-
Deuteronomo 1:26-28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
26 Koma inu munakana kupita kukalowa mʼdzikolo, ndipo munapandukira lamulo la Yehova Mulungu wanu.+ 27 Choncho munapitiriza kungʼungʼudza mʼmatenti anu kuti, ‘Yehova anatitulutsa mʼdziko la Iguputo chifukwa choti ankadana nafe, ndipo akufuna kutipereka mʼmanja mwa Aamori kuti atiwononge. 28 Kodi tikupita kuti? Abale athu achititsa mantha mitima yathu*+ potiuza kuti, “Kumeneko kuli anthu amphamvu zawo ndiponso ataliatali kuposa ifeyo ndipo mizinda yawo ndi ikuluikulu komanso ili ndi mipanda yolimba kwambiri yofika kumwamba.*+ Tinaonakonso ana a Anaki+ kumeneko.”’
-