Uthenga Wabwino Wolembedwa ndi Yohane
20 Pa tsiku loyamba la mlunguwo, Mariya Mmagadala anapita kumanda* kuja m’mamawa kukali mdima, ndipo anaona kuti cimwala cija cacotsedwa kale pamandapo.* 2 Conco iye anathamangila kwa Simoni Petulo, komanso kwa wophunzila wina uja amene Yesu anali kumukonda kwambili, ndipo anawauza kuti: “Ambuye awacotsa m’manda muja, ndipo sitidziwa kumene awaika.”
3 Pamenepo Petulo ndi wophunzila winayo ananyamuka kupita kumandako. 4 Ndiyeno awiliwo anayamba kuthamanga pamodzi, koma wophunzila winayo anathamanga kwambili kuposa Petulo, moti anayambilila kufika kumandako. 5 Atasuzila mkati, anaona nsalu zili pansi, koma sanalowemo. 6 Kenako Simoni Petulo amene anali kubwela m’mbuyo mwake nayenso anafika, ndipo analowa m’mandamo. Iye anaona nsalu zili pansi mmenemo. 7 Nsalu imene anamukulungila kumutu sinali pamodzi ndi nsalu zina, koma inali yopetekapeteka payokha. 8 Wophunzila winayo amene anayambilila kufika kumanda kuja nayenso analowa mkati. Ndipo ataona, anakhulupilila zimene anauzidwa. 9 Panthawiyo, iwo anali asanamvetse zimene lemba limanena, kuti Yesu ayenela kuuka kwa akufa. 10 Conco ophunzilawo anabwelela kunyumba zawo.
11 Koma Mariya anaimililabe panja pafupi ndi mandawo akulila. Pamene anali kulila, anawelama kuti aone m’mandamo. 12 Ndipo anaona angelo awili amene anavala zovala zoyela atakhala pomwe mtembo wa Yesu unagona. Wina anakhala pansi kumutu, ndipo winayo anakhala kumiyendo. 13 Iwo anamufunsa kuti: “Mayi, n’cifukwa ciyani mukulila?” Iye anayankha kuti: “Ambuye wanga atengedwa, ndipo sindidziwa kumene awaika.” 14 Atakamba zimenezi anaceuka, ndipo anaona kuti Yesu ali cilili pamenepo, koma mayiyo sanamuzindikile kuti ndi Yesu. 15 Yesu anamufunsa kuti: “Mayi, n’cifukwa ciyani mukulila? Kodi mukufuna ndani?” Poganiza kuti munthuyo anali wosamalila munda, anamuyankha kuti: “Bambo, ngati ndinu mwamutenga, ndiuzeni kumene mwamuika, ndipo ndipita kukamutenga.” 16 Yesu anamuuza kuti: “Mariya!” Mariya ataceuka, anauza Yesu m’Ciheberi kuti: “Rab·bo′ni!” (kutanthauza “Mphunzitsi!”) 17 Yesu anamuuza kuti: “Usandikangamile, cifukwa nthawi yakuti ndipite kwa Atate sinakwane. Koma pita kwa abale anga ukawauze kuti, ‘Ine ndikupita kwa Atate wanga komanso Atate wanu, kwa Mulungu wanga ndiponso Mulungu wanu.’” 18 Mariya Mmagadala anafika kwa ophunzilawo ndi kuwauza uthenga wakuti: “Ine ndawaona Ambuye!” Ndipo anawafotokozela zimene Yesu anamuuza.
19 Madzulo tsiku limenelo, tsiku loyamba la mlungu, ophunzila ake anasonkhana pamodzi m’nyumba ina yake. Iwo anakhoma zitseko za nyumbayo cifukwa anali kuopa Ayuda. Ndiyeno Yesu anafika n’kuimilila pakati pawo, ndipo anati kwa iwo: “Mtendele ukhale nanu.” 20 Atakamba izi, anawaonetsa manja ndi m’nthiti mwake. Ndipo ophunzilawo anakondwela ataona Ambuyewo. 21 Yesu anawauzanso kuti: “Mtendele ukhale nanu. Monga mmene Atate ananditumila, inenso ndikukutumani.” 22 Atakamba izi, Yesu anawafuzilila mpweya n’kuwauza kuti: “Landilani mzimu woyela. 23 Mukakhululukila munthu macimo, ndiye kuti Mulungu wamukhululukila kale. Koma mukapanda kukhululukila munthu macimo, ndiye kuti Mulungu sanamukhululukile.”
24 Koma Thomasi, mmodzi wa ophunzila 12 amenewo, amene anali kudziwikanso kuti Didimo sanalipo pamene Yesu anabwela. 25 Conco ophunzila enawo anamuuza kuti: “Ife tawaona Ambuye!” Koma iye anawauza kuti: “Ngati sindiona mabala* a misomali m’manja mwawo, ndi kuika cala canga m’mabala a misomaliwo, komanso kuika dzanja langa m’nthiti mwawo, ine sindikhulupilila.”
26 Patapita masiku 8, ophunzila ake anasonkhananso m’nyumba, ndipo Thomasi anali nawo. Yesu analowa ngakhale kuti zitseko zinali zokhoma, ndipo anaimilila pakati pawo n’kukamba kuti: “Mtendele ukhale nanu.” 27 Kenako anauza Thomasi kuti: “Ika cala cako apa, komanso ona manja anga. Gwila m’nthiti mwangamu ndi dzanja lako, ndipo uleke kukayikila* koma ukhulupilile.” 28 Thomasi anamuyankha kuti: “Mbuyanga komanso Mulungu wanga!” 29 Yesu anamuuza kuti: “Popeza wandiona, kodi wakhulupilila? Acimwemwe ndi amene amakhulupilila ngakhale sanaone.”
30 Kukamba zoona, Yesu anacitanso zozizwitsa* zina zambili pamaso pa ophunzila ake, zimene sizinalembedwe mu mpukutu uno. 31 Koma zimenezi zinalembedwa n’colinga cakuti mukhulupilile kuti Yesu ndi Khristu, Mwana wa Mulungu, ndiponso cifukwa cokhulupilila, mukhale ndi moyo kupitila m’dzina lake.