-
Numeri 21:13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Atasamuka kumeneko anakamanga msasa mʼdera la chigwa cha Arinoni, mʼchipululu chochokera kumalire a dziko la Aamori. Chigwa cha Arinoni+ chinali malire pakati pa dziko la Mowabu ndi la Aamori.
-
-
Oweruza 11:17, 18Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
17 Kenako anatumiza uthenga kwa mfumu ya Edomu+ wakuti: “Tiloleni tidutse nawo mʼdziko lanu,” koma mfumu ya Edomu inakana. Anatumizanso uthenga kwa mfumu ya Mowabu,+ koma nayonso sinalole. Choncho Aisiraeli anapitiriza kukhala ku Kadesi.+ 18 Pamene ankadutsa mʼchipululu, analambalala dziko la Edomu+ ndi la Mowabu. Anadutsa chakumʼmawa kwa dziko la Mowabu+ nʼkukamanga misasa mʼchigawo cha Arinoni. Iwo sanadutse malire a Mowabu chifukwa Arinoni ndi amene anali malire a Mowabu.+
-