-
Levitiko 4:11, 12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Koma kunena za chikopa cha ngʼombeyo ndi nyama yake yonse pamodzi ndi mutu wake, ziboda zake, matumbo ake ndi ndowe zake,+ 12 kutanthauza ngʼombe yonseyo, aziitenga nʼkupita nayo kunja kwa msasa. Azipita nayo kumalo oyera kumene amataya phulusa* ndipo aziiwotcha pamoto+ wa nkhuni. Aziwotcha ngʼombeyo kumalo otayako phulusa.
-
-
Levitiko 16:27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
27 Ngʼombe yamphongo ya nsembe yamachimo ndi mbuzi ya nsembe yamachimo, zimene magazi ake analowa nawo mʼmalo oyera pokaphimba machimo, azipita nazo kunja kwa msasa ndipo aziwotcha pamoto zikopa zake, nyama ndi ndowe zake.+
-