-
2 Mbiri 18:8-11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Choncho mfumu ya Isiraeli inaitana nduna yapanyumba ya mfumu nʼkuiuza kuti: “Kamutenge Mikaya mwana wa Imula, ndipo ubwere naye mwamsanga.”+ 9 Mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda anakhala pabwalo* lapageti lolowera mumzinda wa Samariya. Aliyense anakhala pampando wake wachifumu atavala zovala zachifumu ndipo aneneri onse ankalosera pamaso pawo. 10 Ndiyeno Zedekiya mwana wa Kenaana anapanga nyanga zachitsulo nʼkunena kuti: “Yehova wanena kuti, ‘Ndi nyanga izi mudzagunda Asiriya mpaka kuwapha onse.’” 11 Aneneri ena onse ankaloseranso zofanana ndi zimenezi. Ankanena kuti: “Pitani ku Ramoti-giliyadi ndipo mukapambana.+ Yehova akapereka mzindawo kwa inu mfumu.”
-