-
2 Mbiri 18:12-16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Munthu amene anatumidwa kukaitana Mikaya anauza Mikayayo kuti: “Aneneri onse alankhula zabwino kwa mfumu. Nawenso ukalankhule zabwino.”+ 13 Koma Mikaya anati: “Ndikulumbira mʼdzina la Yehova Mulungu wamoyo, zimene Mulungu angandiuze nʼzimene ndikanene.”+ 14 Kenako anafika kwa mfumu ndipo mfumuyo inamufunsa kuti: “Mikaya, kodi tipite kukamenyana ndi Ramoti-giliyadi kapena tisapite?” Nthawi yomweyo Mikaya anayankha kuti: “Pitani mukapambana ndipo mzindawo ukaperekedwa kwa inu mfumu.” 15 Ndiyeno mfumuyo inamufunsa kuti: “Kodi ndikulumbiritse kangati kuti uzindiuza zoona zokhazokha mʼdzina la Yehova?” 16 Choncho Mikaya anati: “Ndikuona Aisiraeli onse atabalalika mʼmapiri ngati nkhosa zopanda mʼbusa.+ Ndipo Yehova anati: ‘Amenewa alibe mtsogoleri. Aliyense abwerere kunyumba kwake mwamtendere.’”
-