LAIBULALI YA PA INTANETI ya Watchtower
Watchtower
LAIBULALI YA PA INTANETI
Cinyanja
  • BAIBO
  • ZOFALITSA
  • MISONKHANO
  • nwt Aroma 1:1-16:27
  • Aroma

Palibe vidiyo yake.

Pepani, vidiyo yakanga kulila.

  • Aroma
  • Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Baibo ya Cimasulilo ca Dziko Latsopano
Aroma

KALATA KWA AROMA

1 Ine Paulo kapolo wa Khristu Yesu, ndinaitanidwa kuti ndikhale mtumwi komanso ndinasankhidwa kuti ndilengeze uthenga wabwino wa Mulungu. 2 Iye analonjeza uthengawu kalekale kupitila mwa aneneli ake m’Malemba oyela. 3 Uthengawo umakamba za Mwana wake, amene ndi mbadwa* ya Davide, 4 ndipo Mulungu anaukitsa Mwana wake ameneyu mwa kugwilitsa nchito mphamvu ya mzimu wake woyela. Inde, ameneyu ndi Yesu Khristu Ambuye wathu. 5 Kudzela mwa ameneyu, tinalandila cisomo ca Mulungu, ndipo ndinasankhidwa kukhala mtumwi kuti ndikathandize anthu a mitundu yonse kuti aonetse cikhulupililo, akhale omvela, ndiponso kuti alemekeze dzina lake. 6 Inunso munaitanidwa pakati pa anthu a mitundu imeneyo kuti mukhale otsatila a Yesu Khristu. 7 Kalatayi ndalembela inu nonse okhala ku Roma amene mumakondedwa ndi Mulungu komanso munaitanidwa kuti mukhale oyela:

Cisomo ndi mtendele wocokela kwa Mulungu Atate wathu ndi Ambuye Yesu Khristu zikhale nanu.

8 Coyamba, ndikuyamika Mulungu wanga kudzela mwa Yesu Khristu cifukwa ca nonsenu, cifukwa anthu padziko lonse akukamba za cikhulupililo canu. 9 Nthawi zonse ndikamapemphela ndimakuchulani m’mapemphelo anga, ndipo Mulungu, amene ndikumucitila utumiki wopatulika ndi mtima wanga wonse polalikila uthenga wabwino wonena za Mwana wake, akundicitila umboni. 10 Ndimapempha Mulungu kuti ngati n’kotheka komanso ngati n’zimene iye akufuna, ndibwele kwanuko tsopano. 11 Cifukwa ndikulakalaka kudzakuonani kuti ndidzakupatseni mphatso inayake yauzimu, kuti mukhale olimba, 12 kapena kuti ndidzalimbikitsidwe ndi cikhulupililo canu, inunso mudzalimbikitsidwe ndi cikhulupililo canga.

13 Koma ndikufuna kuti mudziwe abale, kuti kwa nthawi yaitali ndakhala ndikufuna kubwela kwanuko koma zakhala zikulepheleka mpaka pano. Ndikufuna ndidzaone zotulukapo zabwino za nchito yathu yolalikila ngati mmene zilili pakati pa anthu a mitundu ina yonse. 14 Ine ndili ndi nkhongole kwa Agiriki ndi kwa anthu amene si Agiriki, komanso kwa anthu anzelu ndi kwa anthu opusa. 15 Conco ndikufunitsitsa kudzalengeza uthenga wabwino kwa inunso kumeneko ku Roma. 16 Ine sindikucita nawo manyazi uthenga wabwino. Kukamba zoona, uthengawo ndi njila yamphamvu imene Mulungu akuigwilitsa nchito populumutsa aliyense amene ali ndi cikhulupililo, coyamba Ayuda kenako Agiriki. 17 Mu uthenga umenewu, Mulungu amaulula cilungamo cake kwa anthu amene ali ndi cikhulupililo. Zikatelo, cikhulupililo ca anthuwo cimalimba mogwilizana ndi zimene Malemba amakamba kuti: “Koma wolungama adzakhala ndi moyo cifukwa ca cikhulupililo cake.”

18 Kucokela kumwamba, Mulungu akuonetsa mkwiyo wake kwa anthu onse osamuopa, ndi osalungama amene akucititsa kuti coonadi cisadziwike. 19 Cifukwa Mulungu wawapatsa umboni wokwanila wowathandiza kuti amudziwe. 20 Kucokela pomwe dziko linalengedwa, makhalidwe a Mulungu osaoneka ndi maso akuonekela bwino. Makhalidwe akewo, ngakhalenso mphamvu zake zosatha komanso Umulungu wake, zikuonekela m’zinthu zimene anapanga, moti anthuwo alibenso cifukwa comveka cosakhulupilila kuti Mulungu aliko. 21 Ngakhale kuti iwo anali kumudziwa Mulungu, sanamulemekeze monga Mulungu kapena kumuyamikila. M’malomwake, iwo anayamba kuganiza mopanda nzelu, ndipo mitima yawo yopusa inacita mdima. 22 Ngakhale kuti amakamba kuti ndi anzelu, iwo ndi opusa. 23 M’malo molemekeza Mulungu amene sangafe, iwo amalemekeza zifanizilo za anthu amene amafa, komanso zifanizilo za mbalame, nyama za miyendo inayi ndiponso nyama zokwawa.

24 Conco malinga ndi zilakolako za mitima yawo, Mulungu anawaleka kuti acite zonyansa, kuti acititse manyazi matupi awo. 25 Iwo anasinthanitsa coonadi ca Mulungu ndi bodza, ndipo amalambila ndiponso kucita utumiki wopatulika ku zinthu zolengedwa m’malo mwa Mlengi amene ayenela kutamandidwa mpaka muyaya. Ameni. 26 N’cifukwa cake Mulungu anawaleka kuti atsatile zilakolako zosalamulilika za kugonana, popeza akazi pakati pawo analeka njila yacibadwa yogwilitsila nchito matupi awo n’kumacita zosemphana ndi cibadwa. 27 Amunanso cimodzimodzi, analeka njila yacibadwa yofuna akazi* n’kumatenthetsana okhaokha mwaciwawa ndi cilakolako coipa. Amuna okhaokha kucitilana zonyansa n’kulandililatu mphoto yoyenelela kulakwa kwawo.

28 Popeza iwo sanaone kuti afunika kudziwa Mulungu molondola, iye anawasiya kuti apitilize kuganiza zoipa, n’kumacita zinthu zosayenela. 29 Ndipo anali kucita zosalungama za mtundu ulionse, kuipa konse, dyela,* komanso zinthu zonse zoipa. Mitima yawo inadzaza ndi kaduka, kupha anthu, ndewo, cinyengo ndi njilu. Anali kukonda misece, 30 ndiponso kujeda anzawo, anali kudana ndi Mulungu, anali acipongwe, odzikuza, odzitama, aciwembu, osamvela makolo, 31 osazindikila, osasunga mapangano, opanda cikondi cacibadwa, komanso opanda cifundo. 32 Ngakhale kuti anthu amenewa amalidziwa bwino lamulo lolungama la Mulungu, lakuti amene amacita zinthu zimenezi ndi oyenela imfa, amapitiliza kuzicita. Komanso amagwilizana ndi anthu amene amacita zimenezi.

2 Conco kaya ndiwe ndani, ngati umaweluza ena, ulibe cifukwa comveka codzilungamitsila. Pakuti ukamaweluza ena, umakhala ukudzitsutsa wekha, cifukwa iwenso umacita zomwezo. 2 Ndipo tikudziwa kuti Mulungu akamaweluza anthu amene amacita zimenezi kuti ndi oyenela kulandila cilango, amawaweluza mogwilizana ndi coonadi.

3 Koma kodi iwe ukamaweluza anthu amene amacita zinthu zimene iwenso umacita, kodi uganiza kuti udzacithawa ciweluzo ca Mulungu? 4 Kodi sudziwa kuti Mulungu akukusonyeza kukoma mtima kwake kwakukulu, sakukukwiyila msanga, ndipo akukulezela mtima n’colinga coti ulape? 5 Koma cifukwa ca unkhutukumve wako ndi mtima wako wosafuna kulapa, ukuputa mkwiyo wa Mulungu umene udzaonekela pa tsiku la mkwiyo wake podzaulula ciweluzo cake colungama. 6 Iye adzaweluza aliyense malinga ndi zocita zake. 7 Adzapeleka moyo wosatha kwa anthu amene akufunafuna ulemelelo, ulemu ndi moyo wosawonongeka mwa kupilila pocita nchito zabwino. 8 Koma anthu okonda mikangano, amene satsatila coonadi koma amacita zosalungama, Mulungu adzawaonetsa mkwiyo wake. 9 Munthu aliyense wocita zinthu zoipa adzakumana ndi masautso komanso zowawa, kaya akhale Myuda kapena Mgiriki. 10 Koma munthu aliyense wocita zabwino, adzalandila ulemelelo, ulemu ndi mtendele, coyamba kwa Myuda kenako kwa Mgiriki. 11 Cifukwa Mulungu alibe tsankho.

12 Anthu onse amene anacimwa popanda kudziwa Cilamulo, adzafa popanda kudziwa Cilamulo. Koma onse amene anacimwa akudziwa Cilamulo, adzaweluzidwa mogwilizana ndi Cilamuloco. 13 Pakuti anthu amene amangomva cabe Cilamulo si olungama pamaso pa Mulungu, koma amene amacita zimene Cilamulo cimanena ndi amene adzaonedwe kuti ndi olungama. 14 Pakuti anthu a mitundu ina amene alibe Cilamulo, akamacita mwacibadwa zinthu za m’Cilamulo, ngakhale kuti alibe Cilamulo amaonetsa kuti ali ndi Cilamulo mu mtima mwawo. 15 Iwo amaonetsa kuti mfundo za m’Cilamulo zinalembedwa m’mitima yawo, ndipo cikumbumtima cawo cimawacitila umboni. Anthuwa maganizo awo amawatsutsa kapena kuwatsimikizila kuti acita zoyenela. 16 Zimenezi zidzacitika pa tsiku limene Mulungu, kudzela mwa Khristu Yesu, adzaweluza zinthu zobisika zimene anthu amacita mogwilizana ndi uthenga wabwino umene ndimalalikila.

17 Ena a inu ndinu Ayuda mwa dzina cabe, ndipo mumadalila Cilamulo, ndiponso mumanyadila kuti muli pa ubwenzi ndi Mulungu. 18 Mumadziwa cifunilo ca Mulungu komanso mumavomeleza zinthu zabwino kwambili cifukwa n’zimene munaphunzitsidwa* m’Cilamulo. 19 Mumakhulupilila kuti mungatsogolele akhungu komanso kuunikila anthu amene ali mu mdima. 20 Mumaganiza kuti mungawongolele anthu opanda nzelu, komanso mungaphunzitse ana cifukwa mumamvetsa komanso kudziwa coonadi copezeka m’Cilamulo. 21 Kodi iwe amene umaphunzitsa ena, bwanji sudziphunzitsa wekha? Iwe amene umalalikila kuti, “Usabe,” kodi umabanso? 22 Iwe amene umati, “Usacite cigololo,” kodi umacitanso cigololo? Iwe amene umanyansidwa ndi mafano, umabanso za mu akacisi a mafano? 23 Iwe amene umanyadila Cilamulo, kodi umanyoza Mulungu mwa kuphwanya Cilamulo? 24 Pakuti “dzina la Mulungu likunyozedwa pakati pa anthu a mitundu ina cifukwa ca inu,” monga mmene Malemba amanenela.

25 Mdulidwe umakhala waphindu pokhapokha ngati iweyo umatsatila Cilamulo. Koma ngati umaphwanya Cilamulo, mdulidwe wako umakhala wopanda phindu. 26 Conco ngati munthu wosadulidwa akutsatila mfundo zolungama za Cilamulo, ndiye kuti kusadulidwa kwake kudzaoneka ngati kudulidwa, si conco kodi? 27 Munthu wosadulidwa kuthupi akamatsatila Cilamulo, iye adzakuweluza mwa kucita zimene Cilamulo cimanena. Adzakuweluza iwe amene umaphwanya Cilamulo ngakhale kuti uli ndi malamulo olembedwa ndiponso ndiwe wodulidwa. 28 Amene ndi Myuda kunja kokha si Myuda weniweni, ndiponso mdulidwe wakunja kokha wocitidwa pa thupi si mdulidwe weniweni. 29 Kukhala Myuda weniweni kuli mumtima, ndipo mdulidwe wake ndi wa mumtima wocitidwa ndi mzimu, osati ndi malamulo olembedwa. Munthu wotelo amatamandidwa ndi Mulungu, osati anthu.

3 Kodi kukhala Myuda kuli ndi ubwino wanji, kapena mdulidwe uli ndi phindu lanji? 2 Ubwino wake ndi wambili. Coyamba, mawu opatulika a Mulungu anaikidwa m’manja mwa Ayuda. 3 Nanga bwanji ngati ena anali osakhulupilika? Kodi kusowa cikhulupililo kwawoko kukutanthauza kuti Mulungunso ndi wosakhulupilika? 4 M’pang’ono pomwe! Kwake Mulungu n’kukamba zoona nthawi zonse, ngakhale zitapezeka kuti munthu aliyense ndi wabodza, monga mmene Malemba amanenela kuti: “Mukamalankhula, mumalankhula zacilungamo kuti muwine mlandu pamene mukuweluzidwa.” 5 Komabe ngati kusalungama kwathu kukuonetsa bwino kuti Mulungu ndi wolungama, ndiye tikambe kuti ciyani? Kodi tingakambe kuti Mulungu ndi wosalungama akaonetsa mkwiyo wake? (Ndikulankhula ngati mmene anthu ena onse amalankhulila.) 6 Ayi! Nanga Mulungu akapanda kutelo, kodi adzaliweluza bwanji dziko?

7 Koma ngati cifukwa ca bodza langa coonadi ca Mulungu caonekela kwambili ndipo zimenezo zamubweletsela ulemelelo, n’cifukwa ciyani ndikuweluzidwa monga wocimwa? 8 Ndilekelenji kukamba zimene ena amatinamizila kuti timati: “Tiyeni ticite zoipa kuti zabwino zibwele”? Anthu amenewa adzaweluzidwa mogwilizana ndi cilungamo.

9 Ndiye kodi Ayudafe tili pamalo abwino kuposa ena? Kutali-tali! Cifukwa monga takambila kale, Ayuda ndiponso Agiriki, onse amalamulilidwa ndi ucimo 10 monga mmene Malemba amanenela kuti: “Palibe munthu wolungama ngakhale mmodzi yemwe. 11 Palibe aliyense amene ndi wozindikila ngakhale pang’ono, komanso palibe aliyense amene akuyesetsa kufunafuna Mulungu. 12 Anthu onse apatuka, ndipo onsewo akhala anthu opanda pake. Palibe ngakhale mmodzi amene akuonetsa kukoma mtima.” 13 “Mmelo wawo ndi manda otseguka. Iwo amalankhula zosoceletsa ndi lilime lawo.” “M’milomo yawo muli poizoni wa njoka.” 14 “Ndipo m’kamwa mwawo ndi modzala ndi matembelelo komanso mawu opweteka.” 15 “Mapazi awo amathamangila kukakhetsa magazi.” 16 “Zocita zawo zonse zimakhala zowononga komanso zobweletsa mavuto, 17 ndipo njila ya mtendele saidziwa.” 18 “Iwo saopa Mulungu.”

19 Tsopano tadziwa kuti zinthu zonse zimene Cilamulo cimanena, zimagwila nchito kwa amene amatsatila Cilamuloco. Colinga cake n’kucititsa anthu onse kusowa conena, komanso kuonetsa kuti dziko lonse lili ndi mlandu kwa Mulungu, ndipo liyenela kulangidwa. 20 Conco palibe aliyense amene adzaonedwa wolungama ndi Mulungu mwa kucita nchito za Cilamulo, pakuti Cilamulo cimatithandiza kudziwa bwino ucimo.

21 Koma tsopano zadziwika kuti munthu angakhale wolungama kwa Mulungu popanda kutsatila Cilamulo. Izi zinacitilidwa umboni m’Cilamulo komanso m’zolemba za aneneli. 22 Onse amene amakhulupilila Yesu Khristu, angaonedwe kukhala olungama ndi Mulungu cifukwa palibe kusiyana. 23 Pakuti anthu onse ndi ocimwa ndipo ndi opelewela pa ulemelelo wa Mulungu. 24 Ndipo iwo amaonedwa kukhala olungama mwa cisomo cake cimene waonetsa powamasula kudzela m’dipo limene Khristu Yesu analipila, kumene kuli ngati mphatso yaulele. 25 Mulungu anamupeleka monga nsembe yothandiza anthu kuyanjananso ndi Mulunguyo mwa kukhulupilila magazi ake. Anacita izi pofuna kuonetsa cilungamo cake, cifukwa anaonetsa kuti ndi wosakwiya msanga mwa kukhululuka macimo amene anacitika kale. 26 Anacita izi kuti aonetse cilungamo cake pa nthawi ino, mwa kuona kuti munthu amene amakhulupilila Yesu ndi wolungama.

27 Ndiye kodi pali cifukwa canji codzitamandila? Palibiletu. Kodi tizidzitama cifukwa cotsatila Cilamulo citi? Lamulo la nchito? Ayi ndithu, koma cifukwa cotsatila lamulo la cikhulupililo. 28 Pakuti munthu amakhala wolungama mwa cikhulupililo osati mwa kutsatila Cilamulo. 29 Kodi iye ndi Mulungu wa Ayuda okha? Kodi si kutinso ndi Mulungu wa a mitundu ina? Inde, alinso Mulungu wa anthu a mitundu ina. 30 Pakuti Mulungu ndi mmodzi, iye adzaona kuti anthu odulidwa ndi olungama cifukwa ca cikhulupililo cawo, ndipo adzaonanso kuti anthu osadulidwa ndi olungama cifukwa ca cikhulupililo cawo. 31 Ndiye kodi pamenepa tikuthetsa Cilamulo mwa cikhulupililo cathu? Ayi ndithu! M’malomwake tikulimbikitsa Cilamulo.

4 Popeza zili telo, kodi tingakambe ciyani za kholo lathu Abulahamu? 2 Mwacitsanzo, ngati Abulahamu anaonedwa kuti ndi wolungama cifukwa ca zimene anacita, akanakhala ndi cifukwa codzitamandila, koma osati pamaso pa Mulungu. 3 Kodi paja Malemba amati ciyani? Amati: “Abulahamu anakhulupilila mwa Yehova, ndipo anaonedwa kuti ndi wolungama.” 4 Munthu amene wagwila nchito, saona malipilo ake ngati cisomo, koma ngati cinthu cimene ayenela kulandila.* 5 Koma Mulungu amene amaona anthu ocimwa kukhala olungama amaona kuti munthu yemwe sanagwile nchito, koma amamukhulupilila, ndi wolungama. 6 Davide anakamba za munthu wacimwemwe amene Mulungu amamuona kuti ndi wolungama ngakhale kuti zimene wacita sizikugwilizana kwenikweni ndi Cilamulo. Iye anakamba kuti. 7 “Acimwemwe ndi anthu amene akhululukidwa zocita zawo zophwanya malamulo, ndipo macimo awo akhululukidwa.* 8 Wacimwemwe ndi munthu amene Yehova sadzamuwelengela chimo lake.”

9 Kodi ndi anthu odulidwa cabe amene amakhala acimwemwe? Kapena osadulidwa nawonso amakhala acimwemwe? Paja timati: “Abulahamu anaonedwa wolungama cifukwa ca cikhulupililo cake.” 10 Ndiye kodi iye anaonedwa wolungama ali mu mkhalidwe wotani? Ali wodulidwa kapena wosadulidwa? Iye anali asanadulidwe. 11 Ndipo Mulungu anapatsa Abulahamu mdulidwe ngati cizindikilo cotsimikizila kuti iye anamuona kuti ndi wolungama asanadulidwe cifukwa ca cikhulupililo cake. Anacita zimenezi kuti adzakhale tate wa onse osadulidwa amene ali ndi cikhulupililo kuti anthuwo adzaonedwe kuti ndi olungama. 12 Kuti adzakhalenso tate wa ana odulidwa, osati kwa odulidwa okha ayi, komanso wa amene amayenda moyenela potsatila cikhulupililo cimene tate wathu Abulahamu anali naco asanadulidwe.

13 Cifukwa Abulahamu kapena mbadwa* zake sanalonjezedwe kuti adzalandila dziko monga colowa cawo cifukwa ca Cilamulo ayi. Koma analonjezedwa cifukwa anali ndi cikhulupililo, ndipo Mulungu anamuona kuti ndi wolungama. 14 Pakuti ngati anthu amene akutsatilabe Cilamulo ndi amene adzalandile colowaco, ndiye kuti cikhulupililo cilibenso nchito ndipo lonjezo lija lathetsedwa. 15 Zoona zake n’zakuti, kuphwanya Cilamulo kumacititsa kuti munthu alandile cilango, koma pamene palibe lamulo, palibenso kulakwa.

16 N’cifukwa cake iye anapatsidwa lonjezolo cifukwa ca cikhulupililo, kuti likhale logwilizana ndi cisomo. Komanso anapatsidwa lonjezolo kuti likhale lotsimikizika kwa anthu onse amene ndi mbadwa* zake, osati otsatila Cilamulo okha, koma kuphatikizapo otsatila cikhulupililo ca Abulahamu amene ndi tate wa tonsefe. 17 (Izi n’zogwilizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Ndakusankha kuti ukhale tate wa mitundu yambili.”) Zinali conco pamaso pa Mulungu amene Abulahamu anali kukhulupilila, amenenso amaukitsa akufa ndipo amachula zinthu zimene palibe ngati kuti zilipo.* 18 Abulahamu anali ndi ciyembekezo ndiponso cikhulupililo cakuti adzakhala tate wa mitundu yambili, ngakhale kuti zimenezi zinali kuoneka kuti n’zosatheka. Anakhulupilila izi mogwilizana ndi zimene zinanenedwa kuti: “Umu ndi mmene mbadwa* zako zidzakhalile.” 19 Ndipo ngakhale kuti cikhulupililo cake sicinafooke, pa nthawiyo anali kuona thupi lake ngati lakufa (cifukwa anali ndi zaka pafupifupi 100). Anali kudziwanso kuti Sara ndi wokalamba kwambili moti sangabeleke. 20 Koma cifukwa ca lonjezo la Mulungu, iye sanagwedezeke pa cikhulupililo, koma anakhala wamphamvu mwa cikhulupililo, ndipo anapeleka ulemelelo kwa Mulungu. 21 Iye sanakayikile ngakhale pang’ono kuti zimene Mulungu anamulonjeza angathenso kuzicita. 22 Conco, “Mulungu anamuona kuti ndi wolungama.”

23 Komabe, mawu akuti “Mulungu anamuona kuti ndi wolungama” sanalembedwele iye cabe. 24 Analembelanso ife, amene timaonedwanso olungama cifukwa timakhulupilila Mulungu amene anaukitsa Yesu Ambuye wathu. 25 Yesu anapelekedwa kaamba ka macimo athu, ndipo anaukitsidwa kuti tionedwe olungama.

5 Popeza kuti tsopano tikuonedwa kuti ndife olungama cifukwa cokhala ndi cikhulupililo, tiyeni tikhale pa mtendele* ndi Mulungu kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu. 2 Kukhulupilila Yesu kumatithandiza kuti tizitha kufika kwa Mulungu komanso kuti tizisangalala ndi cisomo cake. Ndipo tiyeni tisangalale* cifukwa tili ndi ciyembekezo colandila ulemelelo wa Mulungu. 3 Si zokhazo, koma tiyeni tizisangalala* tikakumana ndi masautso cifukwa tikudziwa kuti masautso amacititsa kuti tipilile. 4 Kupilila nakonso kumacititsa kuti tikhale ovomelezeka kwa Mulungu, ndipo kukhala ovomelezeka kwa Mulungu kumacititsa kuti tikhale ndi ciyembekezo. 5 Ciyembekezoco sicitigwilitsa mwala cifukwa Mulungu amaonetsa kuti amatikonda mwa kutipatsa mzimu wake woyela.

6 Tikusowa mtengo wogwila, Khristu anafela anthu ocimwa pa nthawi yoikidwilatu. 7 Cifukwa n’capatali kuti munthu aliyense afele munthu wolungama. Koma mwina munthu angalimbe mtima n’kufela munthu wabwino. 8 Koma Mulungu akutionetsa cikondi cake cifukwa pamene tinali ocimwa Khristu anatifela. 9 Ndiponso adzacita zoposa pamenepo mwa kutipulumutsa ku mkwiyo wake kudzela mwa Khristu, popeza tikuonedwa olungama cifukwa ca magazi a Khristuyo. 10 Pakuti pamene tinali adani ake, tinagwilizanitsidwa ndi Mulungu kudzela mu imfa ya Mwana wake. Kuwonjezela pamenepo, moyo wake udzatipulumutsa popeza tsopano tagwilizanitsidwa. 11 Si izi cabe ayi, koma tikusangalalanso mwa Mulungu kudzela mwa Ambuye wathu Yesu Khristu amene kupitila mwa iye tagwilizanitsidwa ndi Mulungu.

12 N’cifukwa cake monga mmene ucimo unalowela m’dziko kudzela mwa munthu mmodzi, ndi imfa kudzela mwa ucimo, imfayo inafalikila kwa anthu onse cifukwa onse anacimwa. 13 Pakuti ucimo unalimo kale m’dziko Cilamulo cisanabwele, koma palibe aliyense amene angaimbidwe mlandu wakuti wacimwa ngati palibe lamulo. 14 Ngakhale n’telo, imfa inalamulila ngati mfumu kuyambila nthawi ya Adamu mpaka ya Mose, ngakhalenso kwa anthu amene sanacimwe mofanana ndi mmene Adamu anacimwila. Adamuyo ndi wofanana ndi amene anali kubwela.

15 Koma mphatsoyo siili ngati ucimowo. Anthu ambili anafa cifukwa ca ucimo wa munthu mmodzi. Koma cisomo cacikulu ca Mulungu ndiponso mphatso yake yaulele imene anaipeleka mokoma mtima kupitila mwa munthu mmodzi, Yesu Khristu, n’zapamwamba kwambili. Mulungu anapeleka mphatso imeneyi kwa anthu onse, ndipo inabweletsa madalitso osaneneka.* 16 Komanso pali kusiyana pakati pa mphatso yaulele imeneyi, ndi mmene zinthu zinakhalila kudzela mwa munthu mmodzi amene anacimwa. Pakuti ciweluzo ca chimo limodzi lija cinali kulandila cilango. Koma mphatso imene inapelekedwa kaamba ka macimo ambili inapangitsa kuti anthu azionedwa kuti ndi olungama. 17 Imfa inalamulila monga mfumu cifukwa ca kucimwa kwa munthu mmodziyo. Koma anthu amene analandila cisomo cacikulu ca Mulungu ndiponso mphatso yake yaulele ya cilungamo, adzakhala ndi moyo kuti alamulile ngati mafumu kudzela mwa munthu mmodziyu, Yesu Khristu.

18 Conco monga mmene chimo limodzi linapangitsila kuti anthu a mitundu yonse aweluzidwe kuti ndi ocimwa, cimodzimodzinso kucita cinthu cimodzi colungama, kunacititsanso kuti anthu a mitundu yonse aonedwe kuti ndi olungama kuti akhale ndi moyo. 19 Pakuti monga mmene kusamvela kwa munthu mmodziyo kunacititsila kuti ambili akhale ocimwa, cimodzimodzinso kudzela mwa kumvela kwa munthu mmodziyo kudzacititsa kuti ambili akhale olungama. 20 Cilamulo cinapelekedwa kuti kucimwa kwa anthu kuonekele poyela. Koma pamene ucimo unaonekela kwambili, cisomo ca Mulungu cinawonjezekanso kwambili. 21 Cifukwa ciyani? Kuti monga mmene ucimo unalamulila ngati mfumu pamodzi ndi imfa, momwemonso cisomo cilamulile monga mfumu kudzela m’cilungamo. Izi zidzacititsa kuti anthu akapeze moyo wosatha kupyolela mwa Yesu Khristu Ambuye wathu.

6 Ndiye kodi tinene kuti ciyani? Tipitilize kucimwa kuti cisomo ciwonjezeke? 2 Ayi ndithu! Popeza kuti tinamasulidwa* ku ucimo, ndiye n’cifukwa ciyani tipitilize kucimwa? 3 Kapena simukudziwa kuti ife tonse amene tinabatizidwa, ndipo tsopano ndife ogwilizana ndi Khristu Yesu, tinabatizidwanso mu imfa yake? 4 Conco ife tinaikidwa naye m’manda pamene tinabatizidwa mu imfa yake, monga mmene Khristu anaukitsidwila kudzela mu ulemelelo wa Atate, kuti tikhale umoyo watsopano. 5 Ngati takhala ogwilizana naye mwa kufa imfa yofanana ndi yake, mosakaikila tidzagwilizananso naye poukitsidwa mofanana naye. 6 Pakuti tikudziwa kuti umunthu wathu wakale unapacikidwa pa mtengo limodzi naye n’colinga coti thupi la ucimo likhale lopanda mphamvu, kuti tisakhalenso akapolo a ucimo. 7 Pakuti munthu amene wafa sakhalanso ndi mlandu* wa macimo ake.

8 Cina, ngati tinafa limodzi ndi Khristu, timakhulupilila kuti tidzakhalanso ndi moyo limodzi ndi iye. 9 Tikudziwa kuti popeza Khristu waukitsidwa, iye sadzafanso ayi, ndipo imfa siikumulamulilanso monga mfumu. 10 Pakuti anafa kuti acotse ucimo kamodzi kokha basi, ndipo moyo umene ali nawo, ali nawo kuti azicita cifunilo ca Mulungu. 11 Inunso muzidziona ngati akufa pa nkhani ya ucimo, koma ngati amoyo kwa Mulungu mwa Khristu Yesu.

12 Conco musalole kuti ucimo upitilize kulamulila monga mfumu m’matupi anu amene akhoza kufa kuti muzitsatila zilakolako zawo. 13 Komanso musapeleke matupi* anu ku ucimo monga zida za nchito zosalungama, koma dzipelekeni kwa Mulungu monga anthu amene aukitsidwa kwa akufa, ndiponso matupi* anu muwapeleke kwa Mulungu monga zida za nchito zolungama. 14 Pakuti ucimo suyenela kukulamulilani monga mfumu, cifukwa simukutsatila Cilamulo, koma mumapindula ndi cisomo ca Mulungu.

15 Ndiye kodi tizicita ciyani? Tizicimwa cifukwa cakuti sitikutsatila Cilamulo koma tikupindula ndi cisomo ca Mulungu? Ayi ndithu! 16 Kodi simukudziwa kuti mukadzipeleka kwa wina aliyense ngati akapolo omvela, mumakhala akapolo a munthu amene mukumvelayo? Mumakhala akapolo a ucimo umene umatsogolela ku imfa, kapena akapolo a kumvela kumene kumatsogolela ku cilungamo. 17 Koma tikumuyamikila Mulungu kuti ngakhale kuti poyamba munali akapolo a ucimo munamvela mocokela pansi pa mtima mfundo zimene munaphunzitsidwa. 18 Inde, popeza kuti munamasulidwa ku ucimo, munakhala akapolo a cilungamo. 19 Ndikulankhula ngati munthu cifukwa ca kufooka kwa matupi anu. Pakuti munapeleka ziwalo zanu ngati akapolo a zonyansa, ndiponso akapolo a kusamvela malamulo kuti muzicita zinthu zophwanya malamulo. Tsopano pelekaninso ziwalo zanu kuti zikhale ngati akapolo a cilungamo kuti muzicita zoyela. 20 Pakuti pamene munali akapolo a ucimo munali omasuka ku cilungamo.

21 Kodi munali kubala zipatso zotani pa nthawiyo? Zinali zinthu zimene mumacita nazo manyazi palipano. Ndipo mapeto a zinthu zimenezo ndi imfa. 22 Koma tsopano, cifukwa cakuti munamasulidwa ku ucimo ndipo munakhala akapolo a Mulungu, mukubala zipatso zoyela, ndipo pa mapeto pake mudzakhala ndi moyo wosatha. 23 Pakuti malipilo a ucimo ndi imfa, koma mphatso imene Mulungu amapeleka ndi moyo wosatha kudzela mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

7 Kodi simukudziwa abale, (pakuti ndikulankhula ndi anthu odziwa cilamulo) kuti Cilamulo cimakhala ndi mphamvu pa munthu pamene ali ndi moyo? 2 Mwacitsanzo, mkazi wokwatiwa amakhala womangidwa kwa mwamuna wake mwalamulo pamene mwamunayo ali moyo. Koma mwamuna wakeyo akamwalila, mkaziyo amamasuka ku lamulo la mwamuna wake. 3 Conco, ngati mkaziyo angakwatiwe ndi mwamuna wina mwamuna wake ali moyo, ndiye kuti wacita cigololo. Koma ngati mwamuna wake wamwalila, mkaziyo amamasuka ku lamulo la mwamuna wake. Ndipo sanacite cigololo akakwatiwa ndi mwamuna wina.

4 Conco abale anga, thupi la Khristu linakumasulani* ku Cilamulo kuti mukhale a winawake amene anaukitsidwa ndi colinga cakuti tibale zipatso kwa Mulungu. 5 Pakuti pamene tinali kukhala mogwilizana ndi matupi athu ocimwawa, Cilamulo cinacititsa kuti zilakolako za ucimo zimene tinali nazo m’matupi* mwathu zionekele. Ndipo zilakolako zimenezi zinatibweletsela imfa. 6 Koma tsopano tamasulidwa ku Cilamulo, cifukwa tafa ku Cilamulo cimene cinali kutimanga kuti tikhale akapolo m’njila yatsopano motsogoleledwa ndi mzimu, osati m’njila yakale motsogoleledwa ndi malamulo olembedwa.

7 Ndiye tinene kuti ciyani? Kodi Cilamulo ndi ucimo? Ayi ndithu! Kukamba zoona, sindikanadziwa ucimo zikanakhala kuti panalibe Cilamulo. Mwacitsanzo, sindikanadziwa za kukhumbila kwansanje ngati Cilamulo sicinanene kuti: “Usasilile mwansanje.” 8 Koma cifukwa ca lamulo, ucimo unapeza njila yondipangitsa kukhala ndi kukhumbila kwansanje kwa mtundu ulionse. Pakuti popanda Cilamulo, ucimo unalibe mphamvu. 9 Cilamulo cisanapelekedwe ndinali wamoyo. Koma Cilamulo citafika, ucimo unakhalanso wamoyo, koma ine ndinafa. 10 Ndipo lamulo limene linali kufunika kunditsogolela ku moyo, linanditsogolela ku imfa. 11 Ucimo unagwilitsa nchito lamulo limeneli pondinyengelela ndipo unandipha. 12 Conco Cilamulo pacokha n’coyela, ndipo malamulo ndi oyela, olungama ndiponso abwino.

13 Kodi izi zitanthauza kuti cinthu cabwino cinacititsa kuti ine ndife? Ayi ndithu! Ucimo ndi umene unacititsa kuti ndife. Cilamulo n’cabwino, kungoti cinacititsa kuti zidziwike bwino kuti ucimo ukucititsa kuti ndife. Conco malamulo anatithandiza kudziwa kuti ucimo ndi woipa kwambili. 14 Pakuti tikudziwa kuti Cilamulo n’cocokela kwa Mulungu,* koma ine ndine wopanda ungwilo, ndipo ndinagulitsidwa ku ucimo. 15 Sindikumvetsa zimene zimandicitikila. Cifukwa sindicita zimene ndimafuna, koma ndimacita zimene ndimadana nazo. 16 Komabe ngati ndimacita zimene sindikufuna kucita, ndiye kuti ndikuvomeleza kuti Cilamulo n’cabwino. 17 Cifukwa sindine amene ndikucita zimenezo, koma ucimo umene uli mwa ine. 18 Pakuti ndikudziwa kuti mwa ine, kutanthauza m’thupi langali, mulibe cabwino ciliconse. Cifukwa ndimafuna kucita zabwino koma sindikwanitsa kuzicita. 19 Zinthu zabwino zimene ndimafuna kucita sindizicita, koma zoipa zimene sindifuna kucita n’zimene ndimacita. 20 Conco ngati ndimacita zimene sindifuna kucita, ndiye kuti amene akucita zimenezo sindine ayi, koma ndi ucimo umene uli mwa ine.

21 Zimene zimandicitikila n’zakuti,* pamene ndikufuna kucita zabwino, zoipa zimakhala kuti zili ndi ine. 22 Ndimasangalala kwambili ndi malamulo a Mulungu mu mtima mwanga, 23 koma ndimaona lamulo lina m’thupi* langa likumenyana ndi malamulo a m’maganizo mwanga n’kundicititsa kukhala kapolo wa lamulo la ucimo limene lili m’thupi* langa. 24 Munthu womvetsa cifundo ine! Ndani angandipulumutse ku thupi ili limene likundicititsa kuti ndife? 25 Ndiyamika Mulungu cifukwa adzandipulumutsa kudzela mwa Yesu Khristu Ambuye wathu. Conco m’maganizo mwanga ndine kapolo wa malamulo a Mulungu, koma m’thupi mwanga ndine kapolo wa lamulo la ucimo.

8 Conco anthu ogwilizana ndi Khristu Yesu alibe mlandu. 2 Pakuti lamulo la mzimu limene limapatsa moyo mogwilizana ndi Khristu Yesu, lakumasulani ku lamulo la ucimo ndi imfa. 3 Cilamulo sicinathe kukumasulani cifukwa anthu ndi ofooka komanso ocimwa. Koma Mulungu anakumasulani mwa kutumiza Mwana wake ali ndi thupi ngati la anthu ocimwa kuti athane ndi ucimo. Conco Mulungu anagonjetsa ucimo mwa kugwilitsa nchito thupi. 4 Mulungu anacita izi kuti ife amene timayenda motsogoleledwa ndi mzimu, osati motsogoleledwa ndi zofuna za thupi, tikwanilitse zolungama zimene Cilamulo cimafuna. 5 Cifukwa otsatila zofuna za thupi, amaika maganizo awo pa zinthu za thupi, koma otsatila mzimu, amaika maganizo awo pa zinthu za mzimu. 6 Pakuti kuika maganizo pa zinthu za thupi kumabweletsa imfa, koma kuika maganizo pa zinthu za mzimu kumabweletsa moyo ndi mtendele. 7 Cifukwa kuika maganizo pa zinthu za thupi kumapangitsa munthu kukhala pa udani ndi Mulungu popeza thupi siligonjela lamulo la Mulungu, ndipo kukamba zoona silingaligonjele. 8 Conco amene amacita zofuna za thupi sangakondweletse Mulungu.

9 Komabe inu simukucita zofuna za thupi koma za mzimu, ngati mzimu wa Mulungu ulidi mwa inu. Koma ngati wina alibe mzimu wa Khristu, ndiye kuti munthu ameneyo si wa Khristu. 10 Ngati Khristu ndi wogwilizana ndi inu, ngakhale kuti thupi ndi lakufa cifukwa ca ucimo, mzimu umacititsa kuti mukhale ndi moyo cifukwa ca cilungamo. 11 Tsopano ngati mzimu wa amene anaukitsa Yesu kwa akufa uli mwa inu, iye amene anaukitsa Khristu Yesu adzacititsanso matupi anu amene angathe kufawo kukhala ndi moyo, kupitila mwa mzimu wake umene uli mwa inu.

12 Conco abale, tisalole matupi athu kumatilamulila n’kumacita zinthu zimene matupiwo amafuna. 13 Cifukwa ngati mumacita zofuna za thupi, ndithu mudzafa. Koma mukalola mphamvu ya mzimu kupha nchito za thupi, mudzakhala ndi moyo. 14 Pakuti onse otsogoleledwa ndi mzimu wa Mulungu, alidi ana a Mulungu. 15 Cifukwa simunalandile mzimu wa ukapolo wokupangitsani kukhalanso ndi mantha, koma munalandila mzimu wakuti mukhale ana, umene timafuula nawo kuti: “Abba,* Atate!” 16 Mzimuwo umacitila umboni pamodzi ndi mzimu wathu kuti ndife ana a Mulungu. 17 Conco ngati ndife ana ake, ndiye kuti ndifenso olandila colowa kucokela kwa Mulungu. Koma tidzalandilanso colowa pamodzi ndi Khristu, ngati tikuvutika naye limodzi kuti tikalandile naye ulemelelo.

18 Ndikuona kuti mavuto amene tikukumana nawo palipano ndi aang’ono powayelekezela ndi ulemelelo umene udzaonekele kudzela mwa ife. 19 Cifukwa cilengedwe cikuyembekezela mwacidwi nthawi imene ulemelelo wa ana a Mulungu udzaonekela. 20 Pakuti cilengedwe cinaweluzidwa kuti cikhale copanda pake, osati mwa kufuna kwake koma kudzela mwa amene anaciweluza. Ndipo anapelekanso ciyembekezo 21 cakuti cilengedweco naconso cidzamasulidwa ku ukapolo wa thupi limene limawonongeka, n’kukhala ndi ufulu waulemelelo wa ana a Mulungu. 22 Pakuti tikudziwa kuti cilengedwe conse pamodzi cikubuula komanso kumva zowawa mpaka pano. 23 Koma sizokhazi. Ifeyo amene tili ndi zipatso zoyambilila zimene ndi mzimu, tikubuula mu mtima mwathu pamene tikuyembekezela mwacidwi kuti Mulungu atitenge kukhala ana ake, kutimasula ndi dipo ku matupi athuwa. 24 Cifukwa tinapulumutsidwa tili ndi ciyembekezo cimeneci, koma cimene ukuciyembekezela cikacitika, sicikhalanso ciyembekezo. Kodi cimene munthu anali kuyembekezela cikacitika, amaciyembekezelabe? 25 Koma ngati zimene tikuyembekezela sizinacitike, timapitiliza kuziyembekezela mwacidwi komanso mopilila.

26 Mofananamo, mzimu umatithandiza pa zimene timalephela kucita. Cifukwa vuto n’lakuti sitidziwa zimene tikufunika kuchula popemphela, koma mzimu umacondelela m’malo mwathu ndi madandaulo amene sitinathe kuwafotokoza. 27 Koma iye amene amafufuza mitima amadziwa zimene mzimu ukutanthauza, cifukwa umacondelela m’malo mwa oyela mogwilizana ndi cifunilo ca Mulungu.

28 Tikudziwa kuti Mulungu amagwilizanitsa zocita zake zonse pofuna kuthandiza amene amakonda Mulunguyo, anthu amene anawaitana mogwilizana ndi colinga cake. 29 Amatelo cifukwa amene anawadziwa coyamba anawasankhilatu kuti akakhale ofanana ndi Mwana wake, kuti iye akhale woyamba kubadwa pakati pa abale ake ambili. 30 Kuwonjezela apo, amene anawasankhilatuwo ndi amenenso anawaitana. Ndipo amene anawaitanawo ndi amenenso iye amawaona kuti ndi olungama. Ndipo anthu amene amawaona kuti ndi olungamawo ndi amenenso anawapatsa ulemelelo.

31 Ndiye kodi tinene ciyani pamenepa? Ngati Mulungu ali kumbali yathu, ndani adzatsutsana nafe? 32 Popeza sanatimane ngakhale Mwana wake koma anamupeleka m’malo mwa ife tonse, kodi sangatipatsenso mokoma mtima zinthu zina zonse pamodzi ndi Mwana wakeyo? 33 Ndani adzaimba mlandu anthu a Mulungu osankhidwa? Popeza Mulungu ndi amene amawaona kuti ndi olungama, 34 ndani adzawatsutsa? Khristu Yesu ndi amene anafa. Inde, kuwonjezela pamenepo ndi amene anaukitsidwa, amenenso ali ku dzanja lamanja la Mulungu, ndipo amacondelela m’malo mwathu.

35 Ndani adzatilekanitsa ndi cikondi ca Khristu? Kodi ndi masautso, zothetsa nzelu, mazunzo, njala, usiwa, zoopsa, kapena lupanga? 36 Malemba amati: “Cifukwa ca inu, tikuphedwa nthawi zonse. Takhala ngati nkhosa zokaphedwa.” 37 Koma tikugonjetsa zinthu zonsezi kothelatu mothandizidwa ndi iye amene anatikonda. 38 Pakuti ndatsimikiza mtima kuti kaya imfa, moyo, angelo, maboma, zinthu zimene zilipo, zinthu zimene zikubwela, mphamvu, 39 msinkhu, kuzama, kapena colengedwa ciliconse, sizidzatha kutilekanitsa ndi cikondi ca Mulungu cimene cili mwa Khristu Yesu Ambuye wathu.

9 Ndikunena zoona mogwilizana ndi Khristu, sindikunama ayi. Cikumbumtima canga cikundicitila umboni mogwilizana ndi mzimu woyela, 2 kuti ndikumva cisoni kwambili ndi kupweteka kosalekeza mu mtima mwanga. 3 Ndikanakonda kuti ine ndilekanitsidwe ndi Khristu monga munthu wotembeleledwa kaamba ka abale anga, anthu a mtundu wanga, 4 amene ndi Aisiraeli. Mulungu anawatenga iwo kuti akhale ana ake ndipo anawapatsa ulemelelo, mapangano, Cilamulo, utumiki wopatulika, ndi malonjezo. 5 Iwo ndi ana a makolo athu akale. Ndipo Khristu anabadwa ngati munthu kucokela kwa iwo. Mulungu, amene ndi wamkulu pa zinthu zonse, atamandike kwamuyaya. Ameni.

6 Komabe sikuti mawu a Mulungu sanakwanilitsidwe ayi. Cifukwa si onse amene ndi mbadwa* za Aisiraeli amene ndi “Aisiraeli enieni.” 7 Ndipo si onse amene ndi ana, cabe cifukwa ndi mbadwa* za Abulahamu. Koma Malemba amati, amene adzachedwa kuti “Mbadwa* zako adzacokela mwa Isaki.” 8 Izi zikutanthauza kuti si ana akuthupi amene ndi ana enieni a Mulungu, koma ana obadwa mogwilizana ndi lonjezolo ndi amene amawelengeledwa kuti ndi mbadwa.* 9 Pakuti lonjezo lija linati: “Panthawi ngati ino, ndidzabwela ndipo Sara adzakhala ndi mwana wamwamuna.” 10 Lonjezolo silinapelekedwe pa nthawi yokhayo. Koma linapelekedwanso pamene Rabeka anakhala ndi pakati pa ana amapasa kucokela kwa munthu mmodzi Isaki, kholo lathu lija. 11 Mapasawo asanabadwe komanso asanacite ciliconse cabwino kapena coipa, Mulungu anaonetsa kuti colinga cake cidzadalila iye amene amaitana, osati zocita za munthu. 12 Iye anauza Rabeka kuti: “Wamkulu adzakhala kapolo kwa wamngʼono.” 13 Mogwilizana ndi zimene Malemba amakamba kuti: “Ndinakonda Yakobo, koma Esau ndinadana naye.”

14 Ndiye tikambe kuti ciyani pamenepa? Kodi Mulungu alibe cilungamo? Ayi ndithu! 15 Cifukwa iye anauza Mose kuti: “Ine ndidzaonetsa cifundo kwa munthu aliyense amene ndafuna kumuonetsa cifundo, ndipo amene ndikufuna kumukomela mtima ndidzamukomela mtima.” 16 Conco sizidalila kufuna kwa munthu kapena khama lake,* koma Mulungu amene ndi wacifundo. 17 Ponena za Farao, Malemba amati: “Ndakusiya ndi moyo kuti ndikuonetse mphamvu zanga komanso kuti dzina langa lilengezedwe pa dziko lonse lapansi.” 18 Conco iye amacitila cifundo munthu aliyense amene wafuna kumucitila cifundo, koma amalola munthu aliyense amene wafuna kuumitsa mtima wake kuti auumitse.

19 Conco ungandiuze kuti: “N’cifukwa ciyani Mulungu akupezabe anthu zifukwa? Kodi ndani akutsutsa cifunilo cake?” 20 Munthu iwe, ndiwe ndani kuti uziyankhana ndi Mulungu? Kodi cinthu coumbidwa cingauze munthu amene anaciumba kuti, “Unandipangilanji conci?” 21 Kodi simukudziwa kuti woumba mbiya ali ndi ufulu woumba ciwiya cina kukhala ca nchito yolemekezeka, cina kukhala ca nchito yonyozeka kucokela ku dothi limodzimodzi? 22 Ndiye bwanji ngati Mulungu anafuna kuonetsa mkwiyo wake kuti mphamvu zake zidziwike, ndipo analekelela moleza mtima kwambili anthu oyenela kuwonongedwa amene anamukwiyitsa?* 23 Ndiponso bwanji ngati anacita zimenezo kuti aonetse kukula kwa ulemelelo wake kwa anthu oyenela kuwacitila cifundo,* amene anawakonzelatu kuti alandile ulemelelo, 24 ndipo anthu ake ndi ife amene anatiitana osati kucokela kwa Ayuda okha, koma kucokelanso ku mitundu ina? 25 Ndi zofanananso ndi zimene ananena mʼbuku la Hoseya kuti: “Aja amene si anthu anga ndidzawachula kuti ‘anthu anga,’ ndipo mkazi amene sanali kukondedwa ndidzamuchula kuti ‘wokondedwa.’ 26 Kumene analikuuzidwa kuti, ‘Sindinu anthu anga,’ kumeneko adzauzidwa kuti, ‘Ndinu ana a Mulungu wamoyo.’”

27 Komanso, Yesaya analengeza zokhudza Isiraeli kuti: “Ngakhale kuti ana a Isiraeli adzakhala ambili monga mcenga wakunyanja, ndi ocepa cabe amene adzapulumuke. 28 Cifukwa Yehova adzaweluza milandu pa dziko lapansi n’kuitsiliza mwamsanga.” 29 Ndiponso malinga ndi zimene Yesaya ananenelatu, “Yehova wa magulu ankhondo akanapanda kutisiyila mbadwa,* tikanakhala ngati Sodomu, ndipo tikanafanana ndi Gomora.”

30 Ndiye tikambe kuti ciyani pamenepa? Tikambe kuti anthu a mitundu ina ngakhale kuti sanatsatile cilungamo, iwo anapeza cilungamo cimene cimabwela cifukwa ca cikhulupililo. 31 Koma ngakhale kuti Aisiraeli anali kutsatila lamulo la cilungamo, sanakwanitse kulitsatila lamulo limenelo. 32 Cifukwa ciyani? Cifukwa cakuti anali kulitsatila mwa zocita zawo, koma osati mwa cikhulupililo. Iwo anapunthwa “pa mwala wopunthwitsa” 33 mogwilizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Taonani! Ine ndikuika mu Ziyoni mwala wopunthwitsa ndiponso thanthwe lokhumudwitsa, koma munthu wokhulupilila mwalawo sadzakhumudwa.”

10 Abale, cimene mtima wanga ukufuna komanso pemphelo langa locondelela kwa Mulungu ndi lakuti Aisiraeli apulumutsidwe. 2 Cifukwa ndikuwacitila umboni kuti ndi okangalika potumikila Mulungu, koma samudziwa molondola. 3 Koma cifukwa cosadziwa cilungamo ca Mulungu, koma n’kumafuna kukhazikitsa cilungamo cawocawo, iwo sanagonjele cilungamo ca Mulungu. 4 Khristu ndiye kutha kwa Cilamulo, kuti aliyense wokhulupilila akhale wolungama.

5 Mose analemba zokhudza cilungamo mogwilizana ndi Cilamulo kuti: “Munthu aliyense amene akucita zinthu zimenezi adzakhala ndi moyo mwa kucita zinthu zimenezo.” 6 Koma ponena za cilungamo cobwela cifukwa ca cikhulupililo, mawu a Mulungu amati: “Mu mtima mwako usamanene kuti, ‘Ndani adzapita kumwamba?’ kuti akatsitse Khristu. 7 Kapena ‘Ndani adzapita ku phompho,’ kuti akaukitse Khristu kwa akufa?” 8 Koma kodi lemba limati ciyani? Limati: “Mawu a Mulungu ali pafupi ndi inu, ali m’kamwa mwanu komanso m’mitima yanu.” Amenewo ndi “mawu” a cikhululupililo amene tikulalikila. 9 Pakuti ngati ukulengeza ndi pakamwa pako kuti Yesu ndi Ambuye, ndipo umakhulupilila mu mtima mwako kuti Mulungu anamuukitsa kwa akufa, udzapulumuka. 10 Cifukwa kuti munthu akhale wolungama amafunikila kukhala ndi cikhulupililo mumtima mwake, koma ndi pakamwa pake, amalengeza poyela cikhulupililo cake kuti akapulumuke.

11 Pakuti lemba lina limati: “Palibe munthu wokhulupilila mwa iye amene adzagwilitsidwa mwala.” 12 Palibe kusiyana pakati pa Myuda ndi Mgiriki, cifukwa onsewo Ambuye wawo ndi mmodzi, amene amapeleka mowolowa manja kwa onse oitana pa iye. 13 Pakuti “aliyense woitanila pa dzina la Yehova, adzapulumuka.” 14 Koma kodi iwo angaitane bwanji pa dzina lake ngati samukhulupilila? Nanga angamukhulupilile bwanji ngati sanamvepo za iye? Ndipo angamve bwanji za iye popanda wina kuwalalikila? 15 Ndiye kodi angalalikile bwanji ngati sanatumidwe? Zili monga mmene Malemba amakambila kuti: “Ndithudi, mapazi a anthu olengeza uthenga wabwino wa zinthu zabwino, ndi okongola kwambili!”

16 Ngakhale n’telo, iwo sanalabadile uthenga wabwino. Pakuti Yesaya anakamba kuti: “Yehova, ndani wakhulupilila zimene wamva kwa ife?”* 17 Conco munthu amakhala ndi cikhulupililo cifukwa ca zimene wamva. Ndipo zimene wamvazo zimacokela m’mawu okamba za Khristu. 18 Koma ndifunse kuti, Kodi iwo sanamve? Kukamba zoona “mawu anamveka pa dziko lonse lapansi, ndipo uthenga unamveka mpaka kumalekezelo a dziko lapansi kumene kuli anthu.” 19 Komanso ndifunse kuti, Kodi Aisiraeli sanadziwe? Coyamba Mose anati: “Ndidzakucititsani nsanje mwa kugwilitsa nchito anthu a mitundu ina. Ndidzakukwiyitsani koopsa mwa kugwilitsa nchito mtundu wopusa.” 20 Koma Yesaya analankhula molimba mtima kwambili kuti: “Amene anandipezawo ndi anthu amene sanali kundifunafuna. Ndinadziwika kwa anthu amene sanali kufunsa za ine.” 21 Koma ponena za Aisiraeli iye anati: “Ndatambasula manja anga tsiku lonse kwa anthu osamvela ndiponso ouma khosi.”

11 Ndiye ndifunse kuti, kodi Mulungu anakana anthu ake? Ayi! Pakuti inenso ndine Mwisiraeli, mbadwa* ya Abulahamu, wocokela mu fuko la Benjamini. 2 Mulungu sanakane anthu ake amene anali oyamba kuwasankha. Kodi simukudziwa zimene lemba lina limakamba zokhudza Eliya, pamene anali kucondelela Mulungu potsutsa Aisiraeli? Lembalo limati: 3 “Yehova, iwo apha aneneli anu ndipo agwetsa maguwa anu a nsembe, moti ndangotsala ndekhandekha. Ndipo tsopano akundifunafuna kuti andiphe.” 4 Koma kodi Mulungu anamuuza ciyani? Anamuuza kuti: “Ine ndasiya anthu 7,000 amene mawondo awo sanagwadilepo Baala.” 5 Conco mofananamo, palipano alipo ena ocepa amene anasankhidwa mwa cisomo. 6 Ndiye ngati anasankhidwa mwa cisomo, ndiye kuti sanasankhidwe cifukwa ca nchito zawo. Ngati si conco, ndiye kuti cisomo sicingakhalenso cisomo.

7 Ndiye tinene ciyani pamenepa? Cinthu cimene Aisiraeli anali kucifunafuna sanacipeze, koma osankhidwawo ndi amene anacipeza. Enawo anaumitsa mitima yawo 8 monga mmene Malemba amakambila kuti: “Mulungu wawapatsa mzimu wa tulo tofa nato, maso osayang’ana, ndi matu osamva mpaka lelo.” 9 Komanso Davide anati: “Thebulo lawo likhale msampha, mbuna, cokhumudwitsa, ndiponso cilango kwa iwo. 10 Maso awo acite mdima kuti asaone, ndipo nthawi zonse cititsani misana yawo kuwelama.”

11 Ndiyeno ndifunse kuti, kodi iwo anapunthwa mpaka kugwelatu? Ayi! Koma cifukwa ca kucimwa kwawo anthu a mitundu ina apeza cipulumutso, ndipo zimenezi zacititsa kuti iwo acite nsanje. 12 Kucimwa kwawo kwabweletsa cuma mʼdziko, ndipo kucepa kwawo kwabweletsa cuma kwa anthu a mitundu ina. Ndiye padzakhala madalitso ambili ciwelengelo cawo cikadzakwanila.

13 Tsopano ndikulankhula ndi inu anthu a mitundu ina. Popeza ndine mtumwi wotumidwa kwa anthu a mitundu ina, ndikulemekeza utumiki wanga, 14 kuti mwina ndingapangitse anthu a mtundu wanga* kucita nsanje nʼkupulumutsapo ena pakati pawo. 15 Pakuti ngati dziko lagwilizanitsidwa ndi Mulungu cifukwa coti iwo anatayidwa, ndiye kuti akadzalandilidwa zidzakhala monga kuti awaukitsa. 16 Komanso, ngati mbali ya mtanda wa mkate imene yapelekedwa nsembe monga cipatso coyambilila ndi yoyela, ndiye kuti mtanda wonse ndi woyelanso. Ndipo ngati muzu ndi woyela, ndiye kuti nthambi nazonso ndi zoyela.

17 Ngati nthambi zina zinadulidwa, ndipo iwe ngakhale kuti ndiwe nthambi ya mtengo wa maolivi wakuchile, unalumikizidwa pakati pa nthambi zotsala, ndipo unayamba kupeza zonse zofunikila kucokela ku muzu wa mtengo wa maolivi umenewo, 18 usayambe kutukumuka ku nthambi zimene zinadulidwazo. Koma ngati utukumuka kwa izo usaiwale kuti si ndiwe amene ukunyamula muzu, koma muzu ndi umene ukukunyamula iwe. 19 Mwina ukunena kuti: “Anadula nthambi zinazi kuti alumikizepo ine.” 20 Zimenezo nʼzoona. Iwo anadulidwa cifukwa ca kusowa cikhulupililo. Koma iwe ukali wolumikizidwa cifukwa ca cikhulupililo. Usadzitukumule, koma ukhale ndi mantha. 21 Cifukwa ngati Mulungu sanalekelele nthambi zacilengedwe, iwenso sadzakulekelela. 22 Conco uziganizila kukoma mtima kwa Mulungu, komanso mkwiyo wake. Amene anagwa anawaonetsa mkwiyo, koma iwe anakuonetsa kukoma mtima. Ukakhalabe woyenelela udzaonetsedwa kukoma mtima kwake. Apo ayi, iwenso udzadulidwa. 23 Ndipo iwonso akayamba kukhala ndi cikhulupililo, adzalumikizidwa, cifukwa Mulungu akhoza kuwalumikizanso. 24 Ngati iwe unadulidwa ku mtengo wa maolivi umene mwacilengedwe umamela m’chile, ndipo mosiyana ndi cilengedwe unalumikizidwa ku mtengo wa maolivi wolimidwa, kodi si capafupi kulumikiza nthambizi ku mtengo wawo umene zinadulidwako?

25 Pakuti sindikufuna kuti mukhale osadziwa cinsinsi copatulilka cimeneci abale, kuopela kuti mungadzione ngati anzelu. Cinsinsico n’cakuti ena mu Isiraeli aumitsa mitima yawo mpaka ciwelengelo conse ca a mitundu ina citakwanila. 26 Mwa njila imeneyi, Aisiraeli onse adzapulumutsidwa mogwilizana ndi zimene Malemba amanena kuti: “Mpulumutsi adzacokela ku Ziyoni, ndipo adzacotsela Yakobo nchito zonse zosalemekeza Mulungu. 27 Ndipo limeneli ndi pangano limene ndidzacite nawo ndikadzawacotsela macimo awo.” 28 N’zoona kuti iwo ndi adani a uthenga wabwino kuti inu zikupindulileni. Koma Mulungu anawasankha ndipo amawakonda cifukwa ca makolo awo akale. 29 Mulungu sadzadziimba mlandu cifukwa ca mphatso zake, ndiponso cifukwa cakuti anawaitana. 30 Inu pa nthawi ina munali osamvela Mulungu, koma tsopano mwaonetsedwa cifundo cifukwa ca kusamvela kwawo. 31 Mulungu wakucitilani cifundo cifukwa ca kusamvela kwa Ayuda. Koma angawacitilenso cifundo mmene anacitila kwa inu. 32 Mulungu walola onse kuti akhale akaidi a kusamvela kuti onsewo awacitile cifundo.

33 Ndithudi, madalitso a Mulungu ndi oculuka kwambili. Nzelu zake nʼzozama, ndiponso iye ndi wodziwa zinthu kwambili. Ziweluzo zake ndi zovuta kuzimvetsa, ndipo ndani angatulukile njila zake? 34 “Ndani wafika podziwa maganizo a Yehova, kapena ndani angakhale mlangizi wake?” 35 Kapenanso “ndani anayambilila kumupatsa kanthu, kuti amubwezele?” 36 Cifukwa zinthu zonse zimacokela kwa iye, ndipo ndiye anazipanga ndiponso ndi zake. Ulemelelo upite kwa iye mpaka muyaya. Ameni.

12 Conco abale, ndikukucondelelani mwa cifundo cacikulu ca Mulungu kuti mupeleke matupi anu monga nsembe yamoyo, yoyela, komanso yovomelezeka kwa Mulungu, umene ndi utumiki wopatulika pogwilitsa nchito luso lanu la kuganiza. 2 Lekani kutengela* nzelu za nthawi ino,* koma sandulikani mwa kusintha maganizo anu, kuti muzindikile cifunilo ca Mulungu, cabwino, covomelezeka, ndi cangwilo.

3 Cifukwa ca cisomo cimene Mulungu anandicitila, ndikuuza aliyense pakati panu kuti musamadziganizile kuposa mmene muyenela kudziganizila. Koma aliyense aziganiza mwanzelu mogwilizana ndi cikhulupililo cimene Mulungu wamupatsa.* 4 Thupi limakhala ndi ziwalo zambili, koma ziwalo zonsezo sizigwila nchito yofanana. 5 Conco ifenso ngakhale kuti tili ambili, ndife thupi limodzi mwa Khristu, ndipo ndife ziwalo zolumikizana. 6 Tili ndi mphatso zosiyanasiyana zimene Mulungu anatipatsa mwa cisomo cake. Conco kaya tili ndi mphatso ya kulosela, tiyeni tilosele mogwilizana ndi cikhulupililo cathu. 7 Kaya tili ndi mphatso ya utumiki, tiyeni ticite utumiki umenewo. Amene amaphunzitsa, aike mtima wake pa kuphunzitsako. 8 Amene amalimbikitsa, azilimbikitsa ndithu. Wogawila* azigawila mowolowa manja. Wotsogolela azitsogolela mwakhama. Ndipo amene amacitila ena cifundo, azitelo mokondwela.*

9 Cikondi canu cisakhale caciphamaso. Nyansidwani nazo zoipa, ndipo yesetsani kucita zabwino. 10 Poonetsa cikondi kwa abale, khalani ndi cikondi ceniceni. Pa nkhani yocitilana ulemu, inu mukhale woyamba. 11 Gwilani nchito molimbika,* ndipo musakhale alesi.* Yakani ndi mzimu. Tumikilani Yehova monga akapolo. 12 Muzikondwela cifukwa ca ciyembekezo. Muzipilila masautso. Limbikilani kupemphela. 13 Gawanani ndi oyelawo malinga ndi zimene akusowa. Khalani oceleza. 14 Pitilizani kudalitsa amene akukuzunzani. Adalitseni, m’malo mowatembelela. 15 Sangalalani ndi amene akusangalala, ndipo lilani ndi amene akulila. 16 Onani ena monga mmene inu mumadzionela. Musamaganize modzikuza,* koma khalani odzicepetsa. Musamadzione ngati anzelu.

17 Musabwezele coipa pa coipa kwa munthu wina aliyense. Ganizilani zimene anthu onse amaona kuti ndi zabwino. 18 Ngati nʼkotheka, yesetsani mmene mungathele kukhala mwamtendele ndi anthu onse. 19 Okondedwa, musamabwezele coipa, koma siyilani malo mkwiyo wa Mulungu. Pakuti Malemba amati: “‘Kubwezela ndi kwanga, ndidzabwezela ndine,’ watelo Yehova.” 20 Koma “ngati mdani wako ali ndi njala, m’patse cakudya. Ngati ali ndi ludzu, m’patse madzi akumwa. Pakuti ukacita zimenezi udzamuunjikila makala a moto pa mutu pake.”* 21 Musalole kuti coipa cikugonjetseni, koma pitilizani kugonjetsa coipa pocita cabwino.

13 Munthu aliyense azimvela aulamulilo waukulu, pakuti palibe ulamulilo umene ungakhalepo pokhapo ngati Mulungu waulola. Olamulila amene alipo ali pa maudindo awo osiyanasiyana m’mphamvuwo mololedwa ndi Mulungu. 2 Conco aliyense amene amatsutsana ndi ulamulilo, amatsutsana ndi zimene Mulungu anakonza. Amene amatsutsana ndi zimene Mulungu anakonza adzadzibweletsela ciweluzo. 3 Cifukwa olamulila amenewa amaopsa ngati umacita zoipa, osati ngati umacita zabwino. Kodi ukufuna kuti usamaope olamulila? Pitiliza kucita zabwino, ndipo olamulilawo adzakutamanda. 4 Iwo ndi mtumiki wa Mulungu kuti zinthu zizikuyendela bwino. Koma ngati ucita zoipa, uzicita mantha cifukwa iwo sanyamula lupanga pacabe. Olamulilawo ndi mtumiki wa Mulungu amene amaonetsa mkwiyo* wa Mulungu kwa munthu wocita zoipa.

5 Conco pali cifukwa comveka coti muziwagonjela, osati cabe cifukwa coopa mkwiyowo, koma cifukwanso ca cikumbumtima canu. 6 N’cifukwa cake mumakhomanso misonkho, cifukwa iwo ndi anchito a Mulungu otumikila anthu, ndipo amakwanilitsa colingaci nthawi zonse. 7 Pelekani kwa onse zimene amafuna.* Wofuna msonkho m’patseni msonkho. Wofuna ndalama ya ciphaso m’patseni ndalama ya ciphaso. Wofuna kuopedwa muopeni. Wofuna kupatsidwa ulemu m’patseni ulemu.

8 Musakhale ndi nkhongole iliyonse kwa munthu aliyense, kupatulapo nkhongole ya kukondana wina ndi mnzake, pakuti amene amakonda munthu mnzake amakwanilitsa lamulo. 9 Cifukwa malamulo onena kuti, “Usacite cigololo, usaphe munthu, usabe, usasilile mwansanje,” ndi lamulo lina lililonse limene lilipo, cidule cake n’cakuti: “Uzikonda munthu mnzako mmene umadzikondela wekha.” 10 Cikondi sicilimbikitsa munthu kucita mnzake zoipa. Conco cikondi cimalimbikitsa munthu kukwanilitsa lamulo.

11 Ndipo muzicita zimenezi cifukwa nyengo ino mukuidziwa, kuti tili kale m’nthawi yofunika kuti muuke ku tulo, cifukwa palipano cipulumutso cathu cayandikila kwambili kuposa pa nthawi imene tinakhala okhulupilila. 12 Usiku watsala pang’ono kutha, ndipo masana ayandikila. Conco tiyeni tivule n’kutaya nchito za mdima, ndipo tivale zida za kuwala. 13 Tiyeni tikhale ndi makhalidwe oyenela monga anthu ocita zinthu masana. Tizipewa maphwando oipa,* kumwa mwaucidakwa, ciwelewele, khalidwe lopanda manyazi,* mikangano, komanso nsanje. 14 Koma valani Ambuye Yesu Khristu, ndipo musamakonzekele kucita zimene thupi limalakalaka.

14 Landilani munthu amene ali ndi cikhulupililo cofooka, koma musamaweluze amene ali ndi maganizo osiyana ndi anu.* 2 Wina amakhala ndi cikhulupililo cakuti angadye ciliconse, koma munthu wofooka amadya zamasamba zokha. 3 Munthu amene amadya ciliconse, asamaone munthu amene amasala zakudya zina kukhala wotsika. Ndipo amene amasala zakudya zina, asaweluze munthu amene amadya ciliconse, cifukwa nayenso analandilidwa ndi Mulungu. 4 Kodi iwe ndiwe ndani kuti uweluze wanchito wa mwiniwake? Mbuye wake ndiye woyenela kumuweluza kuti ndi wolakwa kapena ndi wosalakwa, cifukwa Yehova ndiye angamuthandize kuti zimuyendele bwino.

5 Wina amaona tsiku lina kuti liposa linzake, koma wina amaona kuti masiku onse n’cimodzimodzi. Munthu aliyense atsimikize kuti zimene akukhulupilila n’zovomelezeka. 6 Amene amasunga tsiku amalisunga kuti alemekeze Yehova. Komanso amene amadya ciliconse, amadya kuti alemekeze Yehova cifukwa amayamika Mulungu. Amene amasala zakudya zina, amatelo kuti alemekeze Yehova, ndipo amayamika Mulungu. 7 Kukamba zoona, palibe aliyense wa ife amene amakhala ndi moyo kuti adzilemekeze yekha, ndipo palibe amene amafa kuti adzilemekeze yekha. 8 Pakuti tikakhala ndi moyo, timakhalila moyo Yehova, ndipo tikafa, timafela Yehova. Conco kaya tikhale ndi moyo kapena tife, ndife ake a Yehova. 9 Ndiye cifukwa cake Khristu anafa n’kukhalanso ndi moyo, kuti akhale Ambuye wa akufa komanso amoyo.

10 Koma n’cifukwa ciyani umaweluza m’bale wako? Kapenanso n’cifukwa ciyani umapeputsa m’bale wako? Pakuti tonsefe tidzaimilila patsogolo pa mpando woweluzila wa Mulungu. 11 Cifukwa Malemba amati: “‘Na pali ine Mulungu wamoyo,’ watelo Yehova, ‘bondo lililonse lidzandigwadila, pakuti lilime lililonse lidzavomeleza poyela kuti ndine Mulungu.’” 12 Cotelo, aliyense wa ife adzayankha yekha kwa Mulungu.

13 Pa cifukwa cimeneci, tisamaweluzane, m’malomwake tsimikizani mtima kuti simuikila m’bale wanu cokhumudwitsa kapena copunthwitsa. 14 Ndikudziwa komanso ndikukhulupilila mwa Ambuye Yesu kuti palibe cakudya cimene ndi codetsedwa pa ico cokha. Koma ngati munthu winawake akuona kuti cinacake ndi codetsedwa, ndiye kuti ndi codetsedwa kwa iye. 15 Ngati m’bale wako akukhumudwa cifukwa ca cakudya, ndiye kuti sukumuonetsanso cikondi. Musawononge munthu amene Khristu anamufela cifukwa ca zakudya zanu. 16 Conco musalole kuti anthu azikamba zoipa pa zabwino zimene mumacita. 17 Cifukwa pa nkhani ya Ufumu wa Mulungu, cofunika kwambili si kudya kapena kumwa ayi, koma cilungamo, mtendele, ndi cimwemwe, zimene zimabwela mwa mzimu woyela. 18 Aliyense wotumikila Khristu mwa njila imeneyi ndi wovomelezeka kwa Mulungu, ndipo anthu amakondwela naye.

19 Conco, tiyeni tiziyesetsa kucita zinthu zobweletsa mtendele, komanso zolimbikitsana wina ndi mnzake. 20 Lekani kuwononga nchito ya Mulungu cabe cifukwa ca zakudya. N’zoona kuti zakudya zonse n’zoyela, koma n’kulakwa* kudya zakudyazo ngati wina akukhumudwa nazo. 21 Si bwino kudya nyama kapena kumwa vinyo, kapena kucita ciliconse cimene cimakhumudwitsa m’bale wako. 22 Cikhulupililo cimene uli naco, ukhale naco pakati pa iwe ndi Mulungu. Munthu amakhala wacimwemwe ngati sakudziimba mlandu pa zimene wasankha kucita. 23 Ngati munthu amadya koma amakayikila, ndiye kuti watsutsidwa kale, cifukwa sakudya mogwilizana ndi cikhulupililo. Ndithudi, ciliconse cosagwilizana ndi cikhulupililo ndi chimo.

15 Ife olimba tiyenela kuganizila amene ndi ofooka, osati kumadzikondweletsa tokha. 2 Aliyense wa ife azicita zinthu zokondweletsa mnzake kuti amulimbikitse. 3 Cifukwa ngakhale Khristu sanacite zinthu zodzikondweletsa yekha, koma anacita mmene Malemba amanenela kuti: “Manyozo a anthu amene amakunyozani andigwela.” 4 Zinthu zonse zimene zinalembedwa kalekale zinalembedwa kuti zitilangize. Malembawa amatithandiza kupilila, komanso amatitonthoza ndi colinga coti tikhale ndi ciyembekezo. 5 Mulungu amene amatipatsa mphamvu kuti tipilile, komanso amene amatitonthoza, akuthandizeni nonsenu kukhala ndi maganizo amene Khristu Yesu anali nawo, 6 kuti ndi pakamwa panu, nonsenu capamodzi mutamande Mulungu, Atate wa Ambuye wathu Yesu Khristu.

7 Cotelo landilanani ngati mmene Khristu anakulandililani, kuti ulemelelo upite kwa Mulungu. 8 Kunena zoona, Khristu anakhala mtumiki wa anthu odulidwa potsimikizila kuti Mulungu ndi wokhulupilika. Mwakutelo, anaonetsa kuti malonjezo amene Mulungu anapatsa makolo awo akale ndi odalilika. 9 Anatelo kutinso anthu a mitundu ina alemekeze Mulungu kaamba ka cifundo cake, malinga n’kunena kwa Malemba kuti: “N’cifukwa cake ndidzakulemekezani pakati pa anthu a mitundu ina. Ndipo ndidzakuimbilani nyimbo zotamanda dzina lanu.” 10 Komanso Malemba amati: “Kondwelani inu anthu a mitundu ina pamodzi ndi anthu ake.” 11 Ndiponso amati: “Tamandani Yehova inu mitundu yonse ya anthu, ndipo anthu onse amutamande.” 12 Komanso Yesaya anakamba kuti: “Padzakhala muzu wa Jese, ndipo winawake wolamulila mitundu adzatuluka. Anthu a mitundu ina adzaika ciyembekezo cawo pa iye.” 13 Mulungu amene amapeleka ciyembekezo adzaze mitima yanu ndi cimwemwe cacikulu komanso mtendele wonse, mwa kumudalila kuti ciyembekezo canu cizikulilakulila* mothandizidwa ndi mphamvu ya mzimu woyela.

14 Abale anga, ine ndine wotsimikiza kuti inu ndinu okonzeka kucita zabwino. Mumadziwa zambili komanso mumatha kulangizana wina ndi mnzake. 15 Komabe, ndakulembelani mfundo zina mosapita mʼmbali kuti ndikukumbutseninso. Ndacita izi cifukwa ca cisomo cimene Mulungu anandicitila 16 pondiika kukhala mtumiki wa Khristu Yesu kwa anthu a mitundu ina. Ndikugwila nchito yopatulika yolengeza uthenga wabwino wa Mulungu kuti anthu a mitundu inawa, akhale monga nsembe yovomelezeka kwa Mulungu, imene yayeletsedwa ndi mzimu woyela.

17 Cotelo ndikusangalala kukhala wophunzila wa Khristu Yesu, komanso kugwila nchito ya Mulungu. 18 Pakuti sindidzalankhula ciliconse cimene ndacita pandekha, koma zokhazo zimene Khristu wacita ndi kulankhula kupitila mwa ine, kuti ndithandize anthu a mitundu ina kukhala omvela. 19 Iwo akhala omvela cifukwa ca zizindikilo komanso zodabwitsa zamphamvu zimene mzimu wa Mulungu wacita. Conco ndalalikila mokwanila uthenga wabwino wonena za Khristu, kuyambila ku Yerusalemu mpaka ku Iluriko. 20 Pocita zimenezi ndinatsimikiza mtima kuti ndisalengeze uthenga wabwino kumene anthu anali kulidziwa kale dzina la Khristu, nʼcolinga cakuti ndisamange pamaziko a munthu wina, 21 koma ndicite monga Malemba amanenela kuti: “Amene sanauzidwepo za iye adzamuona, ndipo amene sanamve adzazindikila.”

22 Ndiye cifukwa cakenso ndakhala ndikulephela kubwela kwa inu. 23 Koma tsopano kulibenso gawo lililonse limene sindinafikeko mʼmadela amenewa, ndipo kwa zaka zambili* ndakhala ndikulakalaka kubwela kwanuko. 24 Conco ndikuyembekezela kudzakuonani popita ku Sipaniya, ndipo ndikadzaceza nanu kwakanthawi, mudzandipelekeze pa ulendo wangawo. 25 Koma apa tsopano, ndatsala pang’ono kupita ku Yerusalemu kukatumikila oyela. 26 Abale a ku Makedoniya ndi a ku Akaya apeleka mosangalala mphatso kwa oyela ena a ku Yerusalemu omwe ndi osauka. 27 Nʼzoona kuti iwo anacita zimenezo mokondwela, komabe anali ndi nkhongole kwa oyelawo. Cifukwa ngati anthu a mitundu ina alandilako zinthu zauzimu kucokela kwa oyelawo, ndiye kuti nawonso ayenela kutumikila oyelawo mwa kuwapatsa zinthu zofunikila pa umoyo. 28 Cotelo ndikadzatsiliza kuwapatsa zopelekazi,* ndidzadzela kwanuko popita ku Sipaniya. 29 Komanso ndikudziwa kuti ndikadzafika kwanuko ndidzakubweletselani madalitso ambili ocokela kwa Khristu.

30 Conco abale, kupitila mwa Ambuye wathu Yesu Khristu komanso mwa cikondi ca mzimu oyela, ndikukupemphani kuti mulimbikile kundipemphelela kwa Mulungu, ndipo inenso ndilimbikila kupemphela, 31 kuti ndikalanditsidwe kwa anthu osakhulupilila a ku Yudeya, ndiponso kuti oyela a ku Yerusalemu akalandile bwino mphatso imene ndawanyamulila. 32 Ngati Mulungu alola, ndidzabwela kwa inu mokondwela, ndipo tidzalimbikitsana. 33 Mulungu amene amapeleka mtendele akhale nanu nonsenu. Ameni.

16 Ndikufuna kukudziwitsani za mlongo wathu Febe, amene akutumikila mu mpingo wa ku Kenkereya. 2 Mulandileni mwa Ambuye mmene mumalandilila oyelawo. Ndipo mum’patse thandizo lililonse limene angafunikile, cifukwa nayenso anateteza abale ambili, kuphatikizapo ine.

3 Mundipelekele moni kwa Purisika ndi Akula, anchito anzanga potumikila Khristu Yesu. 4 Iwo anaika miyoyo yawo paciopsezo cifukwa ca ine, ndipo si ine ndekha amene ndikuwayamikila, nayonso mipingo ya anthu a mitundu ina ikuwayamikila. 5 Ndikupelekanso moni ku mpingo umene umasonkhana m’nyumba yawo. Moni kwa wokondedwa wanga Epeneto, amene ndi cipatso coyambilila ca Khristu ku Asia. 6 Moni kwa Mariya, amene wagwila nchito mwakhama pokuthandizani. 7 Moni kwa Anduroniko ndi Yuniya, amene ndi acibale anga komanso akaidi anzanga. Amenewa ndi amuna odziwika kwambili kwa atumwi, ndiponso akhala ogwilizana ndi Khristu kwa nthawi yaitali kuposa ine.

8 Mundipelekele moni kwa Ampiliato, wokondedwa wanga mwa Ambuye. 9 Moni kwa Uribano, wanchito mnzathu mwa Khristu, komanso kwa wokondedwa wanga Sitaku. 10 Moni kwa Apele, wokhulupilika mwa Khristu. Moni kwa anthu a m’banja la Arisitobulo. 11 Moni kwa wacibale wanga Herodiona. Moni kwa anthu a m’banja la Narikiso omwe ndi otsatila a Ambuye. 12 Moni kwa Turufena ndi Turufosa, azimayi amene akugwila nchito mwakhama potumikila Ambuye. Moni kwa Peresida, wokondedwa wathu, amene wagwila nchito mwakhama potumikila Ambuye. 13 Moni kwa Rufu, wosankhidwa mwa Ambuye. Komanso kwa amayi ake amenenso ndi amayi anga. 14 Moni kwa Asunkirito, Felego, Heme, Pateroba, Heremase, ndiponso abale amene ali nawo limodzi. 15 Moni kwa Filologo ndi Yuliya, Nerea ndi mlongo wake komanso Olumpa ndi oyela onse amene ali nawo limodzi. 16 Mupatsane moni mwacikondi. Mipingo yonse ya Khristu ikupeleka moni.

17 Tsopano abale, ndikukulimbikitsani kuti musamale ndi anthu amene amabweletsa magawano komanso kucita zinthu zopunthwitsa ena. Izi ndi zosemphana ndi zimene munaphunzila, conco muziwapewa. 18 Pakuti anthu otelo si akapolo a Ambuye wathu Khristu, koma a zilakolako* zawo. Ndipo amagwilitsa nchito mawu okopa ndiponso acinyengo kuti apusitse anthu osalakwa. 19 Anthu onse akudziwa kuti ndinu omvela, ndipo ndine wokondwa kwambili cifukwa ca inu. Ndikufuna kuti mukhale anzelu pa zabwino, koma osadziwa kanthu pa zoipa. 20 Mulungu amene amapeleka mtendele adzaphwanya Satana pansi pa mapazi anu posacedwapa. Cisomo ca Ambuye wathu Yesu cikhale nanu.

21 Wanchito mnzanga Timoteyo akupeleka moni. Nawonso acibale anga amene ndi Lukiyo, Yasoni, ndi Sosipato akupeleka moni.

22 Ine Teritio, amene ndalemba kalatayi, ndikuti moni mwa Ambuye.

23 Gayo, amene ndikukhala kunyumba kwake, komanso amene mpingo umasonkhana ku nyumba kwake, akupeleka moni. Erasito msungicuma* wa mzinda akupeleka moni. Nayenso Kwarito m’bale wake akupeleka moni. 24* ——

25 Mulungu angakulimbitseni pogwilitsa nchito uthenga wabwino umene ndikulengeza, ndiponso uthenga wonena za Yesu Khristu umene ukulalikidwa. Uthengawu ndi wogwilizana ndi zimene zaululidwa zokhudza cinsinsi copatulika cimene cakhala cobisika kwa nthawi yaitali. 26 Koma tsopano cinsinsi cimeneci caululidwa, ndipo anthu a mitundu yonse acidziwa kudzela m’Malemba aulosi. Izi n’zogwilizana ndi lamulo la Mulungu wamuyaya. Kuti anthu a mitundu yonse azimumvela mwa cikhulupililo. 27 Kwa Mulungu yekhayo amene ndi wanzelu, kukhale ulemelelo kwamuyaya kudzela mwa Yesu Khristu. Ameni.

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

Kapena kuti, “njila yacibadwa ya kugonana ndi akazi.”

Kapena kuti, “kukhumbila kwansanje.”

Kapena kuti, “munaphunzitsidwa ndi mawu a pakamwa.”

Kapena kuti, “monga nkhongole.”

Kapena kuti, “aphimbidwa.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

Ma Baibo ena amati, “amacititsa zinthu zimene kulibe zikhalepo.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

Ma Baibo ena amati, “tili ndi mtendele.”

Ma Baibo ena amati, “timasangalala.”

Ma Baibo ena amati, “timasangalala.”

Kapena kuti, “osefukila.”

M’cinenelo coyambilila, “tinafa ku ucimo.”

Kapena kuti, “wamasulidwa, wakhululukidwa.”

M’cinenelo coyambilila, “ziwalo.”

M’cinenelo coyambilira, “ziwalo.”

M’cinenelo coyambilila, “tinafa ku Cilamulo.”

M’cinenelo coyambilila, “m’ziwalo.”

M’cinenelo coyambilila, “n’cauzimu.”

Kapena kuti, “Ndimapeza lamulo lakuti.”

M’cinenelo coyambilila, “m’ziwalo.”

M’cinenelo coyambilila, “m’ziwalo.”

Liwu la Ciheberi kapena Ciaramu lotanthauza, “Atate,” kapena “Ababa.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “osati amene akufuna kapenanso amene akuthamanga.”

M’cinenelo coyambilila, “ziwiya za mkwiyo.”

M’cinenelo coyambilila, “ziwiya za cifundo.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

Kapena kuti, “wakhulupilila lipoti lathu limene wamva.”

M’cinenelo coyambilila, “mbewu.”

M’cinenelo coyambilila, “mnofu wanga.”

Kapena kuti, “musamaumbidwe ndi.”

Onani Matanthauzo a Mau Ena.

Kapena kuti, “wamugawila.”

Kapena kuti, “wopatsa.”

Kapena kuti, “ndi mtima wonse.”

Kapena kuti, “mwakhama; mwacangu.”

Kapena kuti, “musamataye nthawi pa nchito mwa kungoyendayenda.”

Kapena kuti, “kukulitsa maganizo odzikuza.”

Kutanthauza, kufewetsa komanso kusungunula mtima wa munthu wovuta.

Kapena kuti, “amapeleka cilango.”

M’cinenelo coyambilila, “nkhongole.”

Kapena kuti, “maphwando aphokoso.”

Kapena kuti, “khalidwe lotayilila.”

Mabaibo ena amati, “osagamula pa zoganiza za mumtima mwake.”

Kutanthauza, kukhumudwitsa ena.

Kapena kuti, “cizisefukila.”

Mabaibo ena amati, “zingapo.”

M’cinenelo coyambilila, “cipatso.”

Kapena kuti, “mimba.”

Kapena kuti, “woyang’anila.”

Mawu a pa vesili amapezeka m’Mabaibo ena, koma sapezeka m’mipukutu yosiyanasiyana yodalilika yamakedzana ya Cigiriki.

    Mabuku a m’Cinyanja (2000-2025)
    Tulukani
    Loŵani
    • Cinyanja
    • Gawilani
    • Makonda
    • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
    • Zoyenela Kutsatila
    • Mfundo Yosunga Cisinsi
    • Kusunga Cinsinsi
    • JW.ORG
    • Loŵani
    Gawilani