-
Deuteronomo 21:6-9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Ndiyeno akulu onse amumzinda umene uli pafupi ndi munthu wakufayo azisamba mʼmanja+ pamwamba pa ngʼombe imene yathyoledwa khosi mʼchigwa ija. 7 Ndipo iwo azinena kuti, ‘Manja athu sanakhetse magazi awa, ndiponso maso athu sanaone magaziwa akukhetsedwa. 8 Inu Yehova, musaimbe mlanduwu anthu anu Aisiraeli amene munawawombola,+ ndipo musalole kuti mlandu wa magazi a munthu wosalakwa ukhale pa anthu anu Aisiraeli.’+ Akatero iwo sadzaimbidwa mlandu wa magaziwo. 9 Mukadzachita zimenezi mudzachotsa mlandu wa magazi a munthu wosalakwa pakati panu, chifukwa mudzakhala mutachita zinthu zoyenera pamaso pa Yehova.
-