UTHENGA WABWINO WOLEMBEDWA NDI YOHANE
1 Paciyambi panali Mawu. Mawuyo anali ndi Mulungu, ndipo Mawuyo anali mulungu.* 2 Ameneyo paciyambi anali ndi Mulungu. 3 Zinthu zonse zinakhalako kudzela mwa iye, ndipo palibe ngakhale cinthu cimodzi cinakhalako popanda iye.
4 Moyo unakhalako kupyolela mwa iye, ndipo moyo wa iyeyo unali kuwala kounikila anthu. 5 Kuwalako kukuunika mumdima, koma mdimawo sunagonjetse kuwalako.
6 Ndiyeno kunabwela munthu wina wotumidwa ndi Mulungu, dzina lake Yohane. 7 Munthu ameneyo anabwela monga mboni, kudzacitila umboni za kuwalako n’colinga cakuti anthu a mtundu uliwonse akhulupilile kudzela mwa iye. 8 Iyeyo sanali kuwalako ayi, koma anatumidwa kudzacitila umboni za kuwalako.
9 Kuwala kwenikweni kumene kumaunikila anthu a mtundu uliwonse kunali kutatsala pang’ono kubwela m’dziko. 10 Iye anali m’dziko, ndipo dziko linakhalako kupitila mwa iye, koma dzikolo silinamudziwe. 11 Iyeyo anabwela kwawo, koma anthu akwawo sanamulandile. 12 Komabe onse amene anamulandila, anawapatsa mphamvu kuti akhale ana a Mulungu, cifukwa anakhulupilila m’dzina lake. 13 Amenewa anabadwa kucokela kwa Mulungu, osati kucokela kwa anthu* kapena mwa kufuna kwa anthu,* osatinso mwa kufuna kwa munthu.
14 Conco Mawuyo anakhala munthu, ndipo anali kukhala pakati pathu. Tinaona ulemelelo wake, ulemelelo wofanana ndi umene mwana wobadwa yekha amalandila kucokela kwa atate ake. Iye nthawi zonse anali kuyanjidwa ndi Mulungu,* ndiponso anali kuphunzitsa coonadi. 15 (Yohane anacitila umboni za iye, inde anali kufuula kuti: “Uyu ndi amene ndinali kukamba za iye kuti, ‘Amene akubwela m’mbuyo mwanga ndi wamkulu kuposa ine, cifukwa iye anakhalako ine ndisanabadwe.’”) 16 Cifukwa cakuti anali ndi cisomo cacikulu, nthawi zonse tinali kulandila cisomo cacikulu cosefukila. 17 Popeza Cilamulo cinabwela kupitila mwa Mose, cisomo ndi coonadi zinabwela kupitila mwa Yesu Khristu. 18 Palibe munthu anaonapo Mulungu cikhalile, mulungu wobadwa yekha amene ali kumbali ya Atate,* ndi amene anafotokoza za Mulungu.
19 Yohane anapeleka umboni pamene Ayuda anatumiza ansembe ndi Alevi kucokela ku Yerusalemu kuti akamufunse kuti: “Kodi ndiwe ndani?” 20 Iye anawayankha mosapita m’mbali, ndipo anakana kuti: “Sindine Khristu.” 21 Kenako iwo anamufunsa kuti: “Ndiye ndiwe ndani? Kodi ndiwe Eliya?” Iye anayankha kuti: “Ayi.” “Kodi ndiwe Mneneli?” Iye anayankhanso kuti: “Ayi!” 22 Conco iwo anamufunsa kuti: “Nanga ndiwe ndani? Tiuze kuti tikawayankhe amene atituma. Kodi iweyo mwiniwake umati ndiwe ndani?” 23 Iye anati: “Ndine mawu a winawake amene akufuula m’cipululu kuti, ‘Wongolani njila ya Yehova,’ monga anakambila mneneli Yesaya.” 24 Anthuwo anatumidwa ndi Afarisi. 25 Conco iwo anamufunsa kuti: “Ngati si ndiwe Khristu, kapena Eliya, kapenanso Mneneli, n’cifukwa ciyani umabatiza anthu?” 26 Yohane anawayankha kuti: “Ine ndimabatiza anthu m’madzi. Koma pali wina waimilila pakati panu, amene inu simum’dziwa. 27 Iye akubwela m’mbuyo mwanga, ndipo ine sindine woyenela kumasula nthambo za nsapato zake.” 28 Zinthu zimenezi zinacitikila ku Betaniya kutsidya la Yorodano, kumene Yohane anali kubatiza anthu.
29 Tsiku lotsatila, Yohane anaona Yesu akubwela kwa iye, ndipo anati: “Taonani, Mwanawankhosa wa Mulungu amene akucotsa ucimo wa dziko! 30 Uyu ndi uja amene ndinali kukamba kuti: ‘Amene akubwela m’mbuyo mwanga ndi wamkulu kuposa ine, cifukwa iye anakhalako ine ndisanabadwe.’ 31 Ngakhale ine sindinali kumudziwa, koma cifukwa cimene ndikubatizila anthu m’madzi n’cakuti iye adziwike kwa Isiraeli.” 32 Yohane anacitilanso umboni kuti: “Ndinaona mzimu ukutsika ngati nkhunda kucokela kumwamba, ndipo unakhazikika pa iye. 33 Ngakhale ine sindinali kumudziwa, koma amene ananditumayo kuti ndidzabatize anthu m’madzi, anandiuza kuti: ‘Aliyense amene udzaona kuti mzimu watsikila pa iye n’kukhazikika, ameneyo ndiye amabatiza ndi mzimu woyela.’ 34 Ine ndinauona, ndipo ndikucitila umboni kuti ameneyu ndi Mwana wa Mulungu.”
35 Kenako tsiku lotsatila, Yohane anaimilila pamodzi ndi awili mwa ophunzila ake. 36 Ndipo iye ataona Yesu akuyenda, anati: “Onani, Mwanawankhosa wa Mulungu!” 37 Ophunzila awiliwo atamva kuti wakamba zimenezi, anatsatila Yesu. 38 Ndiyeno Yesu ataceuka n’kuona kuti akumulondola, anawafunsa kuti: “Mukufuna ciyani?” Iwo anamuyankha kuti: “Rabi (liwuli likamasulidwa, limatanthauza, “Mphunzitsi”), mukhala kuti?” 39 Iye anawauza kuti: “Tiyeni mukaoneko.” Conco iwo anapita kukaona kumene iye anali kukhala, ndipo anakhala naye tsiku limenelo, apo nthawi inali itatsala pang’ono kukwana 4 koloko madzulo.* 40 Andireya, m’bale wake wa Simoni Petulo, anali mmodzi wa ophunzila awili aja omwe anamva zimene Yohane ananena n’kutsatila Yesu. 41 Iye coyamba anapita kukafunafuna m’bale wake Simoni n’kumuuza kuti: “Ife tapeza Mesiya” (dzinali likamasulidwa, limatanthauza “Khristu”), 42 ndipo anapita naye kwa Yesu. Yesu atamuona, anamuuza kuti: “Iwe ndiwe Simoni, mwana wa Yohane. Kuyambila lelo, uzichedwa Kefa” (dzinali kumasulila kwake ndi “Petulo”).
43 Tsiku lotsatila, Yesu anafuna kupita ku Galileya. Ndiyeno anakumana ndi Filipo n’kumuuza kuti: “Khala wotsatila wanga.” 44 Filipo anali wocokela ku Betsaida, mzinda umene kunacokela Andireya ndi Petulo. 45 Filipo anapeza Nataniyeli n’kumuuza kuti: “Ife tapeza Yesu mwana wa Yosefe, wa ku Nazareti, amene Mose analemba za iye m’Cilamulo. Aneneli nawonso analemba za iye.” 46 Koma Nataniyeli anamufunsa kuti: “Kodi mu Nazareti mungatuluke munthu aliyense wabwino?” Filipo anamuuza kuti: “Tiye ukaone.” 47 Yesu ataona Nataniyeli akubwela kwa iye, anati: “Onani, Mwisiraeli ndithu, amene mwa iye mulibe cinyengo.” 48 Nataniyeli anamufunsa kuti: “Mwandidziwa bwanji?” Yesu anamuyankha kuti: “Filipo asanakuitane, ndinakuona uli munsi mwa mtengo wamkuyu.” 49 Nataniyeli anakamba kuti: “Mphunzitsi,* inu ndinudi Mwana wa Mulungu, komanso ndinu Mfumu ya Isiraeli.” 50 Yesu anamuyankha kuti: “Kodi wakhulupilila cifukwa ndakuuza kuti ndinakuona uli munsi mwa mtengo wamkuyu? Udzaona zinthu zazikulu kuposa izi.” 51 Kenako anamuuza kuti: “Ndithu ndikukuuzani anthu inu, mudzaona kumwamba kutatseguka, ndipo mudzaona angelo a Mulungu akukwela ndi kutsika kupita kumene kuli Mwana wa munthu.”
2 Pa tsiku lacitatu, ku Kana wa ku Galileya kunali phwando la ukwati, ndipo amayi ake a Yesu analinso kumeneko. 2 Yesu ndi ophunzila ake nawonso anaitanidwa ku phwando la ukwati limenelo.
3 Vinyo atatsala pang’ono kutha, amayi ake a Yesu anauza Yesuyo kuti: “Vinyo waathela.” 4 Koma Yesu anauza mayi akewo kuti: “Mayi, ife zikutikhudza bwanji?* Nthawi yanga sinafike.” 5 Amayi ake anauza amene anali kutumikila kuti: “Mucite zilizonse zimene angakuuzeni.” 6 Tsopano pamalopo panali mbiya zamiyala 6 mogwilizana ndi malamulo a Ayuda a kudziyeletsa. Mbiya iliyonse inali kukwana malita pafupifupi 44 mpaka 66. 7 Yesu anawauza kuti: “Dzazani mbiyazi ndi madzi.” Iwo anadzaza mbiyazo mpaka pakamwa. 8 Kenako iye anawauza kuti: “Tapam’moni mupeleke kwa woyang’anila phwandoli.” Ndipo iwo anapelekadi. 9 Woyang’anila phwando uja analawa madzi amene anasandutsidwa vinyo. Iye sanadziwe kumene vinyoyo anacokela (ngakhale kuti otumikila omwe anatapa madziwo anadziwa). Conco woyang’anila phwandoyo anaitana mkwati 10 n’kumuuza kuti: “Munthu aliyense amatulutsa vinyo wabwino coyamba, ndipo anthu akaledzela m’pamene amatulutsa vinyo amene si wabwino kwenikweni. Koma iwe wasunga vinyo wabwino mpaka pano.” 11 Yesu anacita zimenezi ku Kana wa ku Galileya monga ciyambi ca zozizwitsa zake.* Iye anacititsa kuti ulemelelo wake uonekele, ndipo ophunzila ake anayamba kumukhulupilila.
12 Pambuyo pa izi, Yesu, amayi ake, abale ake, pamodzi ndi ophunzila ake, anapita ku Kaperenao, koma sanakhaleko masiku ambili.
13 Tsopano Pasika wa Ayuda atayandikila, Yesu anapita ku Yerusalemu. 14 Kumeneko anapeza kuti m’kacisi muli ogulitsa ng’ombe, nkhosa, nkhunda, komanso osintha ndalama, atakhalakhala m’mipando yawo. 15 Conco Yesu anapanga mkwapulo wazingwe, ndi kuwathamangitsila panja pa kacisi onse ogulitsa nkhosa ndi ng’ombe. Kenako anakhuthula makobili a osintha ndalama n’kugudubula matebulo awo. 16 Ndiyeno anauza amene anali kugulitsa nkhundawo kuti: “Zicotseni muno izi! Mulekeletu kusandutsa nyumba ya Atate wanga kukhala nyumba yamalonda!”* 17 Ophunzila ake anakumbukila zimene Malemba amanena kuti: “Cangu canga pa nyumba yanu cidzayaka ngati moto mumtima mwanga.”
18 Koma Ayudawo anamuuza kuti: “Kodi ungationetse cizindikilo cotani coonetsa kuti uli ndi ulamulilo wocita zimenezi?” 19 Yesu anawayankha kuti: “Gwetsani kacisi uyu, ndipo ndidzamumanganso m’masiku atatu.” 20 Kenako Ayudawo anakamba kuti: “Panatenga zaka 46 kuti kacisiyu amangidwe, ndiye iwe ukuti udzamumanga m’masiku atatu cabe?” 21 Koma iye ponena za kacisi anali kutanthauza thupi lake. 22 Conco, iye ataukitsidwa kwa akufa, ophunzila ake anakumbukila kuti anali kukonda kunena zimenezi, ndipo anakhulupilila Malemba komanso mawu amene Yesu anakamba.
23 Ndiyeno pamene iye anali ku Yerusalemu pacikondwelelo ca Pasika, anthu ambili anamukhulupilila* ataona zozizwitsa* zimene anali kucita. 24 Koma Yesu sanawadalile kwenikweni, cifukwa anali kuwadziwa bwino onsewo, 25 ndipo iye sanafunikile wina kucita kumuuza za anthu, cifukwa anali kudziwa za mumtima mwa anthu.
3 Panali Mfarisi wina dzina lake Nikodemo, wolamulila wa Ayuda. 2 Munthu ameneyu anapita kwa Yesu usiku n’kumuuza kuti: “Rabi,* tikudziwa kuti ndinu mphunzitsi wocokela kwa Mulungu, cifukwa palibe munthu angakwanitse kucita zizindikilo zimene mumacita ngati Mulungu sali naye.” 3 Yesu anamuyankha kuti: “Ndithudi ndikukuuza, ngati munthu sanabadwenso,* n’zosatheka kuona Ufumu wa Mulungu.” 4 Nikodemo anamufunsa kuti: “Kodi munthu angabadwe bwanji ngati ndi wamkulu kale? Iye sangalowe m’mimba mwa mayi ake kaciwili n’kubadwanso, angatelo kodi?” 5 Yesu anayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuza, ngati munthu sanabadwe mwa madzi ndi mzimu n’zosatheka iye kulowa mu Ufumu wa Mulungu. 6 Wobadwa kwa munthu ndi munthu, ndipo cobadwa ku mzimu ndi mzimu. 7 Usadabwe cifukwa ndakuuza kuti: Anthu inu muyenela kubadwanso. 8 Mphepo imakunthila kumene ikufuna, ndipo inu mumangomvako mkokomo wake, koma simumadziwa kumene yacokela ndi kumene ikupita. Ndi mmenenso zimakhalila kwa aliyense amene wabadwa mu mzimu.”
9 Nikodemo poyankha anati: “Kodi zimenezi zingatheke bwanji?” 10 Yesu anamufunsa kuti: “Kodi sikuti ndiwe mphunzitsi mu Isiraeli, ndiye zitheka bwanji kuti sudziwa zinthu zimenezi? 11 Ndithudi ndikukuuza, zimene tidziwa timazikamba, ndipo zimene taona timazicitila umboni. Koma inu simulandila umboni umene timakupatsani. 12 Ngati ndakuuzani zinthu za padziko lapansi koma simukhulupililabe, mungakhulupilile bwanji ndikakuuzani zinthu zakumwamba? 13 Ndiponso palibe munthu amene anakwelapo kumwamba koma Mwana wa munthu yekha, amene anatsika kucokela kumwambako. 14 Monga mmene Mose anakwezela njoka m’mwamba m’cipululu, nayenso Mwana wa munthu ayenela kukwezedwa m’mwamba, 15 kuti aliyense wokhulupilila iye akapeze moyo wosatha.
16 “Pakuti Mulungu analikonda kwambili dziko, moti anapeleka Mwana wake wobadwa yekha, kuti aliyense womukhulupilila asawonongeke, koma akapeze moyo wosatha. 17 Mulungu sanatumize Mwana wake m’dziko kuti adzaliweluze koma kuti dzikolo lipulumutsidwe kupitila mwa iye. 18 Munthu aliyense wokhulupilila mwa iye sayenela kuweluzidwa. Munthu aliyense wosamukhulupilila waweluzidwa kale, cifukwa sanakhulupilile* Mwana wobadwa yekha wa Mulungu. 19 Tsopano maziko a ciweluzo ndi awa: kuwala kwabwela m’dziko, koma anthu akonda mdima m’malo mwa kuwala, cifukwa ca nchito zawo zoipa. 20 Pakuti aliyense wocita zinthu zoipa amadana ndi kuwala, ndipo sabwela pomwe pali kuwala kuti nchito zake zisaonekele poyela.* 21 Koma amene amacita zabwino, amabwela pamene pali kuwala, kuti nchito zake zionekele kuti anazicita mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.”
22 Zitatha izi, Yesu ndi ophunzila ake anapita kumadela akumidzi a ku Yudeya. Kumeneko anakhala nawo kwa kanthawi ndipo anali kubatiza anthu. 23 Koma nayenso Yohane anali kubatiza anthu ku Ainoni pafupi ndi Salimu, cifukwa kunali madzi ambili, ndipo anthu anali kupita kumeneko kukabatizidwa. 24 Pa nthawiyi n’kuti Yohane anali asanaponyedwe m’ndende.
25 Tsopano ophunzila a Yohane anakangana ndi Myuda wina pa nkhani ya kukhala woyela pamaso pa Mulungu. 26 Conco iwo anapita kwa Yohane n’kumuuza kuti: “Mphunzitsi,* munthu amene munali naye kutsidya la Yorodano, amenenso munamucitila umboni, onani, akubatiza anthu, ndipo onse akupita kwa iye.” 27 Yohane anayankha kuti: “Munthu sangalandile kanthu kalikonse ngati sanapatsidwe kucokela kumwamba. 28 Inuyo mungandicitile umboni kuti ndinati, ‘Ine sindine Khristu, koma ndinatumidwa kuti ndikhale kalambulabwalo wake.’ 29 Mwiniwake wa mkwatibwi ndi mkwati. Koma mnzake wa mkwati akaimilila n’kumva mawu a mkwatiyo, amakondwela kwambili. Conco ine ndine wokondwa kwambili. 30 Ameneyo ayenela kupitiliza kuwonjezeka, koma ine ndiyenela kumacepelacepela.”
31 Amene wacokela kumwamba amaposa ena onse. Amene wacokela pa dziko lapansi ndi wa padziko lapansi, ndipo amakamba zinthu za padziko lapansi. Amene wacokela kumwamba amaposa ena onse. 32 Iye amacitila umboni zimene waona ndi kumva, koma palibe munthu amene amakhulupilila umboni wake. 33 Aliyense amene wakhulupilila umboni wake, wauika cidindo* umboniwo kuti Mulungu ndi woona. 34 Pakuti amene Mulungu anamutuma, amanena mawu a Mulungu, cifukwa Iye sapeleka mzimu moumila.* 35 Atate amakonda Mwana, ndipo anapeleka zinthu zonse m’manja mwake. 36 Amene amakhulupilila Mwanayo adzapeza moyo wosatha. Amene samvela Mwanayo sadzauona moyowo, koma mkwiyo wa Mulungu udzakhalabe pa iye.
4 Ambuye atazindikila kuti Afarisi anamva zakuti iyeyo* akupanga ophunzila ambili ndi kuwabatiza kuposa Yohane, 2 ngakhale kuti si Yesu amene anali kuwabatiza koma ophunzila ake, 3 anacoka ku Yudeya n’kupitanso ku Galileya. 4 Koma anafunika kudzela ku Samariya. 5 Conco, anafika mu mzinda wa Samariya wochedwa Sukari, kufupi ndi munda umene Yakobo anapatsa Yosefe mwana wake. 6 Ndipo kumeneko kunali citsime ca Yakobo. Popeza Yesu anali atalema ndi ulendo, anakhala pansi pacitsimepo.* Apo nthawi ili ca m’ma 12 koloko masana.*
7 Mayi wina wa ku Samariya anabwela kudzatapa madzi. Yesu anapempha mayiyo kuti: “Ndipatsen’koni madzi akumwa.” 8 (Ophunzila ake anali atalowa mumzinda kukagula cakudya.) 9 Conco mayi wacisamariyayo anamufunsa kuti: “Popeza inu ndinu Myuda, n’cifukwa ciyani mukundipempha madzi, ine mayi wacisamariya?” (Cifukwa Ayuda ndi Asamariya sagwilizana.) 10 Yesu anayankha mayiyo kuti: “Mukanadziwa mphatso yaulele ya Mulungu komanso amene akukupemphani kuti, ‘Ndipatsen’koni madzi akumwa,’ mukanamupempha madzi amoyo ndipo akanakupatsani.” 11 Mayiyo anamuyankha kuti: “Bambo, mulibe n’cotapila madzi, ndipo citsimeci n’cozama. Ndiye madzi a moyowo muwatenga kuti? 12 Kodi inu ndinu wamkulu kuposa Yakobo atate wathu, amene anatipatsa citsimeci, cimene iye, ana ake, komanso ng’ombe zake anali kumwapo?” 13 Yesu anamuyankha kuti: “Aliyense wakumwa madzi awa adzamvanso ludzu. 14 Koma aliyense amene adzamwe madzi amene ndidzam’patse sadzamvanso ludzu ngakhale pang’ono. Madzi amene ndidzamupatsewo, mwa iye adzakhala kasupe wotulutsa madzi opatsa moyo wosatha.” 15 Mayiyo anamuuza kuti: “Bambo, ndipatsen’koni madziwo kuti ndisadzamvenso ludzu, ndipo ndisadzabwelenso kuno kudzatapa madzi.”
16 Yesu anauza mayiyo kuti: “Pitani, mukaitane mwamuna wanu kuti abwele kuno.” 17 Mayiyo anayankha kuti: “Ndilibe mwamuna.” Yesu anamuuza kuti: “Mwakamba zoona kuti, ‘Ndilibe mwamuna.’ 18 Cifukwa mwakwatiwapo ndi amuna asanu, ndipo mwamuna amene muli naye pali pano si wanu. Zimene mwakambazi n’zoona.” 19 Mayiyo anati kwa iye: “Bambo, ndadziwa kuti ndinu mneneli. 20 Makolo athu anali kulambilila m’phili ili, koma anthu inu mumakamba kuti ku Yerusalemu n’kumene anthu ayenela kulambilila.” 21 Yesu anauza mayiyo kuti: “Mayi ndikhulupilileni, nthawi idzafika pamene inu simudzalambila Atate m’phili ili kapena ku Yerusalemu. 22 Inu mumalambila cimene simudziwa, koma ife timalambila cimene tidziwa, cifukwa cipulumutso cikuyambila kwa Ayuda. 23 Komabe nthawi ikubwela, ndipo ndi yomwe ino, pamene olambila oona adzalambila Atate motsogoleledwa ndi mzimu komanso coonadi. Pakuti Atate akufunafuna anthu ngati amenewa kuti azimulambila. 24 Mulungu ndi Mzimu, ndipo amene amamulambila ayenela kumulambila motsogoleledwa ndi mzimu komanso coonadi.” 25 Mayiyo anamuuza kuti: “Ndidziwa kuti Mesiya wochedwanso Khristu akubwela. Iyeyo akadzafika adzatifotokozela zinthu zonse poyela.” 26 Yesu anamuuza kuti: “Ndine amene, ineyo amene ndikulankhula nanu.”
27 Nthawi yomweyo ophunzila ake anafika, ndipo anadabwa kuona kuti iye akulankhula ndi mzimayi. Ngakhale n’telo, palibe amene anamufunsa kuti: “Mufunanji kwa iye?” kapena “N’cifukwa ciyani mukukamba ndi mayiyu?” 28 Conco mayiyo anasiya mtsuko wake wa madzi n’kupita mumzinda kukauza anthu kuti: 29 “Tiyeni mukaone munthu amene wandiuza zonse zimene ndinacita. Kodi ameneyu sangakhale Khristu uja?” 30 Iwo anacoka mu mzindawo n’kupita kumene kunali Yesu.
31 Pa nthawiyi ophunzila ake anali kumupempha kuti: “Mphunzitsi,* idyani.” 32 Koma iye anawauza kuti: “Ndili naco cakudya cimene inu simucidziwa.” 33 Conco ophunzilawo anayamba kufunsana kuti: “Palibe aliyense amene wamubweletsela cakudya, alipo ngati?” 34 Yesu anawauza kuti: “Cakudya canga ndi kucita cifunilo ca amene anandituma, ndi kutsiliza nchito yake. 35 Kodi inu simukuti kwatsala miyezi inayi kuti nthawi yokolola ifike? Taonani! Ndikukuuzani kuti: Kwezani maso anu ndi kuona m’mindamo, mbewu zaca* kale kuti zikololedwe. Moti apa 36 wokolola akulandila malipilo, ndipo akusonkhanitsa zipatso ku moyo wosatha, kuti wofesa mbewu ndi wokololayo asangalalile pamodzi. 37 Ndiye cifukwa cake mawu awa ndi oona akuti: Wina ndi wofesa, ndipo wina ndi wokolola. 38 Ine ndinakutumani kuti mukakolole zimene simunagwililepo nchito. Ena anagwila nchito molimbika, ndipo inu mukupindulilapo pa nchito yawo.”
39 Asamariya ambili a mumzindawo anaika cikhulupililo mwa iye cifukwa ca mawu amene mayi uja anacitila umboni akuti: “Wandiuza zonse zimene ndinacita.” 40 Conco pamene Asamariya anafika kwa iye, anamupempha kuti akhale nawo, ndipo iye anakhala kumeneko masiku awili. 41 Zotsatilapo zake zinali zakuti, anthu ena ambili anakhulupilila cifukwa ca zimene iye ananena. 42 Conco anthuwo anauza mayiyo kuti: “Apa sikuti takhulupilila cabe cifukwa ca zimene iwe watiuza ayi, koma cifukwa tadzionela tokha, ndipo tadziwa kuti munthu ameneyu ndi mpulumutsidi wa dziko.”
43 Pambuyo pa masiku awiliwo, iye anacoka kumeneko n’kupita ku Galileya. 44 Yesu mwiniwakeyo anacitila umboni kuti mneneli salemekezedwa kwawo. 45 Conco iye atapita ku Galileya, Agalileya anamulandila, cifukwa anaona zinthu zonse zimene anacita pacikondwelelo ku Yerusalemu, popeza kuti nawonso anapita ku cikondweleloco.
46 Kenako anabwelelanso ku Kana wa ku Galileya, kuja kumene anasandutsa madzi kukhala vinyo. Kumeneko kunali munthu wina wotumikila mfumu, amene mwana wake wamwamuna anali kudwala ku Kaperenao. 47 Munthu ameneyo atamva kuti Yesu wacoka ku Yudeya ndipo wafika ku Galileya, anapita kwa iye n’kumupempha kuti abwele kudzacilitsa mwana wakeyo, pakuti anali atatsala pang’ono kufa. 48 Koma Yesu anamuuza kuti: “Popanda kuona zizindikilo ndi zodabwitsa, anthu inu simungakhulupilile.” 49 Mtumiki wa mfumuyo anamuuza kuti: “Ambuye, tiyeni mwana wanga asanamwalile.” 50 Yesu anamuuza kuti, “Pita, mwana wako ali moyo.” Munthuyo anakhulupilila mawu amene Yesu anamuuza, moti anapitadi. 51 Koma ali m’njila, akapolo ake anakumana naye kudzamuuza kuti mwana wake wamwamuna uja ali moyo.* 52 Conco iye anawafunsa ola limene mwanayo anacila. Iwo anamuyankha kuti: “Malungo* ake anatha dzulo ca m’ma 1 koloko masana.”* 53 Ndiyeno tateyo anadziwa kuti mwana wake anacila mu ola lomwe lija limene Yesu anamuuza kuti: “Mwana wako ali moyo.” Conco iye pamodzi ndi banja lake lonse anakhulupilila. 54 Ici cinali cizindikilo caciwili cimene Yesu anacita atacoka ku Yudeya n’kupita ku Galileya.
5 Pambuyo pa izi, kunali cikondwelelo ca Ayuda, ndipo Yesu anapita ku Yerusalemu. 2 Ku Yerusalemuko, pa Geti ya Nkhosa panali dziwe limene m’Ciheberi limachedwa Betesida. Dziwelo linali ndi makonde asanu okhala ndi zipilala. 3 Anthu ambili odwala, akhungu, olemala, komanso opuwala* manja ndi miyendo anali kugona mmenemo. 4* —— 5 Kumeneko kunali munthu wina amene anali wodwala kwa zaka 38. 6 Yesu ataona munthu ameneyu ali cigonele, komanso atadziwa kuti wakhala wodwala kwa nthawi yaitali, anamufunsa kuti: “Kodi ufuna kucila?” 7 Munthu wodwalayo anamuyankha kuti: “Bambo, ndilibe munthu aliyense woti andiike m’dziweli madzi akawinduka. Ndipo ndikafuna kulowamo wina amandipitilila n’kulowamo.” 8 Yesu anamuuza kuti: “Nyamuka! Nyamula macila* akowa uyambe kuyenda.” 9 Nthawi yomweyo munthuyo anacila, ndipo ananyamula macila* ake n’kuyamba kuyenda.
Tsiku limenelo linali la Sabata. 10 Ndiye Ayudawo anayamba kuuza munthu amene anacilitsidwayo kuti: “Lelo ndi Sabata, conco sikololeka kuti unyamule macila akowo.”* 11 Koma iye anawayankha kuti: “Munthu amene wandicilitsayo ndi yemwe wandiuza kuti, ‘Nyamula macila* akowa uyambe kuyenda.’” 12 Iwo anamufunsa kuti: “Kodi ndani wakuuza kuti, ‘Nyamula macila akowa uyambe kuyenda’?” 13 Koma munthu wocilitsidwayo sanadziwe kuti anali ndani, cifukwa Yesu anali atalowa m’khamu la anthu limene linali pamenepo.
14 Pambuyo pake, Yesu anapeza munthuyo m’kacisi ndipo anamuuza kuti: “Onatu, wacila tsopano. Usakacimwenso, kuti cinthu coipa kwambili cisakakucitikile.” 15 Munthuyo anapita n’kukauza Ayuda aja kuti ndi Yesu amene wamucilitsa. 16 Pa cifukwa cimeneci, Ayuda anayamba kumuvutitsa Yesu, cifukwa anali kucita zinthu zimenezi pa Sabata. 17 Koma iye anawauza kuti: “Atate wanga akugwilabe nchito mpaka pano, inenso ndikugwilabe nchito.” 18 Mwa ici, Ayudawo anayamba kufunafuna njila yoti amuphele, cifukwa kuwonjezela pa kuphwanya Sabata, iye anali kukambanso kuti Mulungu ndi Atate wake, kudzipanga wofanana ndi Mulungu.
19 Conco Yesu poyankha anawauza kuti: “Ndithu ndikukuuzani, Mwana sangacite ciliconse congoganiza pa iye yekha, koma zokhazo zimene waona Atate wake akucita. Cifukwa zilizonse zimene Atate amacita, Mwananso amacita zomwezo, mmene Atate wake amazicitila. 20 Pakuti Atate amamukonda Mwanayo, ndipo amamuonetsa zinthu zonse zimene iwo amacita. Iwo adzamuonetsa nchito zazikulu kuposa izi kuti inu mudabwe nazo. 21 Monga mmene Atate amaukitsila akufa n’kuwapatsa moyo, nayenso Mwana amapeleka moyo kwa amene wafuna kumupatsa. 22 Pakuti Atate saweluza munthu aliyense, koma udindo wonse woweluza aupeleka kwa Mwana, 23 kuti onse azilemekeza Mwanayo monga mmene amalemekezela Atate. Munthu aliyense amene salemekeza Mwanayo, salemekezanso Atate amene anamutuma. 24 Ndithu ndikukuuzani, munthu aliyense amene wamva mawu anga ndi kukhulupilila Atate amene anandituma, adzapeza moyo wosatha. Ndipo iye sadzaweluzidwa, koma wacoka ku imfa n’kupita ku moyo.
25 “Ndithu ndikukuuzani, nthawi ikubwela ndipo ndi yomwe ino, pamene akufa adzamva mawu a Mwana wa Mulungu, ndipo amene akumvela adzakhala ndi moyo. 26 Monga mmene Atate alili ndi moyo mwa iwo eni,* alolanso Mwana kuti akhale ndi moyo mwa iye mwini. 27 Ndipo amupatsanso mphamvu zoweluza, cifukwa iye ndi Mwana wa munthu. 28 Musadabwe nazo zinthu zimenezi, cifukwa nthawi ikubwela pamene onse ali m’manda acikumbutso adzamva mawu ake 29 ndipo adzatuluka. Amene anali kucita zabwino adzauka kuti alandile moyo, koma amene anali kucita zoipa adzauka kuti aweluzidwe. 30 Sindingacite ciliconse congoganiza pa ine ndekha. Ndimaweluza mogwilizana ndi zimene ndamva, ndipo ciweluzo canga ndi colungama cifukwa ndimacita cifunilo ca amene anandituma, osati canga.
31 “Ngati ndikudzicitila ndekha umboni, ndiye kuti umboni wangawo si woona. 32 Pali wina amene amacitila umboni za ine, ndipo ndidziwa kuti umboni wokhudza ine umene amapelekawo ndi woona. 33 Munatumiza anthu kwa Yohane, ndipo iye wacitila umboni coonadi. 34 Komabe, ine sindivomeleza umboni wocokela kwa munthu, koma ndikukamba zimenezi kuti mupulumuke. 35 Munthuyo anali nyale yoyaka komanso younikila, ndipo kwa kanthawi kocepa munali ofunitsitsa kukondwela kwambili cifukwa ca kuwala kwakeko. 36 Koma ine ndili ndi umboni waukulu kuposa wa Yohane, cifukwa nchito zimene Atate wanga anandipatsa kuti ndizikwanilitse, nchitozo n’zimene ndikucita, ndipo zikucitila umboni kuti Atate ananditumadi. 37 Komanso Atate amene anandituma iwo eni akundicitila umboni. Inu simunamvepo mawu ake ndi kale lonse, kapenanso kumuona. 38 Mawu a Mulungu sanakhazikike mwa inu, cifukwa simunakhulupilile mthenga amene iye anatumiza.
39 “Mumafufuza Malemba cifukwa muganiza kuti mudzapeza moyo wosatha kudzela m’Malembawo, ndipo Malemba omwewo amacitilanso umboni za ine. 40 Koma inu simufuna kubwela kwa ine kuti mukapeze moyo. 41 Sindikufuna kulandila ulemelelo wocokela kwa anthu, 42 koma ndidziwa bwino kuti mwa inu mulibe cikondi ca Mulungu. 43 Ine ndabwela m’dzina la Atate wanga, koma simukundilandila. Munthu wina akanabwela m’dzina lake mukanamulandila. 44 Kodi mungakhulupilile bwanji pamene mukupatsana ulemelelo wina ndi mnzake, koma simukuyesetsa kupeza ulemelelo wocokela kwa Mulungu yekhayo? 45 Musaganize kuti ndidzakunenezani kwa Atate, pali wina amene amakunenezani, iye ndi Mose, amene inu mumamudalila. 46 Mukanakhulupilila Mose, mukanakhulupililanso ine, cifukwa iye analembanso za ine. 47 Koma ngati simunakhulupilile zimene analemba, mungakhulupilile bwanji mawu anga?”
6 Pambuyo pa izi, Yesu anawoloka nyanja ya Galileya, kapena kuti nyanja ya Tiberiyo. 2 Ndipo khamu la anthu linali kumutsatila cifukwa linali kuona zozizwitsa* zimene anali kucita pocilitsa anthu. 3 Conco Yesu anakwela m’phili, ndipo anakhala pansi mmenemo pamodzi ndi ophunzila ake. 4 Tsopano cikondwelelo ca Ayuda ca Pasika cinali citayandikila. 5 Yesu atakweza maso ake, n’kuona khamu lalikulu la anthu likubwela kwa iye, anafunsa Filipo kuti: “N’kuti kumene tingakagule mkate kuti anthuwa adye?” 6 Koma iye ananena izi pofuna kumuyesa, cifukwa Yesu anali kudziwa zimene anafuna kucita. 7 Filipo anamuyankha kuti: “Ndalama zokwana madinari 200 sizingakwanile kugula mkate woti aliyense adyeko ngakhale pang’ono.” 8 Mmodzi wa ophunzila ake Andireya, m’bale wake wa Simoni Petulo, anamuuza kuti: 9 “Pano pali kamnyamata komwe kali ndi mitanda isanu ya mkate wabalele ndi tinsomba tiwili. Koma kodi zimenezi zingakwanile khamu lonseli?”
10 Yesu anakamba kuti: “Auzeni anthuwo akhale pansi.” Pamalopo panali udzu wambili. Conco amuna pafupifupi 5,000 anakhala pansi. 11 Yesu anatenga mkatewo n’kuyamika, kenako anaupeleka kwa anthu amene anakhala pansi aja. Iye anacitanso cimodzimodzi ndi tunsomba tuja moti anthuwo anadya mmene anafunila. 12 Anthuwo atadya n’kukhuta, iye anauza ophunzila ake kuti: “Sonkhanitsani zonse zotsala kuti pasawonongeke ciliconse.” 13 Conco iwo anazisonkhanitsa pamodzi ndipo zinadzala matadza 12. Izi ndi zimene zinatsalako pambuyo pakuti anthu aja adya mkate kucokela ku mitanda isanu ya balele n’kulephela kuitsiliza.
14 Anthuwo ataona cozizwitsa* cimene anacitaci anayamba kunena kuti: “Zoonadi uyu ndiye mneneli uja amene anati adzabwela padziko.” 15 Ndiyeno Yesu atadziwa kuti anthuwo akufuna kudzamugwila kuti amulonge ufumu, anacoka n’kupitanso ku phili kwayekha.
16 Ndiyeno kutayamba kuda, ophunzila ake anapita ku nyanja. 17 Iwo anakwela bwato n’kuwoloka nyanjayo kupita ku Kaperenao. Apa n’kuti kwadelatu, ndipo Yesu anali asanabwelebe kwa iwo. 18 Komanso nyanjayo inayamba kuwinduka cifukwa cimphepo camphamvu cinali kuwomba. 19 Iwo atapalasa makilomita asanu kapena 6,* anaona Yesu akuyenda pa nyanja akuyandikila bwatolo, ndipo iwo anacita mantha. 20 Koma iye anawauza kuti: “Ndine, musacite mantha!” 21 Ndiyeno iwo anamulola kukwela m’bwatolo, ndipo posapita nthawi bwatolo linafika kumtunda kumene anali kupita.
22 Tsiku lotsatila, khamu limene linali kutsidya lina la nyanja linazindikila kuti bwato lokhalo laling’ono limene linali m’mbali mwa nyanja palibenso. Ophunzila a Yesu anakwela bwatolo n’kupita popanda Yesu. 23 Koma mabwato amene anacokela ku Tiberiyo anafika pafupi ndi malo amene anthuwo anadyela mkate uja Ambuye atayamika. 24 Conco khamu la anthulo litaona kuti Yesu ndi ophunzila ake kulibe kumeneko, linakwela mabwato awo n’kupita ku Kaperenao kukafunafuna Yesu.
25 Atamupeza kutsidya lina la nyanja anamufunsa kuti: “Mphunzitsi,* mwafika nthawi yanji kuno?” 26 Yesu anawayankha kuti: “Ndithu ndikukuuzani, mukundifunafuna osati cifukwa ca zozizwitsa* zimene munaona, koma cifukwa ca mkate umene munadya ndi kukhuta. 27 Musamagwile nchito kuti mungopeza cakudya cimene cimawonongeka, koma kuti mupeze cakudya cokhalitsa, comwe cimabweletsa moyo wosatha, cimene Mwana wa munthu adzakupatsani. Pakuti Atate Mulungu mwiniyo waika cidindo pa Mwanayo comuvomeleza.”
28 Conco anthuwo anamufunsa kuti: “Kodi tiyenela kutani kuti tizicita zimene Mulungu amafuna?” 29 Yesu anawayankha kuti: “Mulungu amafuna kuti muzionetsa cikhulupililo mwa iye amene anamutuma.” 30 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Kodi mucita cozizwitsa* cotani kuti ticione ndi kukukhulupililani? Mucita nchito yotani? 31 Makolo athu akale, anadya mana m‘cipululu monga mmene Malemba amanenela kuti: ‘Iye anawapatsa cakudya cocokela kumwamba kuti adye.’” 32 Kenako Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Mose sanakupatseni cakudya cocokela kumwamba, koma Atate wanga amakupatsani cakudya ceniceni cocokela kumwamba. 33 Cifukwa cakudya cimene Mulungu wapeleka, ndi iye amene watsika kucokela kumwamba n’kupeleka moyo ku dzikoli.” 34 Conco iwo anamuuza kuti: “Ambuye muzitipatsa cakudya cimeneci nthawi zonse.”
35 Yesu anawauza kuti: “Ine ndine cakudya copatsa moyo. Aliyense wobwela kwa ine sadzamva njala ngakhale pang’ono, ndipo aliyense wokhulupilila mwa ine sadzamva ludzu ayi. 36 Koma monga ndinakuuzilani, inu simukhulupililabe ngakhale kuti mwandiona. 37 Onse amene Atate andipatsa adzabwela kwa ine, ndipo amene wabwela kwa ine sindidzamupitikitsa. 38 Pakuti ndinabwela kucokela kumwamba kudzacita cifunilo ca iye amene anandituma, osati canga ayi. 39 Cifunilo ca amene anandituma n’cakuti, ndisataye ngakhale mmodzi mwa onse amene iye anandipatsa, koma kuti ndikawaukitse pa tsiku lothela. 40 Pakuti cifunilo ca Atate wanga n’cakuti aliyense wovomeleza Mwanayo ndi kukhulupilila mwa iye akapeze moyo wosatha, ndipo ine ndidzamuukitsa pa tsiku lothela.”
41 Ndiyeno Ayudawo anayamba kung’ung’udza za iye cifukwa anakamba kuti: “Ine ndine cakudya cocokela kumwamba.” 42 Iwo anayamba kunena kuti: “Kodi uyu si Yesu mwana wa Yosefe, amene atate ake ndi amayi ake timawadziwa? Nanga bwanji tsopano akunena kuti, ‘Ndinacokela kumwamba’?” 43 Poyankha Yesu anawauza kuti: “Lekani kung’ung’udza pakati panu. 44 Palibe amene angabwele kwa ine ngati Atate amene anandituma sanamukopele* kwa ine, ndipo ine ndidzamuukitsa pa tsiku lothela. 45 Aneneli analemba kuti: ‘Onse adzaphunzitsidwa ndi Yehova.’ Aliyense amene wamvetsela kwa Atate ndipo waphunzila, amabwela kwa ine. 46 Palibe munthu amene anaonapo Atate, kupatulapo iye amene anacokela kwa Mulungu, ameneyu ndiye anaonapo Atate. 47 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wokhulupilila adzapeza moyo wosatha.
48 “Ine ndine cakudya copatsa moyo. 49 Makolo anu akale anadya mana m’cipululu koma anafabe. 50 Ici ndi cakudya cocokela kumwamba, coti aliyense adyeko ndipo asafe. 51 Ine ndine cakudya copatsa moyo cocokela kumwamba. Ngati wina angadye cakudyaci adzakhala ndi moyo kwamuyaya. Ndipo cakudya cimene ndidzapeleka, ndi mnofu wanga kuti anthu* akapeze moyo.”
52 Kenako Ayudawo anayamba kukangana akumati: “Kodi zingatheke bwanji munthu uyu kutipatsa mnofu wake kuti tidye?” 53 Conco Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, ngati simungadye mnofu wa Mwana wa munthu ndi kumwa magazi ake, simudzapeza moyo.* 54 Aliyense amene amadya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga adzapeza moyo wosatha, ndipo ndidzamuukitsa pa tsiku lothela. 55 Cifukwa mnofu wanga ndi cakudya ceniceni, ndipo magazi anga ndi cakumwa ceniceni. 56 Aliyense amene amadya mnofu wanga ndi kumwa magazi anga, amakhalabe wogwilizana ndi ine ndipo inenso ndimakhala wogwilizana naye. 57 Atate wamoyo anandituma ndipo ndili ndi moyo cifukwa ca Atatewo. Conco nayenso amene amadya mnofu wanga adzakhala ndi moyo cifukwa ca ine. 58 Ici ndi cakudya cocokela kumwamba. Sicili ngati cakudya cimene makolo anu akale anadya koma n’kufa ndithu. Aliyense wakudya cakudyaci adzakhala ndi moyo kwamuyaya.” 59 Iye anakamba zimenezi pamene anali kuphunzitsa m’sunagoge* ku Kaperenao.
60 Ambili mwa ophunzila ake atamva izi anati: “Mawu awa ndi okhumudwitsa. Ndani angafune kumvetsela zimenezi?” 61 Koma Yesu atadziwa kuti ophunzila ake anali kung’ung’udza cifukwa ca zimene iye anakamba, anawafunsa kuti: “Kodi izi zakupunthwitsani? 62 Nanga bwanji mukadzaona Mwana wa munthu akukwela kubwelela kumene anali poyamba? 63 Mzimu ndiwo umapatsa moyo koma mnofu ulibe nchito ngakhale pang’ono. Mawu amene ndakuuzani ndi mzimu ndiponso ndi moyo. 64 Koma pali ena a inu amene simukhulupilila.” Cifukwa Yesu anadziwa kucokela paciyambi amene sanamukhulupilile, komanso munthu amene adzamupeleka. 65 Iye anapitiliza kuti: “N’cifukwa cake ndinakuuzani kuti, palibe amene angabwele kwa ine ngati Atate sanamulole.”
66 Kaamba ka ici, ambili mwa ophunzila ake anabwelela ku zinthu zakumbuyo, ndipo analeka kuyenda naye. 67 Conco Yesu anafunsa atumwi ake 12 aja kuti: “Kodi inunso mufuna kupita?” 68 Simoni Petulo anamuyankha kuti: “Ambuye, tingapitenso kwa ndani? Inu ndi amene muli ndi mawu a moyo wosatha. 69 Ife takhulupilila ndipo tadziwa kuti inu ndinu Woyela wa Mulungu.” 70 Yesu anawauza kuti: “Ndinakusankhani 12, si conco? Koma mmodzi wa inu ndi woneneza.”* 71 Apa iye anali kukamba za Yudasi mwana wa Simoni Isikariyoti, cifukwa ameneyu anali kudzamupeleka, ngakhale kuti anali mmodzi wa atumwi 12 amenewo.
7 Izi zitatha, Yesu anapitiliza kugwila nchito yake* mu Galileya. Iye sanafune kucita zimenezi mu Yudeya, cifukwa Ayuda anali kufuna kumupha. 2 Komabe cikondwelelo ca Misasa ca Ayuda cinali citayandikila. 3 Conco abale ake anamuuza kuti: “Cokani kuno mupite ku Yudeya kuti ophunzila anu nawonso akaone nchito zimene mukucita. 4 Cifukwa palibe munthu amene amacita ciliconse mobisa ngati akufuna kuti anthu amudziwe. Ngati mukucita zinthu zimenezi, dzionetseni poyela ku dzikoli.” 5 Koma abale akewo sanali kukhulupilila mwa iye. 6 Conco Yesu anawauza kuti: “Ine nthawi yanga sinafike, koma kwa inu nthawi iliyonse ndi yoyenela. 7 Dzikoli lilibe cifukwa cokudelani, koma ine limadana nane cifukwa ndimacitila umboni kuti nchito zake ndi zoipa. 8 Inu pitani kucikondweleloko, koma ine sindipitako cifukwa nthawi yanga ikalibe kukwana.” 9 Iye atawauza zimenezi, anakhalabe ku Galileya.
10 Koma pamene abale ake ananyamuka kupita kucikondweleloco, nayenso anapita. Osati moonekela, koma mwakabisila. 11 Conco Ayuda anayamba kumufunafuna kucikondweleloco n’kumafunsa kuti: “Kodi munthu uja ali kuti?” 12 Ndipo anthu oculuka m’khamulo anali kunong’onezana zinthu zambili zokhudza iye. Ena anali kukamba kuti: “Munthu amene uja ndi wabwino.” Koma ena anali kukamba kuti: “Iyayi, iye akusoceletsa khamuli.” 13 Koma palibe amene anali kukamba za iye poyela cifukwa anthuwo anali kuopa Ayuda.
14 Cikondweleloco citafika pakati, Yesu analowa m’kacisi n’kuyamba kuphunzitsa. 15 Ayudawo anadabwa kwambili, ndipo anafunsa kuti: “Kodi munthu ameneyu anawadziwa bwanji Malemba* popeza sanapite ku sukulu?”* 16 Yesu anayankha kuti: “Zimene ndimaphunzitsa sizanga ayi, koma ndi za iye amene anandituma. 17 Ngati munthu afuna kucita cifunilo ca Mulungu, adzadziwa ngati zimene ine ndimaphunzitsa zimacokela kwa Mulunguyo, kapena ngati ndimakamba zongoganiza pa ine ndekha. 18 Aliyense amene amakamba za m’maganizo mwake amadzifunila ulemelelo, koma aliyense wofunila ulemelelo iye amene anamutuma, ameneyo ndi woona ndipo mwa iye mulibe cinyengo. 19 Mose anakupatsani Cilamulo si conco? Koma palibe ngakhale mmodzi wa inu amene amamvela Cilamuloco. Nanga n’cifukwa ciyani mukufuna kundipha?” 20 Khamulo linayankha kuti: “Uli ndi ciwanda iwe. Ndani akufuna kukupha?” 21 Yesu anawayankha kuti: “Ndangocita cinthu cimodzi cokha, koma nonse mwadabwa. 22 Pa cifukwa cimeneci, Mose anakupatsani mdulidwe. Sikuti unacokela kwa Mose ayi, koma unacokela kwa makolo akale, ndipo inu mumacita mdulidwe kwa munthu pa sabata. 23 Ngati munthu mumamucita mdulidwe pa sabata n’colinga cakuti Cilamulo ca Mose cisaphwanyidwe, kodi ine mwandikwiyila cifukwa cakuti ndacilitsa munthu pa tsiku la sabata? 24 Lekani kuweluza moyang’ana maonekedwe akunja, koma weluzani ndi ciweluzo colungama.”
25 Ndiyeno anthu ena okhala mu Yerusalemu anayamba kukamba kuti: “Uyu ndiye munthu amene anthu ena akufuna kumupha, si conco? 26 Koma onani! Iye akulankhula poyela, ndipo iwo sakumuuza ciliconse. Kodi olamulilawa afika potsimikiza kuti ameneyu ndi Khristudi? 27 Ayi, ife tidziwa kumene munthuyu akucokela. Koma Khristu akadzabwela palibe adzadziwa kumene wacokela.” 28 Kenako pamene Yesu anali kuphunzitsa m’kacisi, anafuula kuti: “Inu mundidziwa, ndipo kumene ndimacokela mumadziwakonso. Ine sindinabwele mwa kufuna kwanga, koma amene anandituma ndi weniweni, ndipo inuyo simum’dziwa. 29 Ine ndimudziwa cifukwa ndine nthumwi yake. Ndipo ameneyo ndiye anandituma.” 30 Conco iwo anayamba kufunafuna njila yomugwilila, koma palibe anakwanitsa kutelo cifukwa nthawi yake inali isanafike. 31 Komabe ambili m’khamulo anamukhulupilila ndipo anali kukamba kuti: “Kodi Khristu akadzabwela adzacita zizindikilo zoposa zimene munthu uyu wacita?”
32 Afarisi anamva zimene anthu m’khamulo anali kunong‘onezana ponena za iye. Ndipo ansembe aakulu ndi Afarisi anatuma alonda kuti akamugwile.* 33 Ndiyeno Yesu anakamba kuti: “Ndikhalabe nanu kwa kanthawi ndisanapite kwa amene anandituma. 34 Mudzandifunafuna koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapite, inu simudzakwanitsa kufikako.” 35 Conco Ayudawo anayamba kufunsana kuti: “Kodi munthu ameneyu afuna kupita kuti kumene sitingamupeze? Kodi mwina afuna kupita kwa Ayuda amene anamwazikana pakati pa Agiriki kuti akaphunzitse Agirikiwo? 36 Kodi atanthauzanji pokamba kuti, ‘Mudzandifunafuna koma simudzandipeza, ndipo kumene ndidzapite inu simudzakwanitsa kufikako’?”
37 Pa tsiku lothela, tsiku lalikulu la cikondweleloco, Yesu anaimilila n’kuufula kuti: “Ngati pali wina amene ali ndi ludzu abwele kwa ine adzamwe madzi. 38 Monga mmene malemba amanenela, aliyense woika cikhulupililo mwa ine, ‘Mkati mwake mudzatuluka mitsinje ya madzi amoyo.’” 39 Koma Yesu anakamba izi ponena za mzimu woyela umene anthu oika cikhulupililo mwa iye anali pafupi kulandila. Panthawiyo, anthu anali asanalandile mzimu cifukwa Yesu anali asanalandile ulemelelo. 40 Ena m’khamulo amene anamva mawu amenewa, anayamba kukamba kuti: “Ndithudi uyu ndi Mneneli.” 41 Ena anali kukamba kuti: “Uyu ndi Khristu.” Koma ena anali kukamba kuti: “Kodi Khristu angacokele mu Galileya? 42 Kodi sikuti malemba amanena kuti Khristu adzacokela mu m’badwo wa Davide komanso ku Betelehemu, mudzi umene Davide anali kukhala?” 43 Conco khamulo linagawikana pa nkhani yokhudza iye. 44 Ena a iwo anafuna kumugwila,* koma palibe ngakhale mmodzi amene anakwanitsa kutelo.
45 Ndiyeno alondawo atabwelako, ansembe aakulu ndi Afarisi anawafunsa kuti: “N’cifukwa ciyani simunabwele naye?” 46 Alondawo anayankha kuti: “Palibe munthu amene analankhulapo ngati iyeyu n’kale lonse.” 47 Afarisi anayankha kuti: “Kodi inunso mwasoceletsedwa? 48 Palibe wolamulila kapena Mfarisi ngakhale mmodzi amene waika cikhulupililo mwa iye, alipo kapena? 49 Koma khamu la anthu limene silidziwa Cilamulo ndi lotembeleledwa.” 50 Nikodemo amene anafikila Yesu kumbuyoku, komanso amene anali mmodzi wa Afarisi, anawauza kuti: 51 “Malamulo athu salola kuweluza munthu asanafotokoze mbali yake, komanso tisanadziwe zimene iye anacita, si conco?” 52 Iwo anamuyankha kuti: “Kodi iwenso ndiwe wocokela ku Galileya? Fufuza ndipo sudzapeza pamene pamati mu Galileya mudzatuluka mneneli.”*
8 12 Kenako Yesu anawauzanso kuti: “Ine ndine kuwala kwa dziko. Aliyense amene amanditsatila sadzayenda mumdima ngakhale pang’ono, koma adzakhala ndi kuwala kwa moyo.” 13 Conco Afarisi anamuuza kuti: “Iwe umadzicitila wekha umboni; koma umboni wako si woona.” 14 Yesu anawauza kuti: “Ngakhale kuti ndimadzicitila ndekha umboni, umboni wanga ndi woona, cifukwa ndidziwa kumene ndinacokela komanso kumene ndikupita. Koma inu simukudziwa kumene ndinacokela ndi kumene ndikupita. 15 Inu mumaweluza potengela maonekedwe akunja,* ine sindiweluza munthu aliyense. 16 Koma ndikati ndiweluze, ciweluzo canga cimakhala colungama, cifukwa sindiweluza ndekha koma ndimaweluzila pamodzi ndi Atate amene anandituma. 17 Komanso m’Cilamulo canu munalembedwa kuti: ‘Umboni wa anthu awili ndi woona.’ 18 Ine ndimadzicitila ndekha umboni, ndipo Atate amene anandituma amandicitilanso umboni.” 19 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Atate ako ali kuti?” Yesu anayankha kuti: “Ine simundidziwa ayi, komanso Atate simuwadziwa. Mukanandidziwa ine, mukanadziwanso Atate.” 20 Yesu anakamba mawu amenewa ali m’malo osungila ndalama, pamene anali kuphunzitsa m’kacisi. Koma palibe amene anamugwila cifukwa nthawi yake inali isanakwane.
21 Cotelo iye anawauzanso kuti: “Ine ndikupita, ndipo mudzandifunafuna, koma mudzafa mukali ocimwa. Kumene ine ndikupita simungathe kufikako.” 22 Ndiyeno Ayudawo anayamba kukamba kuti: “Kodi ameneyu akufuna kudzipha? Nanga bwanji akunena kuti, ‘Kumene ine ndikupita simungathe kufikako?’” 23 Iye anapitiliza kuwauza kuti: “Inu ndinu ocokela padziko lapansi, koma ine ndine wocokela kumwamba. Inu ndinu a m’dzikoli, koma ine sindinacokele m’dzikoli. 24 N’cifukwa cake ndakuuzani kuti: Mudzafa mukali ocimwa. Cifukwa ngati simukhulupilila kuti amene munali kumuyembekezela uja ndine, mudzafa mukali ocimwa.” 25 Conco iwo anayamba kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe ndani?” Yesu anawayankha kuti: “Nditayilanji nthawi kukamba nanu? 26 Ndili ndi zambili zimene ndingakambe zokhudza inu ndi kupeleka ciweluzo. Kukamba zoona, amene anandituma ndi woona, ndipo zimene ndinamva kwa iye ndimazilankhula m’dzikoli.” 27 Iwo sanazindikile kuti anali kuwauza za Atate. 28 Kenako Yesu anawauza kuti: “Mukadzakweza Mwana wa munthu, mudzadziwa kuti amene munali kuyembekezela uja ndine, komanso kuti sindicita ciliconse congoganiza pandekha. Koma ndimalankhula zinthu zimenezo mogwilizana ndi zimene Atate anandiphunzitsa. 29 Ndipo amene ananditumayo ali nane. Iye sanandisiye ndekha, cifukwa nthawi zonse ndimacita zinthu zomukondweletsa.” 30 Pamene iye anali kukamba zimenezi, anthu ambili anamukhulupilila.
31 Ndiyeno Yesu anapitiliza kuuza Ayuda amene anamukhulupililawo kuti: “Mukapitiliza kusunga mawu anga, ndiye kuti ndinudi ophunzila anga. 32 Mudzadziwa coonadi, ndipo coonadico cidzakumasulani.” 33 Iwo anamuyankha kuti: “Ife ndife ana a Abulahamu, ndipo sitinakhalepo akapolo a munthu aliyense. Ndiye n’cifukwa ciyani ukunena kuti, ‘Mudzamasulidwa’?” 34 Yesu anawayankha kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, aliyense amene amacita chimo ndi kapolo wa chimo. 35 Ndiponso kapolo sakhala m’nyumba ya mbuye wake kwamuyaya, koma mwana ndi amene amakhalamo kwamuyaya. 36 Conco ngati Mwana wakumasulani, mudzakhaladi omasuka. 37 Ndidziwa kuti ndinu ana a Abulahamu. Koma mukufuna kundipha cifukwa mawu anga alibe malo mwa inu. 38 Ine ndimakamba zinthu zimene ndinaona pamene ndinali ndi Atate, koma inu mumacita zinthu zimene mwamva kwa atate wanu.” 39 Iwo anamuyankha kuti: “Atate wathu ndi Abulahamu.” Yesu anawauza kuti: “Mukanakhala ana a Abulahamu, mukanacita nchito za Abulahamu. 40 Koma tsopano mufuna kundipha, ine munthu amene ndakuuzani coonadi cimene ndinamva kwa Mulungu. Abulahamu sanacite zimenezi. 41 Inu mukucita nchito za atate wanu.” Iwo anamuuza kuti: “Ife sitinabadwe kucokela mu ciwelewele,* koma tili ndi Atate mmodzi, Mulungu.”
42 Yesu anawauza kuti: “Mulungu akanakhala Atate wanu, mukanandikonda, cifukwa ine ndinabwela kucokela kwa Mulungu ndipo ndili pano. Sindinabwele mwakufuna kwanga, koma Iyeyo ndiye anandituma. 43 N’cifukwa ciyani simukumvetsa zimene ndikukamba? N’cifukwa cakuti simufuna kumvetsela mawu anga. 44 Inu ndinu ocokela kwa atate wanu Mdyelekezi, ndipo mumafuna kucita zokhumba za atate wanuyo. Ameneyo ndi wakupha kucokela paciyambi, ndipo sanapitilize kukhala m’coonadi, cifukwa mwa iye mulibe coonadi. Iye akamakamba bodza amaonetsa mmene alili cifukwa ndi wabodza, komanso ndiye tate wake wa bodza. 45 Koma cifukwa cakuti ndimakuuzani zoona, simundikhulupilila. 46 Ndani wa inu amene ali ndi umboni woonetsa kuti ndacita chimo? Ngati ndimalankhula zoona, n’cifukwa ciyani simundikhulupilila? 47 Wocokela kwa Mulungu amamvetsela mawu a Mulungu. Inu sindinu ocokela kwa Mulungu. Ndiye cifukwa cake simumvetsela.”
48 Ayudawo anamuyankha kuti: “Kodi tikunama ponena kuti, ‘Ndiwe Msamariya ndipo uli ndi ciwanda’?” 49 Yesu anayankha kuti: “Ine ndilibe ciwanda, koma ndimalemekeza Atate, ndipo inu mukundinyoza. 50 Koma ine sindidzifunila ulemelelo ayi, ndi Mulungu amene amafuna kuti ndilemekezedwe, ndipo Iye ndi woweluza. 51 Ndithudi ndikukuuzani, ngati munthu amasunga mawu anga, sadzaona imfa mpang’ono pomwe.” 52 Ayudawo anamuuza kuti: “Tsopano tadziwa kuti ulidi ndi ciwanda. Abulahamu anamwalila, nawonso aneneli anamwalila, koma iwe ukukamba kuti, ‘Ngati munthu amasunga mawu anga sadzaona imfa ngakhale pang’ono.’ 53 Kodi iwe ndiwe wamkulu kuposa Abulahamu atate wathu, amene anamwalila? Aneneli nawonso anamwalila. Ndiye umadziona kuti ndiwe ndani?” 54 Yesu anayankha kuti: “Ndikadzifunila ndekha ulemelelo, ulemelelo wangawo ndi wopanda pake. Atate wanga ndiye amandipatsa ulemelelo, amene inu mumati ndi Mulungu wanu. 55 Mpaka pano inu simumudziwa, koma ine ndimudziwa. Ndipo ngati ndinganene kuti sindimudziwa, ndiye kuti ndingakhale wabodza ngati inu. Koma ndimudziwa ndithu, ndipo ndimasunga mawu ake. 56 Abulahamu atate wanu anakondwela kwambili cifukwa coyembekezela kuona tsiku langa, ndipo ataliona anasangalala.” 57 Kenako Ayudawo anamuuza kuti: “Iwe ukalibe kukwanitsa ngakhale zaka 50, koma ukuti unamuona Abulahamu?” 58 Yesu anawauza kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, Abulahamu asanakhaleko n’komwe ine ndinaliko kale.” 59 Conco iwo anatola miyala kuti amuponye nayo, koma Yesu anabisala, kenako anatuluka m’kacisi.
9 Pamene Yesu anali kuyenda, anaona munthu wina amene anabadwa wakhungu. 2 Ophunzila ake anamufunsa kuti: “Mphunzitsi,* anacimwa ndani kuti munthu uyu abadwe wakhungu, ndi iyeyo kapena makolo ake?” 3 Yesu anayankha kuti: “Munthu uyu kapena makolo ake, onse sanacimwe. Koma zinakhala conco kuti nchito za Mulungu zionekele pa iye. 4 Tiyenela kugwila nchito za Mulungu amene anandituma kukali masana, cifukwa usiku ukubwela pamene munthu sangagwile nchito. 5 Pamene ine ndili m’dziko, ndine kuwala kwa dziko.” 6 Atakamba zimenezi, analavulila mata pansi n’kukanda matope ndi matawo, kenako anapaka matopewo m’maso mwa munthuyo. 7 Ndipo anamuuza kuti: “Pita ukasambe m’dziwe la Siloamu” (dzinali kumasulila kwake ndi “Wotumizidwa”). Iye anapitadi kukasamba, ndipo anabwelako akuona.
8 Ndiyeno anthu okhala naye pafupi komanso amene kale anali kumuona akupemphapempha anayamba kukamba kuti: “Kodi munthu uyu si uja anali kukhala pansi n’kumapemphapempha?” 9 Anthu ena anali kukamba kuti: “Ndi ameneyu.” Pomwe ena anali kukamba kuti: “Ayi angofanana cabe.” Koma mwiniwakeyo anali kukamba kuti “Ndine amene.” 10 Conco iwo anamufunsa kuti: “Nanga zinatheka bwanji kuti maso ako atseguke?” 11 Iye anayankha kuti: “Munthu wina dzina lake Yesu anakanda matope n’kundipaka m’maso ndipo anandiuza kuti, ‘Pita ku Siloamu ukasambe.’ Conco ine ndinapitadi kukasamba, ndipo ndinayamba kuona.” 12 Atatelo, iwo anamufunsa kuti: “Munthu ameneyo ali kuti?” Iye anayankha kuti: “Kaya sindidziwa.”
13 Anthuwo anapeleka munthu amene anali wakhungu uja kwa Afarisi. 14 Zinangocitika kuti tsiku limene Yesu anakanda matope n’kutsegula maso ake linali la Sabata. 15 Pa nthawiyo, Afarisi nawonso anayamba kumufunsa munthuyo zimene zinacitika kuti ayambe kuona. Iye anawauza kuti: “Anapaka matope m’maso mwanga, ndipo ine ndinasamba, kenako ndinayamba kuona.” 16 Ena mwa Afarisiwo anayamba kunena kuti: “Munthuyo si wocokela kwa Mulungu, cifukwa sasunga Sabata.” Enanso anali kukamba kuti: “Kodi munthu wocimwa angathe bwanji kucita zozizwitsa* ngati izi?” Conco pakati pawo panakhala magawano. 17 Iwo anafunsanso munthu amene anali wakhungu uja kuti: “Ukutipo ciyani za munthu uyu popeza watsegula maso ako?” Munthuyo anayankha kuti: “Iye ndi mneneli.”
18 Koma Ayudawo sanakhulupilile kuti munthuyu analidi wakhungu ndipo wayamba kuona, mpaka anaitana makolo ake. 19 Iwo anafunsa makolowo kuti: “Kodi uyu ndiye mwana wanu uja amene mumati anabadwa wakhungu? Nanga zatheka bwanji kuti ayambe kuona?” 20 Makolo ake anayankha kuti: “Tidziwa kuti uyu ndi mwana wathu, komanso kuti anabadwa wakhungu. 21 Koma zakuti wayamba bwanji kuona, ife sitidziwa, komanso zakuti watsegula maso ake ndani, sitidziwanso. Mufunseni, ndi wamkulu afotokoze yekha.” 22 Makolo ake anayankha conco cifukwa anali kuopa Ayuda, pakuti Ayudawo anali atagwilizana kale zakuti munthu aliyense amene avomeleze kuti Yesu ndi Khristu, afunika kucotsedwa m’sunagoge. 23 Ndiye cifukwa cake makolo akewo anati: “Ndi wamkulu, mufunseni.”
24 Conco iwo anaitananso munthu amene anali wakhungu uja kaciwili n’kumuuza kuti: “Lemekeza Mulungu. Ife tikudziwa kuti munthuyu ndi wocimwa.” 25 Iye anayankha kuti: “Zakuti iye ndi wocimwa ine sindizidziwa. Cimene ndidziwa n’cakuti ndinali wakhungu, koma tsopano ndikuona.” 26 Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Anakucita ciyani? Nanga anatsegula bwanji maso ako?” 27 Iye anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma simunamve. Kodi n’cifukwa ciyani mufuna kumvanso? Kodi nanunso mufuna kukhala ophunzila ake?” 28 Pamenepo iwo anamuyankha monyoza kuti: “Iwe ndiwe wophunzila wa munthu amene uja, koma ife ndife ophunzila a Mose. 29 Ife tidziwa kuti Mulungu analankhula ndi Mose, koma za munthu uyu sitidziwa kumene anacokela.” 30 Munthuyo anawayankha kuti: “Zimenezi n’zodabwitsa kwambili, kuti simudziwa kumene iye anacokela, koma watsegula maso anga! 31 Tidziwa kuti Mulungu samvetsela wocimwa, koma ngati munthu amaopa Mulungu ndi kucita cifunilo cake, amamumvetsela munthuyo. 32 Kuyambila kalekale sitinamvepo kuti wina watsegula maso a munthu amene anabadwa wakhungu. 33 Ngati munthuyu sanacokele kwa Mulungu, sakanakwanitsa kucita ciliconse.” 34 Iwo anamuyankha kuti: “Nonsenu munabadwila mu ucimo, koma kodi ukufuna kutiphunzitsa?” Basi pamenepo anamucotsa m’sunagoge!
35 Ndiyeno Yesu anamva kuti munthu uja amucotsa m’sunagoge, ndipo atamupeza, anamufunsa kuti: “Kodi umukhulupilila Mwana wa munthu?” 36 Munthuyo anayankha kuti: “Kodi Mwana wa munthuyo ndi uti kuti ndikhulupilile mwa iye?” 37 Yesu anamuuza kuti: “Wamuona kale, ndipo ndi amene akukamba nawe.” 38 Iye anati: “Ndakhulupilila mwa inu Ambuye.” Kenako anamugwadila.* 39 Ndiyeno Yesu anati: “Ndinabwela m’dziko kuti anthu aweluzidwe n’colinga cakuti amene saona ayambe kuona, ndipo amene akuona akhale akhungu.” 40 Afarisi amene anali ndi munthuyo anamva zimene Yesu anali kukamba, ndipo anamuuza kuti: “Kodi uganiza kuti nafenso ndife akhungu?” 41 Yesu anawauza kuti: “Mukanakhala akhungu simukanakhala ndi chimo. Koma cifukwa mukunena kuti, ‘Mukuona,’ chimo lanu likhalabe nanu.”
10 “Ndithudi ndikukuuzani, amene amalowa m’khola la nkhosa osadzela pakhomo, koma mocita kukwelela pamalo ena ake, ameneyo ndi wakuba komanso wolanda zinthu za ena. 2 Koma wolowela pakhomo ndi m’busa wa nkhosazo. 3 Mlonda wapakhomo amamutsegulila ameneyu, ndipo nkhosa zimamva mawu ake. Iye amaitana nkhosa zake mwa kuzichula maina ndi kuzitsogolela kuti zituluke. 4 Akazitulutsa nkhosa zake zonse, amazitsogolela. Ndipo nkhosazo zimamutsatila cifukwa zimadziwa mawu ake. 5 Mlendo sizingam’tsatile nkhosazo, koma zidzamuthawa, cifukwa sizidziwa mawu a alendo.” 6 Yesu anawauza fanizoli, koma iwo sanamvetse tanthauzo la zimene anali kuwauzazo.
7 Conco Yesu anakambanso kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, ine ndine khomo la nkhosa. 8 Onse amene abwela n’kumanamizila kuti ndi abusa enieni, ndi mbala komanso olanda, ndipo nkhosa sizinawamvele. 9 Ine ndine khomo. Munthu aliyense wolowa kupitila mwa ine, adzapulumutsidwa. Ameneyo adzalowa ndi kutuluka, ndipo adzapeza msipu. 10 Mbala sibwelela cina koma kuba, kupha, ndi kuwononga. Koma ine ndabwela kuti iwo akhale ndi moyo, inde moyo wosatha. 11 Ine ndine m’busa wabwino. Ndipo m’busa wabwino amapeleka moyo wake kaamba ka nkhosa. 12 Munthu waganyu amene si m’busa komanso amene nkhosazo si zake, akaona mmbulu ukubwela amasiya nkhosazo n’kuthawa. Ndiyeno mmbuluwo umagwilapo nkhosa zina, ndipo zina zonse zimathawa n’kumwazikana. 13 Iye amatelo cifukwa ndi waganyu cabe, ndipo sasamala za nkhosazo. 14 Ine ndine m’busa wabwino. Nkhosa zanga ndimazidziwa, ndipo nazonso zimandidziwa, 15 monga mmene Atate amandidziwila, inenso ndimawadziwa. Cotelo ndikupeleka moyo wanga kaamba ka nkhosazo.
16 “Ndili ndi nkhosa zina zimene si zam’khola ili. Nazonso ndiyenela kuzibweletsa m’khola ili, ndipo zidzamvela mawu anga. Zidzakhala gulu limodzi, ndipo m’busa wawo adzakhala mmodzi. 17 Ndiye cifukwa cake Atate amandikonda cifukwa ndikupeleka moyo wanga kuti ndikaulandilenso. 18 Kulibe munthu amene angacotse moyo wanga, koma ndikuupeleka mwa kufuna kwanga. Ndili ndi mphamvu zoupeleka komanso ndili ndi mphamvu zoulandilanso. Izi n’zimene Atate wanga anandilamula kucita.”*
19 Ayuda anagawikananso cifukwa ca mawu amenewa. 20 Ambili a iwo anali kukamba kuti: “Ali ndi ciwanda ndipo wacita misala. N’cifukwa ciyani mukumumvetsela?” 21 Ena anati: “Mawu awa si a munthu wogwidwa ndi ciwanda. Kodi ciwanda cingatsegule maso a anthu akhungu?”
22 Pa nthawiyi, ku Yerusalemu kunali Cikondwelelo ca Kupatulila Kacisi. Inali nyengo yozizila, 23 ndipo Yesu anali kuyenda m’kacisimo m’khonde lokhala ndi zipilala la Solomo. 24 Ndiyeno Ayuda anamuzungulila n’kuyamba kumufunsa kuti: “Kodi udzativutitsa maganizo mpaka liti? Tiuze mosapita m’mbali ngati ndiwe Khristu.” 25 Yesu anawayankha kuti: “Ndakuuzani kale, koma simukukhulupilila. Nchito zimene ndikuzicita m’dzina la Atate wanga, zikundicitila umboni. 26 Koma simukukhulupililabe, cifukwa si ndinu nkhosa zanga. 27 Nkhosa zanga zimamvela mawu anga. Ndipo ndimazidziwa komanso zimanditsatila. 28 Ndidzazipatsa moyo wosatha ndipo sizidzawonongedwa konse. Palibenso amene adzazitsomphola m’dzanja langa. 29 Nkhosa zimene Atate andipatsa n’zofunika kwambili kuposa zinthu zina zonse, ndipo palibe amene angazitsomphole m’dzanja la Atate. 30 Ine ndi Atate ndife amodzi.”*
31 Apanso Ayuda anatola miyala kuti amuponye nayo. 32 Yesu anawauza kuti: “Ndakuonetsani nchito zabwino zambili zocokela kwa Atate. Pa nchitozo, ndi iti imene mufuna kundiponyela miyala?” 33 Ayudawo anamuyankha kuti: “Sitikufuna kukuponya miyala cifukwa ca nchito yabwino ayi, koma cifukwa conyoza Mulungu. Pakuti iwe ukudzipanga mulungu, pamene ndiwe munthu cabe.” 34 Yesu anawayankha kuti: “Kodi m’Cilamulo canu simunalembedwe kuti, ‘Ine ndinati: “Inu ndinu milungu”’?* 35 Tidziwa kuti Malemba sangathe mphamvu. Conco ngati Mulungu anachula anthu otsutsidwa ndi mawu ake kuti ‘milungu,’ 36 kodi mukuuza ine amene Atate anandiyeletsa n’kunditumiza m’dzikoli kuti, ‘Ukunyoza Mulungu,’ cifukwa ndinati, ‘Ndine Mwana wa Mulungu’? 37 Ngati sindicita nchito za Atate wanga, musandikhulupilile. 38 Koma ngati ndikuzicita, ngakhale kuti simundikhulupilila, khulupililani nchitozo, kuti mudziwe ndi kupitiliza kudziwa kuti ine ndi Atate ndife ogwilizana.” 39 Iwo anafunanso kumugwila, koma anawathawa mozemba.
40 Yesu anawolokanso Yorodano n’kupita kumalo kumene Yohane anali kubatizila anthu poyamba, ndipo anakhala kumeneko. 41 Anthu ambili anabwela kwa iye n’kuyamba kunena kuti: “Yohane sanacite cozizwitsa* ciliconse, koma zonse zimene Yohane anakamba zokhudza munthu uyu zinali zoona.” 42 Conco ambili kumeneko anamukhulupilila.
11 Tsopano munthu wina dzina lake Lazaro anali kudwala. Anali wa m’mudzi wa Betaniya, mmenenso munali kukhala Mariya ndi m’bale wake Marita. 2 Mariyayu ndi uja amene anathila mafuta onunkhila Ambuye ndi kupukuta mapazi awo ndi tsitsi lake. Lazaro amene anali kudwala anali mlongo wake. 3 Conco azilongo akewo anatumiza uthenga kwa Yesu kuti: “Ambuye! munthu uja amene mumamukonda akudwala.” 4 Koma Yesu atamva zimenezi anakamba kuti: “Kudwalaku mapeto ake sadzakhala imfa cabe ayi, koma kudzapangitsa kuti Mulungu alandile ulemelelo, kuti Mwana wa Mulungu alemekezedwe cifukwa ca kudwalako.”
5 Yesu anali kukonda Marita, Mariya, ndi Lazaro. 6 Koma atamva kuti Lazaro akudwala, anakhalabe kumalo kumene anali, kwa masiku ena awili. 7 Pambuyo pa masiku awiliwo, iye anauza ophunzila ake kuti: “Tiyeni tipitenso ku Yudeya.” 8 Ndiyeno ophunzilawo anamuuza kuti: “Mphunzitsi,* posacedwapa anthu a ku Yudeya anali kufuna kukuponyani miyala, ndiye mufunanso kupita kumeneko?” 9 Yesu anayankha kuti: “Masana ali ndi maola 12 si conco? Ngati munthu akuyenda masana, sapunthwa ndi ciliconse cifukwa amaona kuwala kwa dzikoli. 10 Koma munthu akamayenda usiku, amapunthwa cifukwa mwa iye mulibe kuwala.”
11 Pambuyo pokamba zimenezi, iye ananenanso kuti: “Lazaro bwenzi lathu ali m’tulo, koma ndipita kumeneko kukamuutsa.” 12 Ndiyeno ophunzilawo anamuuza kuti: “Ambuye ngati akugona ndiye kuti adzakhala bwino.” 13 Apa Yesu anali kukamba za imfa ya Lazaro. Koma ophunzilawo anaganiza kuti anali kukamba za kugona kopumula cabe. 14 Kenako Yesu anawauza mosapita m’mbali kuti: “Lazaro wamwalila, 15 ndipo ndine wokondwa cifukwa ca inu kuti sindinali kumeneko, kuti mukhulupilile. Koma tiyeni tipite kwa iye.” 16 Conco Thomasi, wochedwanso Didimo, anauza ophunzila anzake kuti: “Nafenso tiyeni tipite, kuti tikafele naye limodzi.”
17 Pamene Yesu anali kufika kumeneko, anapeza kuti Lazaro wakhala kale m’manda* masiku anayi. 18 Mudzi wa Betaniya unali pafupi ndi Yerusalemu pamtunda wa makilomita pafupifupi atatu.* 19 Ndipo Ayuda ambili anabwela kwa Marita ndi Mariya kudzawatonthoza kaamba ka imfa ya mlongo wawo. 20 Marita atamva kuti Yesu akubwela, anapita kukamucingamila, koma Mariya anatsala kunyumba. 21 Kenako Marita anauza Yesu kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno, mlongo wanga sakanamwalila. 22 Koma ngakhale pano, ndikudziwa kuti ciliconse cimene mungamupemphe Mulungu, iye adzakupatsani.” 23 Yesu anamuuza kuti: “Mlongo wako adzauka.” 24 Marita anamuuza kuti: “Ndidziwa kuti adzauka pa kuuka kwa akufa m’tsiku lothela.” 25 Yesu anamuuza kuti: “Ine ndine kuuka ndi moyo. Aliyense wokhulupilila ine, ngakhale atamwalila adzakhalanso ndi moyo. 26 Komanso aliyense amene ali ndi moyo ndipo amandikhulupilila, sadzafa ayi. Kodi ukhulupilila zimenezi?” 27 Marita anayankha kuti: “Inde Ambuye. Ndimakhulupilila kuti ndinu Khristu Mwana wa Mulungu, amene ananenedwelatu kuti adzabwela m’dzikoli.” 28 Iye atanena zimenezi, anapita kukaitana m’bale wake n’kumuuza mseli kuti: “Mphunzitsi wabwela, ndipo akukuitana.” 29 Mariya atamva izi, ananyamuka mwamsanga n’kupita kwa Yesu.
30 Apa n’kuti Yesu asanalowe m’mudzimo. Koma anali akali pamalo pomwe Marita anakumana naye. 31 Ayuda amene anali kutonthoza Mariya m’nyumbamo ataona kuti mwamsanga watuluka n’kupita panja, anamutsatila. Iwo anaganiza kuti anali kupita kumanda* kukalila. 32 Mariya atafika kumene kunali Yesu ndi kumuona, anagwada mpaka nkhope yake pansi kumapazi a Yesu n’kumuuza kuti: “Ambuye, mukanakhala kuno, mlongo wanga sakanamwalila.” 33 Yesu ataona Mariya ndi Ayuda amene anabwela naye akulila, anadzuma cifukwa covutika mumtima* ndi kumva cisoni. 34 Iye anafunsa kuti: “Mwamuika kuti?” Iwo anayankha kuti: “Ambuye, tiyeni mukaone.” 35 Yesu anagwetsa misozi. 36 Ayuda ataona zimenezi anayamba kunena kuti: “Taonani, anali kumukonda kwambili!” 37 Koma ena a iwo anati: “Kodi munthu uyu amene anatsegula maso a munthu wakhungu uja, sakanacitapo kanthu kuti mnzakeyu asamwalile?”
38 Kenako Yesu atadzumanso cifukwa covutika mumtima, anafika kumandako.* Kwenikweni mandawo anali phanga. Ndipo analitseka ndi cimwala. 39 Yesu anati: “Cotsani cimwalaci.” Marita, mlongo wa womwalilayo anamuuza kuti: “Ambuye, apa ayenela kuti wayamba kununkha, cifukwa papita masiku anayi tsopano.” 40 Yesu anamuuza kuti: “Kodi sindinakuuze kuti ngati ukhulupilila udzaona ulemelelo wa Mulungu?” 41 Conco iwo anacotsa cimwalaco. Ndiyeno Yesu anakweza maso ake kumwamba n’kunena kuti: “Atate, ndikukuyamikani kuti mwandimva. 42 Inde, ndidziwa kuti mumandimva nthawi zonse, koma ndanena izi cifukwa ca khamu la anthu limene laimilila panoli, kuti akhulupilile kuti ndinu amene munandituma.” 43 Atakamba zimenezi, anafuula mokweza mawu kuti: “Lazaro, tuluka!” 44 Pamenepo, munthu amene anali wakufa uja anatuluka, ndipo mapazi ndi manja ake anali okulungidwa ndi nsalu, nkhope yake nayonso inali yokulungidwa ndi nsalu. Yesu anawauza kuti: “M’masuleni kuti akwanitse kuyenda.”
45 Conco, Ayuda ambili amene anabwela kwa Mariya n’kuona zimene Yesu anacitazo, anamukhulupilila. 46 Koma ena a iwo anapita kwa Afarisi n’kukawauza zimene Yesu anacita. 47 Conco, ansembe aakulu ndi Afarisi anasonkhanitsa Khoti Yaikulu ya Ayuda* n’kukamba kuti: “Kodi ticite ciyani popeza munthu uyu akucita zozizwitsa* zambili? 48 Ngati tingamulekelele, onse adzamukhulupilila, ndipo Aroma adzabwela n’kudzatilanda malo* athu ndi mtundu wathu.” 49 Koma mmodzi wa iwo, dzina lake Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe caka cimeneco, anawauza kuti: “Palibe cimene mudziwa inu, 50 ndipo simukuona kuti n’caphindu kwa inu kuti munthu mmodzi afele anthu ambili m’malo mwakuti mtundu wonse uwonongeke.” 51 Iye sanakambe zimenezi mongoganiza pa iye yekha, koma cifukwa anali mkulu wa ansembe caka cimeneco, analosela kuti Yesu adzafela mtunduwo. 52 Ndipo osati cabe kufela mtundu, koma kusonkhanitsanso pamodzi ana a Mulungu amene anamwazikana. 53 Cotelo kuyambila tsiku limenelo anamukonzela ciwembu cakuti amuphe.
54 Conco, Yesu sanali kuyendanso moonekela pakati pa Ayuda, koma anacoka kumeneko n’kupita kucigawo cakufupi ndi cipululu, mumzinda wochedwa Efuraimu, ndipo anakhala kumeneko pamodzi ndi ophunzila ake. 55 Tsopano Pasika wa Ayuda anali atayandikila, ndipo anthu ambili ocokela kumadela a kumidzi anapita ku Yerusalemu Pasikayo asanayambe, kuti akacite mwambo wa kudziyeletsa. 56 Iwo anali kusakila Yesu, ndipo ataimilila m’kacisimo, anali kukambilana kuti: “Muganiza bwanji? Kodi ameneyu sabwela ku cikondweleloci?” 57 Koma ansembe aakulu ndi Afarisi analamula kuti ngati wina wadziwa kumene Yesu ali, awadziwitse kuti akamugwile.*
12 Kutangotsala masiku 6 kuti Pasika acitike, Yesu anafika ku Betaniya kumene kunali Lazaro, uja amene iye anamuukitsa kwa akufa. 2 Conco, anamukonzela cakudya camadzulo kumeneko. Marita anali kuwatumikila, ndipo Lazaro anali mmodzi wa anthu omwe anali kudya* naye. 3 Ndiyeno Mariya anatenga mafuta onunkhila odula kwambili, nado weniweni, ndipo mafutawo anali okwana magalamu 327. Iye anathila mafutawo pamapazi a Yesu n’kuwapukuta ndi tsitsi lake. M’nyumba monsemo munangoti guu kafungo kabwino ka mafuta onunkhilawo. 4 Koma Yudasi Isikariyoti, mmodzi wa ophunzila ake, amene anali atatsala pang’ono kumupeleka, anati: 5 “N’cifukwa ciyani mafuta onunkhilawa sanagulitsidwe madinari 300, ndi kupeleka ndalamazo kwa osauka?” 6 Iye anakamba zimenezi osati cifukwa codela nkhawa osauka ayi, koma cifukwa cakuti anali mbala. Iye ndiye anali kusunga bokosi la ndalama, ndipo anali kubapo pandalama zoikidwa mmenemo. 7 Ndiyeno Yesu anati: “Mulekeni acite mwambo umenewu pokonzekela tsiku la kuikidwa kwanga m’manda. 8 Pakuti osaukawo muli nawo nthawi zonse, koma ine simudzakhala nane nthawi zonse.”
9 Ndiyeno khamu la Ayuda linadziwa kuti Yesu anali ku Betaniya. Conco linabwela osati cabe cifukwa ca Yesu, koma kudzaonanso Lazaro amene anamuukitsa kwa akufa. 10 Tsopano ansembe aakulu anakonza ciwembu cakuti aphenso Lazaro, 11 popeza Ayuda ambili anali kupita ku Betaniya, ndipo anali kukhulupilila mwa Yesu cifukwa ca Lazaroyo.
12 Tsiku lotsatila, khamu lalikulu limene linabwela ku cikondweleloco linamva kuti Yesu akubwela mu Yerusalemu. 13 Conco anatenga nthambi za kanjedza n’kupita kukamucingamila, ndipo anayamba kufuula kuti: “M’pulumutseni! Wodalitsika ndi iye wobwela m’dzina la Yehova, Mfumu ya Isiraeli!” 14 Yesu atapeza bulu wamng’ono anakwela pabuluyo monga mmene Malemba amanenela kuti: 15 “Usacite mantha, iwe mwana wamkazi wa Ziyoni. Taona! Mfumu yako ikubwela, itakwela pa mwana wamphongo wa bulu.” 16 Poyamba ophunzila ake sanamvetse zimenezi. Koma Yesu atapatsidwa ulemelelo, iwo anakumbukila kuti zimene anamucitilazo zinafanana ndendende ndi zimene zinalembedwa zokhudza iye.
17 Tsopano khamu limene linalipo poitana Lazaro kuti atuluke m’manda* ndi kumuukitsa kwa akufa, linapitiliza kumucitila umboni. 18 Ici n’cifukwa cina cimene cinapangitsa khamulo kupita kukamucingamila, popeza anamva kuti iye anacita cozizwitsa* cimeneci. 19 Conco Afarisi anayamba kukambilana kuti: “Mwaona, mapulani athu alephelelatu. Taonani! Dziko lonse lakhamukila kwa iye.”
20 Ndiyeno pa anthu amene anabwela kudzalambila ku cikondweleloco, panalinso Agiriki. 21 Iwo anapita kwa Filipo, wocokela ku Betsaida wa ku Galileya, ndipo anayamba kumupempha kuti: “Bambo, tikufuna kuona Yesu.” 22 Filipo anapita kukauza Andireya. Ndipo Andireya ndi Filipo anapita kukauza Yesu.
23 Koma Yesu anawayankha kuti: “Nthawi yafika yakuti Mwana wa munthu alemekezeke. 24 Ndithudi ndikukuuzani, ngati kambewu ka tiligu sikanagwele m’nthaka n’kufa, kamakhalabe kambewu kamodzi. Koma kakafa, kamabala zipatso zambili. 25 Aliyense wokonda moyo wake akuuwononga, koma aliyense amene amadana ndi moyo wake m’dziko lino akuuteteza kuti akapeze moyo wosatha. 26 Ngati munthu akufuna kunditumikila, anditsatile. Ndipo kumene ine ndidzakhala, mtumiki wanga adzakhalanso komweko. Aliyense wonditumikila, Atate adzamulemekeza. 27 Tsopano ndavutika kwambili mumtima,* kodi ndinene ciyani? Atate, ndipulumutseni ku nthawi iyi. Komabe ndiye cifukwa cake ndinabwela kuti nthawiyi indifikile. 28 Atate lemekezani dzina lanu.” Ndiyeno kunamveka mawu kucokela kumwamba akuti: “Ndalilemekeza ndipo ndidzalilemekezanso.”
29 Gulu la anthu amene anaimilila pamalopo atamva mawuwo, anayamba kukamba kuti kwagunda bingu. Ena anali kunena kuti: “Mngelo wakamba naye.” 30 Yesu anawauza kuti: “Mawuwa amveka osati cifukwa ca ine, koma cifukwa ca inu. 31 Tsopano dzikoli likuweluzidwa. Wolamulila wa dzikoli aponyedwa kunja tsopano. 32 Koma ndikadzakwezedwa* m’mwamba padziko lapansi, ndidzabweletsa anthu a mtundu uliwonse kwa ine.” 33 Ananena zimenezi pofuna kuonetsa mmene adzafela pakangopita nthawi yocepa. 34 Ndiyeno gulu la anthulo linamuyankha kuti: “Tinamva m’Cilamulo kuti Khristu adzakhalako kosatha. Nanga n’cifukwa ciyani mukukamba kuti Mwana wa munthu ayenela kukwezedwa m’mwamba?* Kodi Mwana wa munthu ameneyo ndani?” 35 Yesu anawauza kuti: “Kuwala kudzakhalabe nanu kwa kanthawi kocepa. Yendani pamene kuwala kukalipo kuti mdima usakufikileni. Munthu aliyense woyenda mumdima sadziwa kumene akupita. 36 Pomwe kuwala kukalipo, onetsani kuti mumakhulupilila kuwalako, kuti mukhale ana a kuwala.”
Yesu atanena zimenezo, anacoka n’kukawabisala. 37 Ngakhale kuti iye anacita zozizwitsa* zambili pamaso pawo, iwo sanamukhulupililebe. 38 Zinatelo kuti mawu a mneneli Yesaya akwanilitsidwe. Iye anati: “Yehova, ndani wakhulupilila zimene wamva kwa ife?* Ndipo kodi dzanja la Yehova laonetsedwa kwa ndani?” 39 Cifukwa cimene sanakhulupilile, n’cimene Yesaya ananenso kuti: 40 “Iye wacititsa khungu maso awo, ndipo waumitsa mitima yawo kuti asaone ndi maso awo, komanso kuti mitima yawo isamvetse zinthu n’kutembenuka kuti ine ndiwacilitse.” 41 Yesaya anakamba zimenezi cifukwa anaona ulemelelo wa Khristu, ndipo anafotokoza zokhudza iye. 42 Komabe, ambili anamukhulupilila, ngakhalenso olamulila. Koma iwo sanamuvomeleze poyela cifukwa coopa Afarisi kuti angawacotse m’sunagoge. 43 Pakuti iwo anali kukonda ulemelelo wocokela kwa anthu kuposa ulemelelo wocokela kwa Mulungu.
44 Koma Yesu anafuula kuti: “Aliyense wokhulupilila ine, sakhulupilila cabe ine, koma amakhulupililanso amene anandituma. 45 Ndipo aliyense waona ine, waonanso amene anandituma. 46 Ndabwela monga kuwala m’dzikoli, kuti aliyense wondikhulupilila asapitilize kukhala mumdima. 47 Ngati munthu wamva mawu anga koma osawasunga, sindingamuweluze cifukwa ndinabwela kudzapulumutsa dziko osati kudzaliweluza. 48 Aliyense wondinyalanyaza komanso wosalandila mawu anga, pali mmodzi amene adzamuweluza. Mawu amene ndalankhula ndi amene adzamuweluza pa tsiku lothela. 49 Cifukwa sindinakambepo ciliconse congoganiza pandekha, koma Atate amene anandituma ndi amene anandilamula zimene ndiyenela kukamba ndi zimene ndiyenela kulankhula. 50 Ndipo ndikudziwa kuti lamulo limenelo ndi lothandiza anthu kudzapeza moyo wosatha. Conco, zilizonse zimene ndimakamba, ndimazikamba mogwilizana ndi zimene Atate anandiuza.”
13 Tsopano cikondwelelo ca Pasika cisanafike, Yesu anadziwilatu kuti nthawi yake yakuti acoke m’dzikoli n’kupita kwa Atate wake yakwana. Iye anawakonda kwambili ophunzila ake amene anali m’dzikoli, moti anawakonda mpaka pamapeto a moyo wake. 2 Cakudya camadzulo cili mkati, Mdyelekezi anali ataika kale maganizo ofuna kupeleka Yesu mumtima mwa Yudasi Isikariyoti, mwana wa Simoni. 3 Conco Yesu podziwa kuti Atate wake anapeleka zinthu zonse m’manja mwake, ndiponso kuti anacokela kwa Mulungu komanso kuti anali kupita kwa Mulungu, 4 ananyamuka pa cakudya camadzuloco, ndipo anavula malaya ake akunja n’kuwaika pambali. Ndiyeno anatenga thaulo n’kulimanga m’ciuno mwake. 5 Atatelo, anaika madzi m’beseni n’kuyamba kusambika mapazi a ophunzila ake, ndi kuwapukuta ndi thaulo limene anamanga m’ciuno lija. 6 Kenako anafika pa Simoni Petulo. Iye anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, mufuna kusambika mapazi anga?” 7 Yesu anamuyankha kuti: “Zimene ndikucita sungazimvetse pakali pano, koma udzazimvetsa pambuyo pake.” 8 Petulo anamuuza kuti: “Koma sindilola m’pang’ono pomwe kuti musambike mapazi anga.” Yesu anamuyankha kuti: “Ngati sindikusambika, ulibe gawo kwa ine.” 9 Simoni Petulo anamuuza kuti: “Ambuye, musangosambika mapazi anga okha ayi, koma mundisambikenso manja ndi mutu womwe.” 10 Yesu anamuuza kuti: “Amene wasamba m’thupi amangofunika kusamba mapazi okha basi, cifukwa thupi lonse ndi loyela. Ndipo inu ndinu oyela, koma osati nonsenu.” 11 Iye anali kudziwa munthu amene anali kudzamupeleka. N’cifukwa cake anati: “Sikuti nonsenu ndinu oyela.”
12 Atatsiliza kuwasambika mapazi, n’kuvalanso malaya ake akunja, anakhalanso pathebulo n’kuwafunsa kuti: “Kodi mwadziwa cifukwa cake ndasambika mapazi anu? 13 Inu mumandichula kuti ‘Mphunzitsi’ komanso ‘Ambuye,’ ndipo mumalondola cifukwa ndinedi Mphunzitsi komanso Ambuye. 14 Conco, ngati ine Ambuye komanso Mphunzitsi ndasambika mapazi anu, inunso muyenela kusambikana mapazi wina ndi mnzake. 15 Cifukwa ndakupatsani citsanzo, kuti monga mmene ine ndacitila kwa inu, inunso muzicita cimodzimodzi. 16 Ndithudi ndikukuuzani, kapolo saposa mbuye wake, ndiponso wotumidwa saposa womutuma. 17 Ngati mumazidziwa zinthu zimenezi, mudzakhala acimwemwe mukamazicita. 18 Sindikunena nonsenu, ndidziwa amene ndawasankha. Koma zimenezi zacitika kuti lemba likwanilitsidwe, limene limati: ‘Amene anali kudya cakudya canga, wanyamula kadenene kake n’kundiukila.’* 19 Tsopano ndikukuuzani izi zisanacitike, kuti zikadzacitika mukakhulupilile kuti munthu uja munali kuyembekezela ndine. 20 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wolandila munthu wotumidwa ndi ine walandilanso ine, ndipo aliyense amene walandila ine, walandilanso iye amene anandituma.”
21 Atakamba zimenezi, Yesu anavutika mumzimu, ndipo anacitila umboni kuti: “Ndithudi ndikukuuzani, mmodzi wa inu andipeleka.” 22 Ophunzila ake anayamba kupenyanapenyana, cifukwa sanadziwe kuti iye anali kukamba ndani. 23 Mmodzi wa ophunzilawo, amene Yesu anali kumukonda, anali khale pafupi ndi Yesu.* 24 Ndiyeno Simoni Petulo anamugumulila mutu ameneyo n’kumuuza kuti: “Tiuze, akunena ndani.” 25 Wophunzilayo anatsamila pacifuwa ca Yesu n’kumufunsa kuti: “Ambuye, mukukamba ndani?” 26 Yesu anayankha kuti: “Ndi amene ndipatse cidutswa ca mkate cimene ndisunse.” Atasunsa cidutswaco anapatsa Yudasi, mwana wa Simoni Isikariyoti. 27 Yudasi atalandila cidutswa ca mkateco, Satana analowa mwa iye. Pamenepo Yesu anamuuza kuti: “Zimene ufuna kucita uzicite mwamsanga.” 28 Koma amene anali nawo pathebulopo sanadziwe cifukwa cimene anamuuzila zimenezi. 29 Ena anaganiza kuti, popeza Yudasi anali kusunga bokosi la ndalama, ndiye kuti Yesu anali kumuuza kuti, “Ugule zofunikila pacikondwelelo,” kapena ayenela kupeleka kenakake kwa osauka. 30 Conco Yudasi atalandila cidutswa ca mkateco, anatuluka panja nthawi yomweyo ndipo unali usiku.
31 Yudasi atatuluka, Yesu anati: “Tsopano Mwana wa munthu walemekezedwa, ndipo Mulungu walemekezedwa kudzela mwa iye. 32 Mulungu iye mwini amulemekeza, ndipo amulemekeza nthawi yomwe ino. 33 Inu anzanga apamtima, ndikhala nanu kwa kanthawi kocepa cabe. Mudzandifunafuna, ndipo monga ndinauzila Ayuda kuti, ‘Kumene ndidzapite, inu simudzakwanitsa kufikako,’ inunso ndikukuuzani zimenezi. 34 Ndikukupatsani lamulo latsopano kuti muzikondana, monga mmene ine ndakukondelani, inunso muzikondana cimodzimodzi. 35 Mukamakondana wina ndi mnzake, onse adzadziwa kuti ndinu ophunzila anga.”
36 Simoni Petulo anamufunsa kuti: “Ambuye, mukupita kuti?” Yesu anayankha kuti: “Kumene ndikupita, simungandilondole pali pano, koma mudzandilondola m’tsogolo.” 37 Petulo anamufunsanso kuti: “Ambuye, n’cifukwa ciyani sindingakulondoleni pali pano? Ine ndidzapeleka moyo wanga cifukwa ca inu.” 38 Yesu anayankha kuti: “Kodi udzapeleka moyo wako cifukwa ca ine? Ndithudi ndikukuuza, tambala asanalile, iwe undikana katatu.”
14 “Mitima yanu isavutike. Khulupililani Mulungu, ndipo khulupililaninso ine. 2 M’nyumba ya Atate wanga muli malo ambili okhalamo. Mukanakhala kuti mulibe, n’kanakuuzani. Conco ndikupita kukakukonzelani malo. 3 Komanso ndikapita kukakukonzelani malo, ndidzabwelanso kudzakutengani n’kupita nanu, kuti kumene ine ndikakhale inunso mukakhale komweko. 4 Ndipo njila ya kumene ine ndikupita, inu muidziwa.”
5 Thomasi anamufunsa kuti: “Ambuye, kumene inu mukupita sitidziwako. Ndiye njilayo tingaidziwe bwanji?”
6 Yesu anamuyankha kuti: “Ine ndine njila, coonadi, ndi moyo. Palibe amene angafike kwa Atate akapanda kudzela mwa ine. 7 Anthu inu mukanandidziwa ine, mukanawadziwanso Atate wanga. Kuyambila tsopano kupita m’tsogolo mwawadziwa, ndipo mwawaona kale.”
8 Filipo anamuuza kuti: “Ambuye, tionetseni Atatewo, ndipo mukatelo tikhutila.”
9 Yesu anamuuza kuti: “Ngakhale kuti anthu inu ndakhala nanu kwa nthawi yaitali yonseyi, Filipo, kodi sunandidziwebe? Amene waona ine waonanso Atate. Nanga n’cifukwa ciyani ukuti ‘Tionetseni Atate’? 10 Kodi sukhulupilila kuti ine ndi Atate ndife ogwilizana? Zimene ndimakuuzani si za m’maganizo mwanga ayi, koma Atate amene akhalabe ogwilizana nane, akucita nchito zawo. 11 Khulupilila kuti ine ndi Atate ndife ogwilizana. Apo ayi, khulupilila cifukwa ca nchitozo. 12 Ndithudi ndikukuuzani, aliyense wondikhulupilila adzacitanso nchito zimene ine ndimacita. Ndipo adzacita nchito zazikulu kuposa zimenezi cifukwa ine ndikupita kwa Atate. 13 Komanso ciliconse cimene mudzapempha m’dzina langa ine ndidzacicita, kuti Atate alemekezedwe kupitila mwa Mwana wake. 14 Mukapempha ciliconse m’dzina langa, ine ndidzacicita.
15 “Ngati mumandikonda, mudzasunga malamulo anga. 16 Ndidzapempha Atate, ndipo iwo adzakupatsani mthandizi* wina amene adzakhala nanu kwamuyaya. 17 Mthandiziyo ndi mzimu wa coonadi, umene dzikoli silingaulandile, cifukwa siliuona kapena kuudziwa. Inu mumaudziwa cifukwa uli mwa inu ndipo umakhala mwa inu. 18 Sindidzakusiyani mukulila,* ndidzabwela kwa inu. 19 Posacedwapa dziko silidzandionanso. Koma inu mudzandiona cifukwa ndili ndi moyo, ndiponso inu mudzakhala ndi moyo. 20 Pa tsiku limenelo mudzadziwa kuti ine ndi Atate ndife ogwilizana, komanso kuti inu ndi ine ndife ogwilizana. 21 Aliyense amene ali ndi malamulo anga ndipo amawatsatila, ndi amene amandikonda. Komanso aliyense amene amandikonda, Atate wanganso adzamukonda. Inenso ndidzamukonda, ndipo ndidzadzionetsa bwinobwino kwa iye.”
22 Yudasi, koma osati Isikariyoti, anamufunsa kuti: “Ambuye, n’cifukwa ciyani mukufuna kudzionetsa bwinobwino kwa ife osati kudzikoli?”
23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati munthu amandikonda adzasunga mawu anga, ndipo Atate wanga adzamukonda, komanso tidzapita kwa iwo n’kuyamba kukhala nawo. 24 Amene sandikonda sasunga mawu anga. Mawu amene mukuwamvawa si anga ayi, koma ndi a Atate amene anandituma.
25 “Ndakuuzani zinthu zimenezi pamene ndikali nanu. 26 Koma mthandiziyo, amene ndi mzimu woyela umene Atate adzatumiza m’dzina langa, ameneyo adzakuphunzitsani zinthu zonse, ndi kukukumbutsani zonse zimene ndinakuuzani. 27 Ndikusiyilani mtendele, ndipo ndikupatsani mtendele wanga. Sindikupatsani mtendelewo mmene dziko limakupatsilani ayi. Mitima yanu isavutike kapena kucita mantha. 28 Mwamva kuti ndakuuzani kuti, ‘Ndikupita ndipo ndidzabwelanso kwa inu.’ Ngati mumandikonda, mukanakondwela kuti ndikupita kwa Atate, cifukwa Atate ndi wamkulu kuposa ine. 29 Conco ndakuuzani tsopano zimenezi zisanacitike, kuti zikadzacitika mukakhulupilile. 30 Sindikamba nanu zambili cifukwa wolamulila wa dzikoli akubwela, ndipo iye alibe mphamvu pa ine. 31 Koma kuti dziko lidziwe kuti ndimawakonda Atate, ndikucita ndendende zimene Atatewo anandilamula. Nyamukani, tiyeni ticokeko kuno.
15 “Ine ndine mtengo wampesa weniweni ndipo Atate ndi mlimi. 2 Iye adzadula nthambi iliyonse mwa ine imene sibala zipatso, ndipo adzayeletsa nthambi iliyonse yobala zipatso mwa kuitengulila* kuti ibale zipatso zoculuka. 3 Inu ndinu oyela kale cifukwa ca mawu amene ndakuuzani. 4 Khalanibe ogwilizana ndi ine, ndipo inenso ndidzakhalabe wogwilizana ndi inu. Nthambi singabale zipatso payokha, ngati siyolumikizika kumtengo wampesa. Mofananamo, inunso simungabale zipatso ngati simukhalabe ogwilizana ndi ine. 5 Ine ndine mtengo wampesa, ndipo inu ndinu nthambi zake. Aliyense wogwilizana ndi ine, inenso ndidzagwilizana naye, ndipo adzabala zipatso zambili cifukwa popanda ine palibe ciliconse cimene mungacite. 6 Ngati munthu sakhalabe wogwilizana ndi ine, ali ngati nthambi yodulidwa imene imauma. Anthu amasonkhanitsa nthambizo n’kuziponya pamoto, ndipo zimapsa. 7 Ngati mukhalabe ogwilizana ndi ine, komanso ngati mawu anga akhalabe mwa inu, mungapemphe ciliconse cimene mufuna ndipo cidzacitika. 8 Atate amalemekezeka ngati mupitiliza kubala zipatso zambili ndi kuonetsa kuti ndinu ophunzila anga. 9 Monga mmene Atate amandikondela, inenso ndimakukondani. Khalanibe m’cikondi canga. 10 Mukamasunga malamulo anga, mudzakhalabe m’cikondi canga, monga mmene inenso ndasungila malamulo a Atate wanga ndi kukhalabe m’cikondi cake.
11 “Ndakuuzani zinthu zimenezi kuti cimwemwe canga cikhale mwa inu, komanso kuti cimwemwe canu cisefukile. 12 Lamulo langa n’lakuti muzikondana wina ndi mnzake mmenenso ine ndimakukondelani. 13 Palibe munthu amene ali ndi cikondi cacikulu kuposa ca munthu amene wapeleka moyo wake cifukwa ca mabwenzi ake. 14 Mukhala mabwenzi anga mukamacita zimene ndimakulamulani. 15 Sindikukuchulaninso kuti akapolo, cifukwa kapolo sadziwa zimene mbuye wake akucita. Koma ndakuchulani kuti mabwenzi, cifukwa ndakuuzani zonse zimene ndinamva kwa Atate wanga. 16 Si ndinu amene munandisankha, koma ine ndinakusankhani. Ndinakusankhani kuti mupitilize kubala zipatso, komanso kuti zipatso zanu zisathe, kuti ciliconse cimene mungapemphe Atate m’dzina langa akupatseni.
17 “Ndikukulamulani zimenezi n’colinga cakuti muzikondana wina ndi mnzake. 18 Ngati dziko limadana nanu, dziwani kuti linadana ndi ine lisanadane ndi inu. 19 Mukanakhala a dzikoli, dzikoli likanakukondani monga akeake. Tsopano simuli a dziko, koma ine ndakusankhani kucokela m’dzikoli, n’cifukwa cake dzikoli limadana nanu. 20 Muzikumbukila mawu amene ndinakuuzani akuti: Kapolo saposa mbuye wake. Ngati iwo azunza ine, inunso adzakuzunzani. Ngati asunga mawu anga, adzasunganso mawu anu. 21 Koma iwo adzakucitilani zinthu zonsezi cifukwa ca dzina langa, popeza samudziwa amene anandituma. 22 Ndikanapanda kubwela n’kulankhula nawo, akanakhala opanda chimo. Koma tsopano alibe cifukwa cokanila chimo lawo. 23 Amene amadana ndi ine, amadananso ndi Atate wanga. 24 Ndikanapanda kucita nchito pakati pawo zimene palibe munthu aliyense akanazicita, iwo akanakhala opanda chimo. Koma tsopano andiona ndipo adana nane, komanso adana ndi Atate wanga. 25 Koma zimenezi zacitika kuti mawu olembedwa m’Cilamulo cawo akwanilitsidwe, akuti: ‘Anadana nane popanda cifukwa.’ 26 Mthandizi amene ndidzakutumizilani kucokela kwa Atate akadzabwela, amene ndi mzimu wa coonadi wocokela kwa Atate, ameneyo adzacitila umboni, 27 ndipo inunso mudzandicitila umboni, cifukwa mwakhala nane kucokela paciyambi.
16 “Ndakuuzani zinthu zimenezi kuti musataye* cikhulupililo canu. 2 Anthu adzakucotsani m’sunagoge. Ndipo nthawi idzafika pamene aliyense amene adzakuphani adzaganiza kuti wacita utumiki wopatulika kwa Mulungu. 3 Koma adzacita zinthu zimenezi cifukwa Atate sawadziwa komanso ine sandidziwa. 4 Komabe, ndakuuzani zinthu zimenezi kuti nthawi yakuti zicitike ikadzafika, mukakumbukile kuti ndinakuuzani.
“Poyamba sindinakuuzeni zinthu zimenezi cifukwa ndinali nanu. 5 Tsopano ndikupita kwa amene anandituma, koma palibe ngakhale mmodzi wa inu amene wandifunsa kuti, ‘Mukupita kuti?’ 6 Koma cifukwa ndakuuzani zinthu zimenezi, mitima yanu yadzala ndi cisoni. 7 Kukuuzani zoona, kupita kwanga kudzakupindulilani. Cifukwa ngati sindingapite, mthandizi uja sadzabwela kwa inu. Koma ndikapita ndidzamutumiza kwa inu. 8 Ndipo iye akadzabwela, adzapeleka umboni wokhutilitsa kudzikoli wonena za ucimo, cilungamo, komanso ciweluzo. 9 Coyamba adzapeleka umboni wokamba za ucimo, cifukwa iwo sakundikhulupilila. 10 Kenako adzapeleka umboni wokamba za cilungamo, cifukwa ndikupita kwa Atate ndipo inu simudzandionanso. 11 Pamapeto pake, adzapeleka umboni wokamba za ciweluzo, cifukwa wolamulila wa dzikoli waweluzidwa.
12 “Ndikali ndi zambili zakuti ndikuuzeni, koma simungazimvetse pali pano. 13 Koma mthandiziyo akadzabwela, amene ndi mzimu wa coonadi, adzakutsogolelani m’coonadi conse. Pakuti iye sadzalankhula zongoganiza pa iye yekha, koma adzalankhula zimene wamva ndipo adzalengeza kwa inu zinthu zimene zidzabwela. 14 Ameneyo adzandilemekeza, cifukwa adzalengeza kwa inu zimene adzalandila kucokela kwa ine. 15 Zinthu zonse zimene Atate ali nazo ndi zanga. Ndiye cifukwa cake ndanena kuti mthandiziyo adzalengeza zimene walandila kucokela kwa ine. 16 Kwa kanthawi kocepa simudzanionanso, ndipo kwa kanthawi kocepa mudzandiona.”
17 Atakamba zimenezi, ena mwa ophunzila ake anayamba kufunsana kuti: “Kodi watanthauzanji potiuza kuti, ‘Kwa kanthawi kocepa simudzandionanso, ndipo kwa kanthawi kocepa mudzandiona,’ komanso kuti, ‘cifukwa ndikupita kwa Atate’?” 18 Iwo anali kukamba kuti: “Kodi akutanthauza ciyani ponena kuti, ‘kwa kanthawi kocepa’? Sitikumvetsa zimene akukamba.” 19 Yesu anadziwa kuti iwo anali kufuna kumufunsa. Conco anawauza kuti: “Kodi mukufunsana zimenezi cifukwa ndakamba kuti: ‘Kwa kanthawi kocepa simudzandionanso, ndipo kwa kanthawi kocepa mudzandiona’? 20 Ndithudi ndikukuuzani, inu mudzalila ndi kubuma,* koma dzikoli lidzakondwela. Mudzamva cisoni, koma cisoni canu cidzasanduka cimwemwe. 21 Mkazi pobeleka amavutika kwambili cifukwa nthawi yake yakwana. Koma akabeleka mwana, amaiwala zopwetekazo cifukwa ca cimwemwe cakuti munthu wabadwa padziko lapansi. 22 Cimodzimodzi inunso, pali pano muli ndi cisoni, koma ndidzakuonaninso ndipo mitima yanu idzakondwela. Palibenso amene adzakulandani cimwemwe canuco. 23 Patsiku limenelo simudzandifunsanso funso lililonse. Ndithudi ndikukuuzani, ngati mungapemphe ciliconse kwa Atate m’dzina langa adzakupatsani. 24 Mpaka pano simunapemphepo ciliconse m’dzina langa. Pemphani ndipo mudzalandila kuti cimwemwe canu cisefukile.
25 “Ndakuuzani zinthu zimenezi m’mafanizo. Nthawi ikubwela pamene sindidzalankhulanso nanu m’mafanizo, koma ndidzakuuzani momveka bwino za Atate. 26 Patsikulo mudzapempha cinthu kwa Atate m’dzina langa. Pokamba izi, sinditanthauza kuti ndidzakupemphelani ayi. 27 Atatewo amakukondani, cifukwa munandikonda, ndipo munakhulupilila kuti ndinabwela monga woimilako Mulungu. 28 Ndinabwela m’dzikoli monga woimilako Atate wanga. Tsopano ndikucoka m’dzikoli, ndipo ndikupita kwa Atate.”
29 Ophunzila ake anati: “Ambuye, tsopano mukulankhula zomveka bwino cifukwa simukugwilitsa nchito mafanizo. 30 Tsopano tadziwa kuti mumadziwa zinthu zonse, ndipo m’posafunikilanso kuti wina akufunseni mafunso. Mwa ici, tikukhulupilila kuti munacokela kwa Mulungu.” 31 Yesu anawafunsa kuti: “Kodi mwakhulupilila tsopano? 32 Taonani! Nthawi ikubwela, ndipo yafika kale, pamene nonse mudzabalalika aliyense kupita kunyumba kwake, ndipo mudzandisiya ndekha. Koma sindili ndekha, cifukwa Atate ali nane. 33 Ndakuuzani zinthu zimenezi, kuti kudzela mwa ine mukhale ndi mtendele. M’dzikoli mudzakumana ndi masautso, koma limbani mtima! Ine ndaligonjetsa dziko.”
17 Yesu atakamba zinthu zimenezi, anakweza maso ake kumwamba n’kunena kuti: “Atate, nthawi yafika tsopano. Lemekezani mwana wanu kuti mwana wanuyo akulemekezeni, 2 monga mmene mwamupatsila ulamulilo pa anthu onse kuti iye apeleke moyo wosatha kwa onse amene munamupatsa. 3 Iwo adzapeza moyo wosatha akamadziwa za inu* Mulungu yekhayo woona, komanso za Yesu Khristu amene inu munamutuma. 4 Ndakulemekezani pa dziko lapansi, cifukwa cakuti ndatsiliza nchito imene munandipatsa. 5 Tsopano Atate, ndiloleni ndikhale pambali panu, ndipo mundipatse ulemelelo umene ndinali nawo pambali panu dziko lisanakhalepo.
6 “Anthu amene munandipatsa kucokela m’dzikoli ndawadziwitsa dzina lanu. Anali anu, koma munawapeleka kwa ine, ndipo iwo asunga* mawu anu. 7 Zonse zimene munandipatsa n’zocokela kwa inu, 8 cifukwa ndawapatsa mawu amene inu munandipatsa. Iwo awalandila, ndipo adziwadi kuti ndinabwela monga wokuimilani, ndipo akhulupilila kuti ndinu munandituma. 9 Conco ndikuwapemphelela. Sindikupemphelela dzikoli, koma aja amene inu munandipatsa cifukwa ndi anu. 10 Zinthu zanga zonse ndi zanu, ndipo zanu ndi zanga. Ine ndalemekezeka pakati pawo.
11 “Ine ndikucoka m’dzikoli, koma iwo akali m’dzikoli, ndipo ine ndikubwela kwa inu. Atate woyela, ayang’anileni cifukwa ca dzina lanu limene munandipatsa, kuti akhale amodzi* mmenenso inu ndi ine tilili amodzi.* 12 Pamene ndinali nawo, ndinali kuwayang’anila cifukwa ca dzina lanu limene munandipatsa. Ine ndawateteza, ndipo palibe ngakhale mmodzi amene wawonongeka kupatulapo mwana wa ciwonongeko, kuti lemba likwanilitsidwe. 13 Koma tsopano ndikubwela kwa inu, ndipo ndikukamba zimenezi m’dzikoli kuti akhale ndi cimwemwe cosefukila ngati cimene ine ndili naco. 14 Ndawapatsa mawu anu, koma dzikoli limadana nawo, cifukwa iwo sali a dzikoli, mmenenso ine sindili wa dzikoli.
15 “Sindikupempha kuti muwacotse m’dzikoli, koma kuti muwayang’anile cifukwa ca woipayo. 16 Iwo sali a dzikoli mmenenso ine sindili wa dzikoli. 17 Ayeletseni* ndi coonadi, mawu anu ndiwo coonadi. 18 Monga mmene inu munanditumizila m’dziko, inenso ndawatumiza m’dziko. 19 Ndipo ine ndikudziyeletsa cifukwa ca iwo, kuti nawonso ayeletsedwe ndi coonadi.
20 “Sindikupemphelela awa okha ayi, koma ndikupemphelelanso aliyense amene amakhulupilila mwa ine pambuyo pomvetsela zimene iwo amaphunzitsa. 21 Ndikucita izi kuti onsewo akhale amodzi monga mmene ine ndi inu Atate tilili ogwilizana, kuti nawonso akhale ogwilizana ndi ife, n’colinga coti dzikoli likhulupilile kuti ndinu munandituma. 22 Ine ndawapatsa ulemelelo umene munandipatsa kuti akhale amodzi, mmenenso ife tilili amodzi. 23 Ine ndikhale wogwilizana ndi iwo, ndipo inu mukhale wogwilizana ndi ine, n’colinga coti iwo akhale ogwilizana kwambili, kuti dziko lidziwe kuti ndinu munandituma, komanso kuti mumawakonda mmene inu mumandikondela. 24 Atate, ndikufuna kuti amene mwandipatsa akakhale kumene ine ndidzakhala, kuti iwo akaone ulemelelo umene inu mwandipatsa, cifukwa munandikonda dziko lisanakhalepo. 25 Atate Wolungama, dzikoli silikudziwani ayi, koma ine ndimakudziwani, ndipo iwowa afika podziwa kuti ndinu munandituma. 26 Ndawadziwitsa dzina lanu, ndipo ndidzapitiliza kuwadziwitsa dzinalo, kuti iwo azionetsa cikondi ngati cimene inu munandionetsa, kuti inenso ndikhale wogwilizana nawo.”
18 Yesu atakamba zimenezi, anatuluka pamodzi ndi ophunzila ake n’kuwoloka cigwa ca Kidironi kupita kumene kunali munda winawake. Ndipo iye pamodzi ndi ophunzila ake analowa m’mundawo. 2 Yudasi womupeleka uja, nayenso anali kudziwako kumalo amenewo, cifukwa nthawi zambili Yesu anali kukumana ndi ophunzila ake kumeneko. 3 Conco Yudasi anabwela ndi gulu la asilikali pamodzi ndi alonda ocokela kwa ansembe aakulu ndi Afarisi. Iwo anabwela atanyamula miyuni, nyale, ndi zida. 4 Ndiye popeza Yesu anali kudziwa zonse zimene zimucitikile, anawayandikila n’kuwafunsa kuti: “Kodi mukufuna ndani?” 5 Iwo anamuyankha kuti: “Yesu Mnazareti.” Iye anawauza kuti: “Ndine.” Ndipo Yudasi womupeleka uja anali nawo limodzi.
6 Koma Yesu atawauza kuti, “Ndine,” iwo anabwelela m’mbuyo n’kugwa pansi. 7 Ndiyeno iye anawafunsanso kuti: “Kodi mukufuna ndani?” Iwo anati: “Yesu Mnazareti.” 8 Yesu anayankha kuti: “Ndakuuzani kale kuti ndine. Conco ngati mukufuna ine, alekeni awa azipita.” 9 Izi zinacitika kuti mawu amene iye anakamba akwanilitsidwe, akuti: “Pa anthu amene munandipatsa, sindinatayepo ngakhale mmodzi.”
10 Ndiyeno Simoni Petulo, amene anali ndi lupanga, analisolola n’kutema nalo kapolo wa mkulu wa ansembe mpaka kumudula khutu la kudzanja lamanja. Kapoloyo dzina lake anali Makasi. 11 Koma Yesu anauza Petulo kuti: “Bweza lupangalo m’cimake. Kodi sindiyenela kumwa za m’kapu zimene Atate andipatsa?”
12 Kenako asilikaliwo, mkulu wa asilikali, komanso alonda a Ayuda, anagwila Yesu n’kumumanga manja. 13 Iwo coyamba anapita naye kwa Anasi, cifukwa anali mpongozi wa Kayafa, amene anali mkulu wa ansembe m’cakaco. 14 Kayafa ameneyu ndi amene analangiza Ayudawo kuti zinali zowapindulila kuti munthu mmodzi afele anthu onse.
15 Tsopano Simoni Petulo ndi wophunzila wina anali kulondola Yesu. Wophunzilayo anali wodziwika kwa mkulu wa ansembe uja, ndipo iye pamodzi ndi Yesu analowa m’bwalo la nyumba ya mkulu wa ansembeyo. 16 Koma Petulo anaimilila pakhomo* panja. Conco wophunzila winayo amene mkulu wa ansembe uja anali kumudziwa, anatuluka n’kukakamba ndi mlonda wapakhomo n’kulowetsa Petulo. 17 Ndiyeno mtsikana wanchito amene anali mlonda pakhomopo anafunsa Petulo kuti: “Kodi inunso sindinu mmodzi wa ophunzila a munthu uyu?” Iye anati: “Ayi sindine.” 18 Ndiyeno atumiki ndi alonda anaimilila akuwotha moto wamalasha umene anayatsa cifukwa kunali kozizila. Nayenso Petulo anaimilila nawo pamodzi akuwotha motowo.
19 Conco wansembe wamkulu anafunsa Yesu za ophunzila ake, komanso zimene iye anali kuphunzitsa. 20 Yesu anayankha kuti: “Ndalankhula poyela ku dzikoli. Nthawi zonse ndinali kuphunzitsa m’masunagoge ndi m’kacisi mmene Ayuda onse anali kusonkhana pamodzi, ndipo ine sindinalankhulepo ciliconse mobisa. 21 Ndiye n’cifukwa ciyani mukufunsa ine? Funsani amene anamva zimene ndinali kuwauza. Onani! Anthuwa akudziwa zimene ndinanena.” 22 Yesu atakamba izi, mmodzi wa alonda amene anaimilila naye pafupi, anamuwaza mbama kumaso n’kunena kuti: “Kodi umu ndi mmene ungayankhile wansembe wamkulu?” 23 Yesu anamuyankha kuti: “Ngati ndakamba colakwika, peleka* umboni wa colakwikaco. Koma ngati ndakamba zoona, n’cifukwa ciyani wandimenya?” 24 Ndiyeno Anasi anatumiza Yesu kwa Kayafa mkulu wa ansembe atam’manga manja.
25 Tsopano Simoni Petulo anali cilili akuwotha moto pamenepo. Ndiyeno iwo anamufunsa kuti: “Kodi inunso si ndinu mmodzi wa ophunzila ake?” Iye anakana ndipo anati: “Ayi si ndine.” 26 Mmodzi wa akapolo a mkulu wa nsembe uja, yemwe anali wacibale wa munthu amene Petulo anamudula khutu, anati: “Ndinakuona uli naye m’munda muja, ndi bodza?” 27 Petulo anakananso, ndipo nthawi yomweyo tambala analila.
28 Kenako iwo anamutenga Yesu kwa Kayafa n’kupita naye kunyumba kwa bwanamkubwa. Apa kunali m’mamawa kwambili. Koma iwo sanalowe m’nyumba ya bwanamkubwayo poopa kuti angadetsedwe, cifukwa anali kufuna kudya Pasika. 29 Conco Pilato anatuluka panja n’kuwafunsa kuti: “Kodi munthuyu mwamubweletsa kuno pa mlandu wanji?” 30 Iwo anamuyankha kuti: “Munthu uyu akanakhala kuti sanalakwe,* sitikanamubweletsa kwa inu.” 31 Pilato anawauza kuti: “M’tengeni mukamuweluze nokha malinga ndi malamulo anu.” Ayudawo anamuuza kuti: “Ife tilibe ulamulilo wopha munthu aliyense.” 32 Izi zinakwanilitsa mawu amene Yesu anakamba oonetsa mmene adzafele pakangopita nthawi yocepa.
33 Conco Pilato analowanso m’nyumba ya bwanamkubwayo, ndipo anaitana Yesu n’kumufunsa kuti: “Kodi ndiwe Mfumu ya Ayuda?” 34 Yesu anayankha kuti: “Kodi mukufunsa zimenezi cifukwa mwangoganiza nokha, kapena cifukwa cakuti ena akuuzani za ine?” 35 Pilato anayankha kuti: “Ine sindine Myuda. Anthu a mtundu wako komanso ansembe aakulu ndiwo akupeleka kwa ine. Kodi unacita ciyani?” 36 Yesu anayankha kuti: “Ufumu wanga si wa m’dzikoli. Ufumu wanga ukanakhala wa m’dzikoli, atumiki anga akanamenya nkhondo kuti ndisapelekedwe kwa Ayuda. Koma mmene zililimu, Ufumu wanga si wocokela m’dzikoli.” 37 Ndiyeno Pilato anamufunsa kuti: “Cabwino, ndiye kodi ndiwe mfumu?” Yesu anayankha kuti: “Mukunena nokha kuti ndine mfumu. Ici n’cimene ndinabadwila komanso n’cimene ndinabwelela m’dziko, kuti ndidzacitile umboni coonadi. Aliyense amene ali kumbali ya coonadi amamvela mawu anga.” 38 Pilato anamufunsa kuti: “Kodi coonadi n’ciyani?”
Atakamba zimenezi, anatulukanso panja n’kupita kwa Ayuda, ndipo anawauza kuti: “Munthu uyu sindikum’peza ndi mlandu uliwonse. 39 Paja inu mumafuna kuti nthawi zonse pacikondwelelo ca Pasika ndizikumasulilani munthu mmodzi. Ndiye kodi mufuna ndikumasulileni Mfumu ya Ayuda?” 40 Iwo anafuulanso kuti: “Osati munthu uyu, koma Baraba!” Barabayo anali wacifwamba.
19 Kenako Pilato anatenga Yesu n’kumukwapula. 2 Ndipo asilikali analuka cisoti cacifumu caminga n’kumuveka kumutu. Anamuvekanso mkanjo wa mtundu wapepo. 3 Iwo anali kupita kwa iye n’kumakamba kuti: “Moni,* inu Mfumu ya Ayuda!” Analinso kumuwaza mambama kumaso. 4 Pilato anapitanso panja n’kuwauza kuti: “Onani! Ine ndamubweletsa panja kwa inu kuti mudziwe kuti sindinamupeze ndi mlandu uliwonse.” 5 Conco Yesu anatuluka panja atavala cisoti cacifumu caminga cija, ndi mkanjo wa mtundu wapepo. Kenako Pilato anawauza kuti: “Onani! Munthu uja ndi uyu!” 6 Koma pamene ansembe aakulu ndi alonda anamuona, anafuula kuti: “Apacikidwe! Apacikidwe ndithu!”* Pilato anawauza kuti: “Mutengeni inuyo mukamuphe nokha,* cifukwa ine sindikumupeza ndi mlandu uliwonse.” 7 Ayudawo anamuyankha kuti: “Ife tili ndi malamulo. Malinga ndi malamulowo, iye ayenela kufa cifukwa anali kunena kuti ndi mwana wa Mulungu.”
8 Pilato atamva zimene iwo anali kukamba, anacita mantha kwambili, 9 ndipo iye analowanso m’nyumba ya bwanamkubwa ndi kufunsa Yesu kuti: “Kodi unacokela kuti?” Koma Yesu sanamuyankhe ciliconse. 10 Conco Pilato anamufunsa kuti: “Kodi sufuna kukamba ndi ine? Kodi sudziwa kuti ndili ndi mphamvu zokumasula komanso mphamvu zokupha?”* 11 Yesu anamuyankha kuti: “Simukanakhala ndi mphamvu pa ine ngakhale pang’ono ngati simunapatsidwe mphamvuzo kucokela kumwamba. Ndiye cifukwa cake munthu amene anandipeleka kwa inu ali ndi chimo lalikulu zedi.”
12 Pa cifukwa cimeneci, Pilato anayamba kuyesayesa kupeza njila yakuti amumasule, koma Ayudawo anafuula kuti: “Mukam’masula munthu uyu, ndiye kuti sindinu bwenzi la Kaisara. Aliyense wodzipanga kukhala mfumu amatsutsana ndi Kaisara.” 13 Ndiyeno Pilato atamva mawu amenewa, anatulutsa Yesu panja, ndipo anakhala pampando woweluzila milandu pa malo ochedwa Bwalo la Miyala, koma mu Ciheberi amachedwa, Gab′ba·tha. 14 Tsopano linali tsiku la Cikonzekelo ca Pasika, ndipo nthawi inali ca m’ma 12 koloko masana.* Pilato anauza Ayudawo kuti: “Onani! Mfumu yanu iyi!” 15 Koma iwo anafuula kuti: “Anyongedwe! Anyongedwe! Apacikidwe ndithu ameneyo!”* Ndiyeno Pilato anawafunsa kuti: “Kodi mufuna ndiphe mfumu yanu?” Ansembe aakulu anayankha kuti: “Ife tilibe mfumu ina koma Kaisara.” 16 Kenako anamupeleka kwa iwo kuti akaphedwe pamtengo.
Conco Yesu anakhala m’manja mwawo. 17 Atadzinyamulila yekha mtengo wozunzikilapo,* anatuluka n’kupita kumalo ochedwa Cibade, amene m’Ciheberi anali kuchedwa Gologota. 18 Kumeneko anamukhomelela pamtengo pamodzi ndi amuna ena awili, wina kumbali iyi, wina kumbali inayi. Ndipo Yesu anali pakati. 19 Nayenso Pilato analemba dzina laudindo n’kuliika pamtengo wozunzikilapowo.* Analembapo kuti: “Uyu ndi Yesu Mnazareti, Mfumu ya Ayuda.” 20 Ayuda ambili anawelenga mawuwo, cifukwa kumene Yesu anamukhomelela pamtengo kunali kufupi ndi mzinda, ndipo mawuwo analembedwa m’Ciheberi, m’Cilatini, ndi m’Cigiriki. 21 Koma ansembe aakulu a Ayuda anauza Pilato kuti: “Musalembe kuti, ‘Mfumu ya Ayuda,’ koma kuti iye anati, ‘Ndine Mfumu ya Ayuda.’” 22 Pilato anawayankha kuti: “Zimene ndalemba, ndalemba.”
23 Asilikaliwo atamukhomelela Yesu pa mtengo, anatenga zovala zake zakunja n’kuzigawa panayi, ndipo msilikali aliyense anatengako mbali imodzi. Iwo anatenganso covala camkati. Koma covala camkatico cinalibe msoko. Cinali nsalu imodzi kucokela pamwamba mpaka pansi. 24 Conco asilikaliwo anauzana kuti: “Tisacing’ambe covalaci, m’malo mwake tiyeni ticite maele kuti tidziwe amene angacitenge.” Izi zinacitika kuti lemba likwanilitsidwe limene limati: “Iwo adzagawana zovala zanga, ndipo adzacita maele pa covala canga.” Ndipo asilikaliwo anacitadi zimenezi.
25 Koma pafupi ndi mtengo wozunzikilapo wa Yesu, panaimilila amayi ake ndi m’bale wawo, Mariya mkazi wa Kulopa, komanso Mariya Mmagadala. 26 Yesu ataona amayi ake komanso wophunzila uja amene anali kumukonda ataimilila pafupi, anauza amayi akewo kuti: “Mayi, kuyambila lelo, uyu ndi mwana wanu.” 27 Anauzanso wophunzila uja kuti: “Kuyambila lelo, awa ndi mayi ako.” Ndipo kuyambila nthawiyo wophunzilayo anatenga mayiwo n’kupita nawo kunyumba kwake.
28 Pambuyo pa izi, Yesu atadziwa kuti zonse zacitika, kuti malemba akwanilitsidwe, ananena kuti: “Ndamva ludzu.” 29 Pamalopo panali mtsuko wodzala ndi vinyo wowawasa. Conco iwo anaviika siponji mu vinyo wowawasayo, ndipo anaisomeka ku kamtengo ka hisope, kenako anakanyamula kamtengoko n’kukafikitsa pakamwa pa Yesu. 30 Yesu atalandila vinyo wowawasayo, anati: “Zakwanilitsidwa!” Ndipo atawelamitsa mutu, anapeleka mzimu wake.*
31 Limeneli linali tsiku la Cikonzekelo. Conco Ayuda sanafune kuti mitemboyo ikhalebe pamitengo yozunzikilapo pa tsiku la Sabata (cifukwa Sabatalo linali lalikulu). Cotelo Ayudawo anapempha Pilato kuti awalole kukawathyola miyendo ndi kucotsa mitembo yawo. 32 Ndiyeno asilikali anabwela n’kuthyola miyendo ya munthu woyamba, komanso ya munthu winayo amene anapacikidwa pambali pake. 33 Koma atafika pa Yesu anapeza kuti wafa kale, conco iwo sanathyole miyendo yake. 34 Koma mmodzi wa asilikaliwo analasa Yesu m’nthiti ndi mkondo, ndipo nthawi yomweyo magazi ndi madzi anatuluka. 35 Munthu amene anaona zimenezo anacitila umboni, ndipo umboni wake ndi woona. Iye akudziwa kuti zimene amakamba ndi zoona, kuti inu mukhulupilile. 36 Ndipo izi zinacitika kuti lemba likwanilitsidwe limene limati: “Sadzathyoledwa fupa ngakhale limodzi.”* 37 Komanso lemba lina limati: “Iwo adzayang’ana kwa munthu amene anamulasa.”
38 Pambuyo pa zinthu zimenezi, Yosefe wa ku Arimateya, amene anali wophunzila wa Yesu wamseli cifukwa coopa Ayuda, anapempha Pilato kuti akacotse mtembo wa Yesu, ndipo Pilatoyo anamulola. Conco iye anabwela n’kutenga mtembowo. 39 Nikodemo, munthu amene anapita kwa Yesu usiku nthawi yoyamba, nayenso anabwela atanyamula mule wosakaniza ndi aloye, wolemela makilogalamu pafupifupi 32.7. 40 Conco iwo anatenga mtembo wa Yesu n’kuukulunga mu nsalu zamalilo zonunkhila, malinga ndi mwambo wa Ayuda woika malilo. 41 Kumene anamuphela* kunali munda, ndipo m’mundamo munali manda* atsopano omwe munali musanaikidwepo munthu cikhalile. 42 Popeza linali tsiku la Cikonzekelo ca Ayuda, komanso poti mandawo anali pafupi, iwo anaika Yesu mmenemo.
20 Pa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya Mmagadala anapita kumanda* kuja m’mamawa kukali mdima, ndipo anaona kuti cimwala cija cacotsedwa kale pamandapo.* 2 Conco iye anathamangila kwa Simoni Petulo, komanso kwa wophunzila wina uja amene Yesu anali kumukonda kwambili, ndipo anawauza kuti: “Ambuye awacotsa m’manda muja, ndipo sitidziwa kumene awaika.”
3 Pamenepo Petulo ndi wophunzila winayo ananyamuka kupita kumandako. 4 Ndiyeno awiliwo anayamba kuthamanga pamodzi, koma wophunzila winayo anathamanga kwambili kuposa Petulo, moti anayambilila kufika kumandako. 5 Atasuzila mkati, anaona nsalu zili pansi, koma sanalowemo. 6 Kenako Simoni Petulo amene anali kubwela m’mbuyo mwake nayenso anafika, ndipo analowa m’mandamo. Iye anaona nsalu zili pansi mmenemo. 7 Nsalu imene anamukulungila kumutu sinali pamodzi ndi nsalu zina, koma inali yopetekapeteka payokha. 8 Wophunzila winayo amene anayambilila kufika kumanda kuja nayenso analowa mkati. Ndipo ataona, anakhulupilila zimene anauzidwa. 9 Panthawiyo, iwo anali asanamvetse zimene lemba limanena, kuti Yesu ayenela kuuka kwa akufa. 10 Conco ophunzilawo anabwelela kunyumba zawo.
11 Koma Mariya anaimililabe panja pafupi ndi mandawo akulila. Pamene anali kulila, anawelama kuti aone m’mandamo. 12 Ndipo anaona angelo awili amene anavala zovala zoyela atakhala pomwe mtembo wa Yesu unagona. Wina anakhala pansi kumutu, ndipo winayo anakhala kumiyendo. 13 Iwo anamufunsa kuti: “Mayi, n’cifukwa ciyani mukulila?” Iye anayankha kuti: “Ambuye wanga atengedwa, ndipo sindidziwa kumene awaika.” 14 Atakamba zimenezi anaceuka, ndipo anaona kuti Yesu ali cilili pamenepo, koma mayiyo sanamuzindikile kuti ndi Yesu. 15 Yesu anamufunsa kuti: “Mayi, n’cifukwa ciyani mukulila? Kodi mukufuna ndani?” Poganiza kuti munthuyo anali wosamalila munda, anamuyankha kuti: “Bambo, ngati ndinu mwamutenga, ndiuzeni kumene mwamuika, ndipo ndipita kukamutenga.” 16 Yesu anamuuza kuti: “Mariya!” Mariya ataceuka, anauza Yesu m’Ciheberi kuti: “Rab·bo′ni!” (kutanthauza “Mphunzitsi!”) 17 Yesu anamuuza kuti: “Usandikangamile, cifukwa nthawi yakuti ndipite kwa Atate sinakwane. Koma pita kwa abale anga ukawauze kuti, ‘Ine ndikupita kwa Atate wanga komanso Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndiponso Mulungu wanu.’” 18 Mariya Mmagadala anafika kwa ophunzilawo ndi kuwauza uthenga wakuti: “Ine ndawaona Ambuye!” Ndipo anawafotokozela zimene Yesu anamuuza.
19 Madzulo tsiku limenelo, tsiku loyamba la mlungu, ophunzila ake anasonkhana pamodzi m’nyumba ina yake. Iwo anakhoma zitseko za nyumbayo cifukwa anali kuopa Ayuda. Ndiyeno Yesu anafika n’kuimilila pakati pawo, ndipo anati kwa iwo: “Mtendele ukhale nanu.” 20 Atakamba izi, anawaonetsa manja ndi m’nthiti mwake. Ndipo ophunzilawo anakondwela ataona Ambuyewo. 21 Yesu anawauzanso kuti: “Mtendele ukhale nanu. Monga mmene Atate ananditumila, inenso ndikukutumani.” 22 Atakamba izi, Yesu anawafuzilila mpweya n’kuwauza kuti: “Landilani mzimu woyela. 23 Mukakhululukila munthu macimo, ndiye kuti Mulungu wamukhululukila kale. Koma mukapanda kukhululukila munthu macimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukile.”
24 Koma Thomasi, mmodzi wa ophunzila 12 amenewo, amene anali kudziwikanso kuti Didimo sanalipo pamene Yesu anabwela. 25 Conco ophunzila enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anawauza kuti: “Ngati sindiona mabala* a misomali m’manja mwawo, ndi kuika cala canga m’mabala a misomaliwo, komanso kuika dzanja langa m’nthiti mwawo, ine sindikhulupilila.”
26 Patapita masiku 8, ophunzila ake anasonkhananso m’nyumba, ndipo Thomasi anali nawo. Yesu analowa ngakhale kuti zitseko zinali zokhoma, ndipo anaimilila pakati pawo n’kukamba kuti: “Mtendele ukhale nanu.” 27 Kenako anauza Thomasi kuti: “Ika cala cako apa, komanso ona manja anga. Gwila m’nthiti mwangamu ndi dzanja lako, ndipo uleke kukayikila* koma ukhulupilile.” 28 Thomasi anamuyankha kuti: “Mbuyanga komanso Mulungu wanga!” 29 Yesu anamuuza kuti: “Popeza wandiona, kodi wakhulupilila? Acimwemwe ndi amene amakhulupilila ngakhale sanaone.”
30 Kukamba zoona, Yesu anacitanso zozizwitsa* zina zambili pamaso pa ophunzila ake, zimene sizinalembedwe mu mpukutu uno. 31 Koma zimenezi zinalembedwa n’colinga cakuti mukhulupilile kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndiponso cifukwa cokhulupilila, mukhale ndi moyo kupitila m’dzina lake.
21 Pambuyo pa izi, Yesu anaonekelanso kwa ophunzilawo ku nyanja ya Tiberiyo. Kuonekela kwake kunali motele. 2 Kumeneko kunali Simoni Petulo, Thomasi (wochedwa Didimo), Natanayeli wa ku Kana wa ku Galileya, ana a Zebedayo, ndi ophunzila ake ena awili, onsewa anali pamodzi. 3 Simoni Petulo anauza anzakewo kuti: “Ine ndikupita kukapha nsomba.” Iwo anamuuza kuti: “Ifenso tipita nawe.” Iwo anapita kukakwela bwato n’kupita naye, koma usiku umenewo sanaphe kalikonse.
4 Pamene kunali kuca, Yesu anaimilila m’mbali mwa nyanja, koma ophunzilawo sanazindikile kuti anali Yesu. 5 Yesu anawafunsa kuti: “Ana inu, kodi muli ndi cakudya ciliconse?”* Iwo anayankha kuti: “Ayi!” 6 Iye anawauza kuti: “Ponyani ukonde wanu kudzanja lamanja la bwatolo ndipo mupezako kanthu.” Iwo anaponyadi ukondewo, koma sanakwanitse kuuguzila m’bwatolo cifukwa ca kuculuka kwa nsomba. 7 Kenako, wophunzila amene Yesu anali kumukonda anauza Petulo kuti: “Ndi Ambuye!” Ndiyeno Simoni Petulo atamva kuti ndi Ambuye, anavala covala cake cakunja, cifukwa anali malisece,* ndipo analumphila m’nyanja. 8 Koma ophunzila enawo anabwela m’bwato laling’ono akukoka ukonde wodzala ndi nsomba, cifukwa sanali kutali kwenikweni ndi mtunda, panali cabe mtunda wa mamita pafupifupi 90.
9 Atafika kumtunda anaona moto wamalasha, ndipo pa motowo panali nsomba ndi mkate. 10 Yesu anawauza kuti: “Bweletsani zina mwa nsomba zimene mwangopha kumenezo.” 11 Conco Simoni Petulo anakwela m’bwatomo n’kukokela ku mtunda ukonde wodzala ndi nsomba zikuluzikulu zokwana 153. Koma ngakhale kuti zinali zoculuka zedi, ukondewo sunang’ambike. 12 Yesu anawauza kuti: “Bwelani mudye cakudya cam’mawa.” Panalibe ngakhale wophunzila mmodzi amene analimba mtima kumufunsa kuti: “Kodi ndinu ndani?” cifukwa iwo anadziwa kuti ndi Ambuye. 13 Yesu anatenga mkate n’kuwapatsa, ndipo anacitanso cimodzimodzi ndi nsomba. 14 Aka kanali kacitatu Yesu kuonekela kwa ophunzilawo pambuyo pakuti waukitsidwa kwa akufa.
15 Atatsiliza kudya cakudya ca m’mawaco, Yesu anafunsa Simoni Petulo kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine kuposa izi?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mukudziwa kuti ndimakukondani kwambili.” Iye anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga.” 16 Yesu anamufunsanso kaciwili kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine?” Iye anamuyankha kuti: “Inde Ambuye, inunso mudziwa kuti ndimakukondani kwambili.” Yesu anamuuza kuti: “Weta ana a nkhosa anga.” 17 Iye anamufunsanso kacitatu kuti: “Simoni mwana wa Yohane, kodi umandikonda ine?” Petulo anamva cisoni kuti anafunsidwa kacitatu kuti: “Kodi ine umandikonda kwambili?” Conco iye anamuuza kuti: “Ambuye, inu mudziwa zonse. Mudziwa kuti ndimakukondani kwambili.” Yesu anamuuza kuti: “Dyetsa ana a nkhosa anga. 18 Ndithudi ndikukuuza, pamene unali mnyamata unali kudzivalika wekha n’kupita kumene unali kufuna. Koma ukadzakalamba, udzatambasula manja ako, ndipo munthu wina adzakuvalika, ndipo adzakunyamula ndi kukupeleka kumene iwe sufuna.” 19 Iye anakamba zimenezi poonetsa mtundu wa imfa imene Petulo adzalemekeza nayo Mulungu. Atanena zimenezi, anamuuza kuti: “Pitiliza kunditsatila.”
20 Petulo anaceuka, ndipo anaona wophunzila amene Yesu anali kumukonda akuwatsatila. Wophunzilayu ndi uja amene anatsamila pacifuwa ca Yesu pa cakudya camadzulo n’kumufunsa kuti: “Ambuye, ndani amene akufuna kukupelekani?” 21 Ndiyeno Petulo atamuona, anafunsa Yesu kuti: “Ambuye, nanga n’ciyani cidzacitika kwa uyu?” 22 Yesu anamuuza kuti: “Ngati ine ndifuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka n’tabwela, kodi iwe zikukhudza bwanji? Iwe ungopitiliza kunditsatila.” 23 Conco mbili imene inamveka pakati pa abale inali yakuti wophunzilayu sadzafa. Koma Yesu sanakambe kuti wophunzilayu sadzafa ayi. Iye anati: “Ngati ine ndifuna kuti akhalebe ndi moyo mpaka n’tabwela, kodi zikukhudza bwanji?”
24 Wophunzilayu ndi amene akucitila umboni zinthu zimenezi. Iye ndiye analemba zinthu zimenezi, ndipo tidziwa kuti umboni wake ndi woona.
25 Palinso zinthu zina zambili zimene Yesu anacita. Zinthu zimenezi zikanalembedwa mwatsatanetsatane, ndiona kuti mipukutu yolembedwayo sikanakwana padziko.
Kapena kuti, “anali waumulungu.”
M’cinenelo coyambilila, “magazi.”
M’cinenelo coyambilila, “cifunilo ca thupi.”
Kapena kuti, “anali ndi cisomo ca Mulungu.”
Kapena kuti, “pacifuwa ca Atate.” Kutanthauza malo abwino apadela.
M’cinenelo coyambilila, “ola la 10.”
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ndi dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.
M’cinenelo coyambilila, “n’ciyani kwa ine ndi inu mayi.” Awa ndi mawu okuluwika oonetsa kukana. Pokamba kuti mayi, sikuti Yesu anataya ulemu.
M’cinenelo coyambilila, “zizindikilo zake.”
Kapena kuti, “msika.”
M’cinenelo coyambilila, “anakhulupilila dzina lake.”
M’cinenelo coyambilila, “zizindikilo.”
“Rabi ndi dzina laulemu la mphunzitsi wa Ciyuda.”
Ma Baibo ena amati, “sanabadwe kucokela kumwamba.”
M’cinenelo coyambilila, “sanakhulupilile m’dzina la.”
Kapena kuti, “ zisadzudzulidwe.”
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi Rabi ndi dzina laulemu la mphunzitsi wa Ciyuda.
Kapena kuti, “watsimikizila.”
Kapena kuti, “mocita kupima.”
M’cinenelo coyambilila, “ambuye.”
Kapena kuti, “kasupe wamadzi.”
M’cinenelo coyambilila, “ola la 6.”
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi Rabi ndi dzina laulemu la mphunzitsi wa Ciyuda.
M’cinenelo coyambilila, “mwayela kale.”
Kapena kuti, “wacila.”
M’cinenelo coyambilila, “kutentha thupi.”
M’cinenelo coyambilila, “ola la 7.”
Kapena kuti, “akufa ziwalo.”
Mawu a pa vesiyi amapezeka m’ma Baibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.
Kapena kuti, “bedi.”
Kapena kuti, “bedi.”
Kapena kuti, “bedi.”
Kapena kuti, “bedi.”
Kapena kuti, “ali ndi mphamvu zopeleka moyo; mwa iye mwini muli mphatso ya moyo.”
M’cinenelo coyambilila, “zizindikilo zodabwitsa.”
M’cinenelo coyambilila, “cizindikilo.”
M’cinenelo coyambilila, “masitadiya pafupifupi 25 kapena 30.”
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ndi dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.
M’cinenelo coyambilila, “zizindikilo.”
M’cinenelo coyambilila, “cizindikilo.”
M’cinenelo coyambilila, “sanamukokele.”
M’cinenelo coyambilila, “dziko.”
M’cinenelo coyambilila, “mwa inu mulibe moyo.”
Ma Baibo ena amati, “pamene anali kuphunzitsa pamalo ocitila misonkhano.”
Kapena kuti, “ndi mdyelekezi.”
Kapena kuti, “anapitiliza kuyendayenda.”
M’cinenelo coyambilila, “zolemba.”
Kutanthauza, “masukulu a Arabi.”
Kapena kuti, “amumange.”
Kapena kuti, “kumumanga.”
“Mipukutu ingapo komanso yodalilika ilibe vesi 53 mpaka caputala 8 vesi 11.”
Kapena kuti, “potengela mfundo za anthu.”
Onani Matanthauzo a Mawu Ena.
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ndi dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.”
M’cinenelo coyambilila, “zizindikilo.”
Kapena kuti, “anamuwelamila.”
M’cinenelo coyambilila, “Ndinalandila lamulo limeneli kucokela kwa Atate wanga.”
Kapena kuti, “ndife ogwilizana.”
Kapena kuti, “ofanana ndi mulungu.”
M’cinenelo coyambilila, “cizindikilo ciliconse.”
Kapena kuti, “Rabi.” M’Ciheberi, Rabi ndi dzina laulemu la mphunzitsi waciyuda.
Kapena kuti, “m’manda acikumbutso.”
M’cinenelo coyambilila, “masitadiya pafupifupi 15.”
Kapena kuti, “kumanda acikumbutso.”
M’cinenelo coyambilila, “mumzimu.”
Kapena kuti, “kumanda acikumbutsowo.”
M’cinenelo coyambilila, “Sanihedirini.”
M’cinenelo coyambilila, “zizindikilo zambili.”
Kutanthauza kacisi.
Kapena kuti, “akamumange.”
Kapena kuti, “akudya pa thebulo.”
Kapena kuti, “m’manda acikumbutso.”
M’cinenelo coyambilila, “cizindikilo cimeneci.”
Kapena kuti, “moyo wanga ukuvutika.”
Kutanthauza kuphedwa pamtengo.
Onani mawu a m’munsi pa Yohane 12:32
M’cinenelo coyambilila, “zizindikilo.”
Kapena kuti, “wakhulupilila lipoti lathu limene wamva.”
Kapena kuti, “wandiukila.”
M’cinenelo coyambilila, “pacifuwa ca Yesu.”
Kapena kuti, “wokutonthozani.”
Kapena kuti, “monga ana amasiye.”
Kapena kuti, “kuidulila.”
M’cinenelo coyambilila, “musapunthwe.”
Kutanthauza, kulila kwa gulu la anthu pamalilo.
Kapena kuti, “akamaphunzila za inu.”
Kapena kuti, “amvela.”
Kapena kuti, “ogwilizana.”
Kapena kuti, “ogwilizana.”
Kapena kuti, “apatuleni.”
Kapena kuti, “polowela.”
Kapena kuti, “citila umboni.”
Kapena kuti, “akanakhala kuti si wophwanya malamulo.”
Kapena kuti, “mutamandike.”
Kapena kuti, “aphedwe mwa kumupacika pamtengo.”
Kapena kuti, “aphedwe mwa kumupacika pamtengo.”
Kapena kuti, “zolamula kuti akuphe mwa kukupacika pamtengo.”
M’cinenelo coyambilila, “pafupifupi ola la 6.”
Kapena kuti, “aphedwe mwa kumupacika pamtengo.”
Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Onani Matanthauzo a Mau Ena.
Kapena kuti, “anatsilizika.”
Kapena kuti, “sadzaphwanyidwa.”
Kapena kuti, “kuphedwa mwa kumupacika pamtengo.”
Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
Kapena kuti, “kumanda acikumbutso.”
Kapena kuti, “manda acikumbutso.”
Kapena kuti, “zizindikilo.”
M’cinenelo coyambilila, “kukhala wosakhulupilila.”
Kapena kuti, “zizindikilo.”
Kapena kuti, “kodi muli ndi nsomba iliyonse?”
Kapena kuti, “anali wosavala mokwanila.”