-
Salimo 18:31-42Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Kodi pali Mulungu winanso woposa Yehova?+
Nanga pali thanthwe linanso kupatula Mulungu wathu?+
33 Iye amachititsa mapazi anga kuti akhale ngati a mbawala,
Amachititsa kuti ndiime pamalo okwera.+
34 Iye amaphunzitsa manja anga kumenya nkhondo,
Manja anga angathe kukunga uta wakopa.*
35 Inu mumandipatsa chishango chanu chachipulumutso,+
Dzanja lanu lamanja limandithandiza,*
Ndipo kudzichepetsa kwanu nʼkumene kumandikweza.+
36 Mumakulitsa njira kuti mapazi anga azidutsamo,
Ndipo mapazi anga sadzaterereka.+
37 Ndidzathamangitsa adani anga nʼkuwapeza,
Sindidzabwerera mpaka onse nditawawononga.
38 Ndidzawaphwanya kuti asadzukenso.+
Ndidzawapondaponda ndi mapazi anga.
39 Inu mudzandipatsa mphamvu kuti ndithe kumenya nkhondo.
Mudzachititsa kuti adani anga agonje.+
41 Iwo amafuula kuti athandizidwe, koma palibe amene angawapulumutse,
Amafika pofuulira Yehova, koma iye samawayankha.
42 Ndidzawapera ndipo adzakhala ngati fumbi louluzika ndi mphepo.
Ndidzawakhuthula ngati matope mumsewu.
-