-
2 Mbiri 18:18-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
18 Mikaya anati: “Choncho imvani mawu a Yehova: Ndinaona Yehova atakhala pampando wake wachifumu+ ndipo gulu lonse lakumwamba+ linaimirira kumanja ndi kumanzere kwake.+ 19 Ndiyeno Yehova anati, ‘Ndani akapusitse Ahabu mfumu ya Isiraeli, kuti apite ku Ramoti-giliyadi nʼkukafa?’ Choncho angelo osiyanasiyana ankanena maganizo awo, wina izi, wina izi. 20 Kenako mngelo*+ wina anabwera kudzaima pamaso pa Yehova nʼkunena kuti, ‘Ine ndikamʼpusitsa.’ Yehova anamufunsa kuti, ‘Ukamʼpusitsa bwanji?’ 21 Iye anayankha kuti, ‘Ndipita kukakhala mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri ake onse.’ Ndiyeno Mulungu anati, ‘Ukamʼpusitsadi ndipo zikakuyendera bwino. Pita ukachite zimenezo.’ 22 Choncho Yehova waika mzimu wabodza mʼkamwa mwa aneneri anuwa,+ koma Yehovayo wanena kuti inuyo muona tsoka.”
-