PHUNZILO 53
Sankhani Zosangalatsa Zovomelezeka kwa Yehova
Yehova ni “Mulungu wacimwemwe.” (1 Timoteyo 1:11) Iye amafuna kuti nafenso tizikhala na umoyo wacimwemwe komanso wosangalatsa. Ndipo amakondwela tikamapatula nthawi yakuti tipumuleko. Mu phunzilo lino, tiona mmene tingagwilitsile nchito nthawi yathu yosanguluka m’njila yabwino komanso yovomelezeka kwa Yehova.
1. Kodi tiyenela kukumbukila ciyani posankha zosangalatsa?
Kodi mumakonda kucita ciyani pamene mukupumula? Ena amakonda kungokhala panyumba—akuŵelenga buku, kumvela nyimbo, kutamba filimu, kapena kuyang’ana zinthu pa intaneti. Ena amakonda kucita zinthu pamodzi na anzawo monga—kupita kokayenda, kukanyaya, kapena kucita maseŵelo. Ciliconse cimene cingakhale makonda athu, tiyeni tionetsetse kuti tikusankha zosangalatsa ‘zovomelezeka kwa Ambuye.’ (Aefeso 5:10) M’pofunika kuimvetsetsa mfundo imeneyi, cifukwa m’zosangalatsa zambili masiku ano, mumakhalanso zinthu zimene Yehova amadana nazo monga ciwawa, zaciwelewele, kapena zamizimu. (Ŵelengani Salimo 11:5.) Kodi n’ciyani cingatithandize kupanga zisankho zanzelu pa nkhani ya zosangalatsa?
Tikasankha mabwenzi okonda Yehova, angatithandize kwambili posankha zosangalatsa. Monga tinaonela m’Phunzilo 48, “munthu woyenda ndi anthu anzelu adzakhala wanzelu.” Koma ngati timakonda kuceza na anthu amene sakonda malamulo a Mulungu, ‘tidzapeza mavuto.’—Miyambo 13:20.
2. N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala nayo nthawi imene timathela pa zosangalatsa?
Ngakhale titasankha zosangalatsa zabwino, tiyenelabe kusamala kuti zisatidyele nthawi yoculuka kwambili. Tikapanda kusamala tidzasoŵa nthawi yocita zinthu zofunika kwambili. Baibo imatilimbikitsa ‘kugwilitsa nchito bwino nthawi yathu.’—Ŵelengani Aefeso 5:15, 16.
KUMBANI MOZAMILAPO
Dziŵani mmene mungapangile zisankho zabwino pa nkhani ya zosangalatsa.
3. Pewani zosangalatsa zoipa
N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala posankha zosangalatsa? Tambani VIDIYO, kenako kambilanani mafunso otsatila.
Kodi maseŵelo a m’nthawi zamakedzana ofika mpaka kuphana, akufanana bwanji na zosangalatsa zina zamakono?
Mu vidiyo imeneyi, kodi Danny anaphunzilapo ciyani pa zosangalatsa?
Ŵelengani Aroma 12:9, na kukambilana funso ili:
Kodi lemba limeneli lingakuthandizeni bwanji posankha zosangalatsa?
Kodi ni zinthu ziti zimene Yehova amadana nazo? Ŵelengani Miyambo 6:16, 17, komanso Agalatiya 5:19-21. Pambuyo poŵelenga lililonse la malembawa, kambilanani funso ili:
Pa zimene zachulidwa pa lembali, ni zinthu ziti zofala m’zosangalatsa za masiku ano?
Mmene mungasankhile zosangalatsa mwanzelu
Dzifunseni kuti:
Ciphatikizapo ciyani? Kodi m’cosangalatsa cimeneci muli zinthu zimene Yehova amadana nazo?
Cimacitika nthawi yanji? Kodi cimabwela pa nthawi yoyenela kucita zinthu zofunika kwambili?
Muli anthu otani? Kodi anthu a m’cosangalatsa cimeneco ni osakonda Yehova, amene angakhale mayanjano oipa kwa ine?
Ni cinthu canzelu kutalikilana naco cinthu coopsa ciliconse. Conco, tiyenelanso kukhala kutali na cosangalatsa ciliconse cimene tikuona kuti sicingakhale cabwino kwa ife
4. Gwilitsani nchito nthawi yanu mwanzelu
Tambani VIDIYO, kenako kambilanani funso lotsatila.
Ngakhale kuti m’bale wa mu vidiyo iyi sanali kutamba ciliconse coipa, kodi cinayamba kucitika kwa iye n’ciyani cifukwa cosasamala nayo nthawi yopumula?
Ŵelengani Afilipi 1:10, na kukambilana funso ili:
Kodi lembali lingatithandize bwanji kusamala nayo nthawi yocita zosangulutsa?
5. Sankhani zosangalatsa zoyenela
Ngakhale kuti zosangalatsa zina sizovomelezeka kwa Yehova, pali zinthu zambili zimene tingacite zosangalatsa. Ŵelengani Mlaliki 8:15, komanso Afilipi 4:8, na kukambilana funso ili:
Kodi mungachuleko zosangalatsa zabwino zimene mumakonda?
Zilipo zosangalatsa komanso zosangulutsa zabwino
ANTHU ENA AMAKAMBA KUTI: “Palibe vuto kutamba zosangalatsa mmene muli zaciwawa, zaciwelewele, kapena zamizimu, malinga inu simucitako zinthu zimenezo.”
Nanga inu muganiza bwanji?
CIDULE CAKE
Yehova amafuna kuti tizisankha zosangalatsa zabwino zotikondweletsa.
Mafunso Obweleza
Kodi Mkhristu ayenela kupewa zosangalatsa zotani?
N’cifukwa ciyani tiyenela kusamala nayo nthawi yotayila pa zosangalatsa?
N’cifukwa ciyani muyenela kusankha zosangalatsa zovomelezeka kwa Yehova?
FUFUZANI
Onani kuti ndani ali na udindo wotisankhila zosangalatsa.
Onani mmene mungapangile zisankho zabwino, pa nkhani ya zosangulutsa zimene mungacite panthawi yopumula.
Mu nkhani yakuti “Ndinasiya Ngakhale Kudana ndi Azungu,” onani mmene munthu wina anasinthila zosangalatsa zake.
“Baibulo Limasintha Anthu” (Nsanja ya Olonda, February 1, 2010)
Onani mmene mayi akupangila cisankho canzelu pa zosangalatsa zophatikizapo zamizimu.