-
1 Mbiri 11:12-14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Wotsatira wake anali Eliezara+ mwana wa Dodo, mwana wa Ahohi.+ Iye anali mmodzi wa asilikali atatu amphamvuwo. 13 Iye anali ndi Davide ku Pasi-damimu+ kumene Afilisiti anasonkhana kuti amenyane nawo. Kumeneko kunali munda wa balere wambiri ndipo anthu anali atathawa chifukwa choopa Afilisitiwo. 14 Koma iye anaima pakati pa mundawo nʼkuuteteza ndipo anapitiriza kupha Afilisiti, moti Yehova anawathandiza kuti apambane.+
-