23 Yehova Mulungu wanu adzawapereka kwa inu ndipo mudzawagonjetsa mobwerezabwereza mpaka onse atatha.+ 24 Adzapereka mafumu awo mʼmanja mwanu,+ ndipo inu mudzafafanize mayina awo padziko lapansi.+ Palibe munthu amene adzalimbane ndi inu+ mpaka mutawawononga.+