetsa galimoto paliŵiro lalikulu? M’mikhalidwe yotero, kaŵirikaŵiri kusaleza mtima n’kwatsoka. Mkati mwa 1989, m’limene panthaŵiyo linali dziko la West Germany, m’ngozi zoposa 400,000 za pamisewu yaikulu munavulala anthu kapena kufa. M’ngozi zimenezi, 1 pa 3 zinachititsidwa ndi kuyendetsa galimoto mwaliŵiro kwambiri kapena motsatizana kwambiri ndi lakutsogolo. Chifukwa chake, pamlingo winawake, kukhala wosaleza mtima kunavulaza kapena kupha anthu oposa 137,000. Ha, mphotho yake ya kusaleza mtima n’njoipa chotani nanga!
“Kuleza mtima kumandivuta pamene munthu wina andidodometsa nthaŵi zonse,” akudandaula motero Ann, “kapena pamene munthu wina adzitama kwambiri.” Karl-Hermann akuvomereza kuti kuleza mtima kwake kumatokosedwa ndi “achichepere amene samalemekeza achikulire.”
Imeneyi ndi mikhalidwe ina ingakuchititseni kukhala wosaleza mtima. Nangano, kodi ndimotani mmene mungakulitsire kuleza mtima?
Yehova Angathe Kulimbitsa Kuleza Mtima Kwanu
Anthu ambiri amaganiza kuti kuleza mtima kumasonyeza kuzengereza kapena kufooka. Komabe, kwa Yehova, ndiko chizindikiro cha nyonga. Iye mwiniyo “aleza mtima . . . wosafuna kuti ena awonongeke, koma kuti onse afike kukulapa.” (2 Petro 3:9) Chotero, kuti mulimbitse kudziletsa kwanu, yandikirani kwambiri kwa Yehova ndi kudalira pa iye ndi mtima wanu wonse. Kulimbitsa unansi wanu ndi Mulungu ndiko sitepe limodzi lofunika koposa pakukulitsa mkhalidwe wa kuleza mtima.
Ndiponso, nkofunika kudziŵa zifuno za Yehova kaamba ka dziko lapansi ndi mtundu wa anthu. Abrahamu “analindirira mudzi wokhala nawo maziko [Ufumu wa Mulungu], mmisiri wake ndi womanga wake ndiye Mulungu.” (Ahebri 11:10) Mofananamo, kudzakhala kopindulitsa kukhala ndi lingaliro looneka bwino la malonjezo aumulungu ndi kukhala wokhutira pakuyembekeza Yehova. Pamenepo mudzazindikira kuti kuleza mtima, kosiyana kwambiri ndi kusonyeza kuzengereza, kwenikweni kumapindula anthu kuwabweretsa m’kulambira koona. Chifukwa chake, “yesani kulekerera kwa Ambuye wathu chipulumutso.”—2 Petro 3:15.
Bwanji ngati mikhalidwe ya inu mwini iyesa kuleza mtima kwanu kukhala pafupifupi kosapiririka? Kodi osapembedza amakuikani pamkhalidwe wovutitsa maganizo? Kodi mwakhala mukudwala nthenda imene ikuonekera kukhala yosachiritsika kwanthaŵi yaitali? M’mikhalidwe yotero, khulupirirani zimene mtumwi Yakobo analemba. Atatchula za zitsanzo zimene aneneri anapereka m’kusonyeza kuleza mtima, iye anasonyeza chinsinsi cha kukhalabe wabata pansi pachitsenderezo chachikulu. Yakobo anati: “Kodi wina wa inu akumva zowawa? Apemphere.”—Yakobo 5:10, 13.
Pemphani Mulungu mwakhama m’pemphero kuti alimbitse kuleza mtima kwanu ndi kukuthandizani kulamulira mzimu wanu pansi pachiyeso. Tembenukirani kwa Yehova mobwerezabwereza, ndipo adzakuthandizani kudziŵa mikhalidwe kapena zizoloŵezi za ena zimene zimawopseza mtendere wanu. Kupempherera pasadakhale mikhalidwe yoyesa yothekera kungakuthandizeni kukhala ndi bata.
Lingaliro Loyenera la Inu Mwini ndi Ena
Kuti musunge mkhalidwe wamaganizo wabata, muyenera kudziona inu mwini ndi ena m’njira yoyenera. Zimenezi nzotheka kupyolera m’phunziro la Baibulo, pakuti limeneli limasonyeza kuti aliyense ali ndi choloŵa cha kupanda ungwiro ndipo chifukwa chake ali ndi zofooka zake. Ndiponso, chidziŵitso cha Baibulo chidzakuthandizani kukula m’chikondi. Mkhalidwe umenewu n’ngwofunika kotero kuti tisonyeze kuleza mtima kulinga kwa ena.—Yohane 13:34, 35; Aroma 5:12; Afilipi 1:9.
Chikondi ndi kufunitsitsa kukhululukira zingathe kukutonthozani pamene mukwiyitsidwa. Ngati winawake ali ndi zizoloŵezi zimene zimakunyong’onyani, chikondi chidzakukumbutsani kuti zili zizoloŵezizo zimene mumada, osati munthuyo. Lingalirani kuti ndi mwakaŵirikaŵiri motani mmene zofooka za inu mwini zimayesera kuleza mtima kwa Mulungu ndi mmene ziyenera kukhumudwitsira ena.
Lingaliro loyenera la inu mwini lidzakuthandizaninso kuyembekezera moleza mtima. Mwachitsanzo, kodi mwakhala mukukalimira mathayo muutumiki wa Yehova, koma mmalo mwake kugwiritsidwa mwala? Kodi mukuona kuti kuleza mtima kwanu kukutha mofulumira mofanana ndi nchenga wotsirizira m’galasi lopimira nthaŵi? Ngati zimenezo zili choncho, pamenepo kumbukirani kuti kusaleza mtima kwakukulu kumazikidwa pa kudzikuza. “Wofatsa mtima apambana wodzikuza mtima,” anatero Solomo. (Mlaliki 7:8) Inde, kudzikuza ndiko chododometsa chachikulu pakukulitsa kuleza mtima. Kodi sizoona kuti munthu wodzichepetsa amapeza kuti kuyembekezera mofatsa n’kosavuta? Chifukwa chake, kulitsani kudzichepetsa, ndipo mudzakhala wokhoza bwino kwambiri kulola kuyembekezera ndi mtendere wa maganizo.—Miyambo 15:33.
Kuleza Mtima Kumafupa Kwambiri
Abrahamu amadziŵika kwambiri chifukwa cha chikhulupiriro chake. (Aroma 4:11) Komabe, kuleza mtima kunachititsa chikhulupiriro chake kukhala cholimba. Kodi nchiyani chimene chinali mfupo yake chifukwa cha kuyembekezera pa Yehova?
Abrahamu anakhala ndi dalitso la kudaliridwa kwambiri ndi Yehova. Chotero dzina la Abrahamu linakhala lalikulu ndipo mbadwa zake zinakhala mtundu waukulu. Mitundu yonse ya padziko lapansi ikhoza kudzidalitsa kupyolera mwa mbewu yake. Abrahamu anatumikira monga wonenera wa Mulungu, Mlengi weniweniyo. Kodi Abrahamu akanakhalanso ndi mfupo ina yaikulu ya chikhulupiriro ndi kuleza mtima koposa imeneyi?
“[Yehova, NW] ali wodzala chikondi, ndi wachifundo” kwa Akristu amene amapirira ziyeso moleza mtima. (Yakobo 5:10, 11) Anthu otero amakhala ndi chikumbumtima choyera chifukwa cha kuchita chifuniro chake. Pamenepo, ponena za inu, ngati muyembekezera Yehova ndi kupirira ziyeso moleza mtima, kudziletsa kwanu kuzadzetsa chivomerezo ndi madalitso a Yehova.
Kuleza mtima kumachita zabwino kwa anthu a Mulungu m’mbali zonse za moyo. Atumiki ena aŵiri a Yehova, otchedwa Christian ndi Agnes, anadziŵa zimenezi pamene anasankha zotomerana. Iwo anachedwetsa kutomeranako chifukwa cha kulemekeza makolo a Christian, amene anafuna nthaŵi yodziŵana ndi Agnes. Kodi mchitidwe umenewu unali ndi chiyambukiro chotani?
“Tinazindikira pambuyo pake zimene kuleza mtima kwathuko kunatanthauza kwa makolo anga,” Christian akufotokoza motero. “Kuyembekezera moleza mtima kwathu sikunathetse unansi wathu pakati pa mkazi wanga ndi ine. Koma kunali ngati njerwa yoyamba m’kumanga unansi wathu ndi makolo anga.” Inde, kuleza mtima kumafupa kwambiri.
Kuleza mtima kumachirikizanso mtendere. Banja ndi mabwenzi adzakhala othokoza kuti simumakangana nawo pa chophophonya chawo chilichonse. Mkhalidwe wanu wabata ndi kuzindikira pamene ena apanga zolakwa udzaletsa mikhalidwe yochititsa manyazi. Mwambi wina wa ku China umati: “Kuleza mtima panyengo ya mkwiyo kudzakupulumutsani kwa masiku zana a mkwiyo.”
Kuleza mtima kumakulitsa umunthu wanu, kwenikweni kukumasunga mikhalidwe ina ili mumkhalidwe wabwino. Kumapangitsa chikhulupiriro chanu kukhala cholimba, mtendere wanu kukhala wokhalitsa, ndipo chikondi chanu kukhala champhamvu. Kukhala woleza mtima kudzakuthandizani kukhala wachisangalalo posonyeza kukoma mtima, ubwino, ndi chifatso. Kusonyeza kuleza mtima kumakulitsa nyonga yofunika kukulitsidwa ya kupirira ndi kudziletsa.
Pamenepotu, yembekezerani moleza mtima kaamba ka kukwaniritsidwa kwa malonjezo a Yehova, ndipo mukutsimikiziridwa za mtsogolo mokondweretsa. Monga Abrahamu, “mwa chikhulupiriro ndi kuleza mtima [mulandiretu malonjezowo, NW].”—Ahebri 6:12.
[Chithunzi patsamba 23]
Unansi wapafupi ndi Yehova udzakuthandizani kusonyeza kuleza mtima, monga momwe Abrahamu anachitira