-
1 Samueli 13:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Sauli anasankha amuna 3,000 a mu Isiraeli. Pa amunawa, 2,000 anali ndi Sauliyo ku Mikimasi komanso kudera lamapiri la Beteli. Pamene amuna 1,000 anali ndi Yonatani+ ku Gibeya+ wa ku Benjamini. Anthu ena onse otsalawo anawauza kuti abwerere kumatenti awo. 3 Kenako Yonatani anapha asilikali a Afilisiti+ amene anali ku Geba+ ndipo Afilisiti anamva zimenezi. Zitatero Sauli analiza lipenga la nyanga ya nkhosa+ mʼdziko lonse nʼkunena kuti: “Tamverani Aheberi nonse!”
-