-
2 Mbiri 18:23-27Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Zedekiya+ mwana wa Kenaana anapita pomwe panali Mikaya+ nʼkumumenya mbama+ ndipo ananena kuti: “Zingatheke bwanji kuti mzimu wa Yehova undidutse nʼkukalankhula ndi iwe?”+ 24 Mikaya anayankha kuti: “Udzadziwa zimenezo tsiku limene udzalowe mʼchipinda chamkati kukabisala.” 25 Ndiyeno mfumu ya Isiraeli inati: “Mtengeni Mikaya mupite naye kwa Amoni mkulu wa mzinda ndi Yowasi mwana wa mfumu. 26 Mukawauze kuti, ‘Mfumu yanena kuti: “Mʼtsekereni munthu uyu.+ Muzimʼpatsa chakudya chochepa ndi madzi ochepa mpaka nditabwerako mwamtendere.”’” 27 Koma Mikaya anati: “Mukakabwerakodi mwamtendere ndiye kuti Yehova sanalankhule nane.”+ Ananenanso kuti: “Anthu inu, mawu angawa muwakumbukire.”
-