-
Levitiko 7:34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
34 Ine ndikutenga chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku ndiponso mwendo womwe ndi gawo lopatulika. Ndikutenga zimenezi pansembe zamgwirizano za Aisiraeli nʼkuzipereka kwa Aroni wansembe ndi ana ake. Limeneli ndi lamulo kwa Aisiraeli mpaka kalekale.+
-
-
Levitiko 10:14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Mudyenso chidale cha nsembe yoyendetsa uku ndi uku ndi mwendo wa gawo lopatulika.+ Muzidyere pamalo amene ayeretsedwa, inuyo, ana anu aamuna ndi ana anu aakazi.+ Muzichita zimenezi chifukwa zinthu zimenezi zaperekedwa kwa inu monga gawo lanu ndi gawo la ana anu kuchokera pa nsembe zamgwirizano za Aisiraeli.
-
-
Deuteronomo 18:4Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
4 Aziperekanso kwa wansembe mbewu zawo zoyambirira kucha, vinyo wawo watsopano, mafuta awo ndi ubweya wa nkhosa zawo umene ameta moyambirira.+
-