-
2 Mbiri 18:28-32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Zitatero mfumu ya Isiraeli ndi Yehosafati mfumu ya Yuda ananyamuka kupita ku Ramoti-giliyadi.+ 29 Mfumu ya Isiraeli inauza Yehosafati kuti: “Ine ndidzisintha kuti ndisadziwike ndipo ndimenya nawo nkhondo. Koma inuyo muvale zovala zanu zachifumu.” Choncho mfumu ya Isiraeli inadzisintha nʼkuyamba kumenya nawo nkhondo. 30 Mfumu ya Siriya inali italamula akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaleta kuti: “Musakamenyane ndi wina aliyense, wamngʼono kapena wamkulu, koma mfumu ya Isiraeli yokha basi.” 31 Akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaleta aja atangomuona Yehosafati, anaganiza kuti: “Mfumu ya Isiraeli ija ndi imeneyi.” Choncho anatembenuka kuti amenyane naye ndipo Yehosafati anayamba kukuwa kuti anthu amuthandize,+ ndipo Yehova anamuthandiza. Nthawi yomweyo Mulungu anawachititsa kuti amusiye. 32 Akuluakulu oyangʼanira asilikali okwera magaletawo atangozindikira kuti si mfumu ya Isiraeli, anasiya kumuthamangitsa nʼkubwerera.
-