Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chichewa
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • MISONKHANO
  • g19 No. 3 tsamba 6-7
  • Mtendere wa M’maganizo

Palibe Vidiyo.

Pepani vidiyoyi ikukanika kutsegula.

  • Mtendere wa M’maganizo
  • Galamukani!—2019
  • Timitu
  • Nkhani Yofanana
  • KUPSA MTIMA
  • KUYAMIKIRA
  • MFUNDO ZINA ZA M’BAIBULO
  • Kodi Baibulo Limanena Zotani pa Nkhani ya Kukwiya?
    Kuyankha Mafunso a M’Baibulo
  • “Kuzindikira Kumachititsa Munthu Kubweza Mkwiyo”
    Nsanja ya Olonda—2014
  • Kusamalira Mkwiyo—Wanu ndi wa Ena
    Nsanja ya Olonda—1987
  • Kodi Ndingalamulire Motani Kupsya Mtima Kwanga?
    Galamukani!—1987
Onani Zambiri
Galamukani!—2019
g19 No. 3 tsamba 6-7
Anthu ali pamzera kusitolo ndipo akwiya kwambiri kupatulapo mayi wina ndi mwana wake omwe akuoneka odekha

Mtendere wa M’maganizo

Baibulo limatilangiza kuti tizipewa makhalidwe omwe angativulaze monga kupsa mtima. Limatilimbikitsanso kuti tizikhala ndi makhalidwe abwino.

KUPSA MTIMA

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Munthu wosakwiya msanga ndi wabwino kuposa munthu wamphamvu.”​—Miyambo 16:32.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Timapindula kwambiri tikamayesetsa kuugwira mtima. N’zoona kuti nthawi zina tonsefe tikhoza kukwiya pazifukwa zomveka, koma kulekerera mkwiyo kwa nthawi yaitali kungatibweretsere mavuto aakulu. Ochita kafukufuku a masiku ano amanena kuti munthu amene amalephera kuugwira mtima amatha kulankhula kapena kuchita zinthu zimene pambuyo pake amanong’oneza nazo bondo.

ZIMENE MUNGACHITE: Musamalole kuti mkwiyo uzikulamulirani. Ena amaganiza kuti anthu amene sachedwa kupsa mtima ndi amphamvu, koma kunena zoona anthu amenewa ndi ofooka. Tikutero chifukwa Baibulo limati: “Munthu wosaugwira mtima ali ngati mzinda umene mpanda wake wagumulidwa, n’kuusiya wopanda mpanda.” (Miyambo 25:28) Chimene chingakuthandizeni kuti muziugwira mtima ndi kumvetsa kaye nkhani yonse musanachitepo kanthu. Pa nkhani imeneyi Baibulo limati: “Kuzindikira kumachititsa munthu kubweza mkwiyo wake.” (Miyambo 19:11) Tingachite bwino kumvetsa mbali zonse za nkhaniyo zomwe zingatithandize kubweza mkwiyo wathu.

KUYAMIKIRA

MFUNDO YA M’BAIBULO: “Sonyezani kuti ndinu oyamikira.”​—Akolose 3:15.

ZIMENE TIKUPHUNZIRAPO: Anthu amanena kuti munthu amene amakonda kuyamikira ena ndi amene amakhala wosangalala. Ngakhale anthu amene m’bale wawo wamwalira kapena zinthu zawo zonse zawonongeka, amavomereza mfundo imeneyi. Anthuwa amanena kuti chimene chimawathandiza kupirira ndi kuyamikira zinthu zabwino zimene ali nazo m’malo momangoganizira zomwe zawachitikira.

ZIMENE MUNGACHITE: Tsiku lililonse muzilemba kapena kuganizira zinthu zabwino zimene zakuchitikirani. Ndipo sizifunikira kuti zichite kukhala zinthu zikuluzikulu. Zikhoza kukhala zinthu zazing’ono ngati kutuluka kwa dzuwa, mmene mwachezera ndi munthu wina kapena chifukwa choti mwadzukanso ndi moyo. Zinthu zimenezi zingakuthandizeni kukhala wosangalala ngati mutamaziganizira komanso kuziyamikira.

Zimakhalanso zothandiza kwambiri mukamaganizira komanso kuyamikira kuti muli ndi banja komanso anzanu abwino. Anthu ena akachita zabwino kapena akasonyeza khalidwe linalake limene lakuchititsani chidwi, mungachite bwino kuwauza mmene mukumvera kaya powalembera kalata, imelo kapena meseji. Zimenezi zingathandize kuti muzigwirizana nawo kwambiri ndipo inuyo mungamasangalale chifukwa chokhala wopatsa.​—Machitidwe 20:35.

MFUNDO ZINA ZA M’BAIBULO

Mayi akumvetsera Baibulo longomvetsera pamene akupinda zovala za mwana wake

Mukhoza kupanga dawunilodi Baibulo longomvetsera. Baibuloli likupezeka m’zinenero 40 pa jw.org

MKANGANO UKABUKA MUZICHOKAPO.

“Chiyambi cha mkangano chili ngati kuboola damu kuti madzi atulukemo. Choncho mkangano usanabuke, chokapo.”​—MIYAMBO 17:14.

MUSAMANGOKHALIRA KUDERA NKHAWA ZAM’TSOGOLO.

“Musamade nkhawa za tsiku lotsatira, chifukwa tsiku lotsatira lidzakhala ndi zodetsa nkhawa zakenso. Zoipa za tsiku lililonse n’zokwanira pa tsikulo.”​—MATEYU 6:34.

MUZIGANIZA KAYE M’MALO MONGOCHITA ZINTHU CHIFUKWA CHA MMENE MUKUMVERA.

“Kuganiza bwino kudzakuyang’anira, ndipo kuzindikira kudzakuteteza.”​—MIYAMBO 2:11.

    Mabuku a Chichewa (1974-2025)
    Tulukani
    Lowani
    • Chichewa
    • Tumizirani Ena
    • Zimene Mumakonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenera Kutsatira
    • Nkhani Yosunga Chinsinsi
    • Privacy Settings
    • JW.ORG
    • Lowani
    Tumizirani Ena