-
2 Mbiri 18:33, 34Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
33 Koma munthu wina anaponya muvi wake chiponyeponye ndipo unakabaya mfumu ya Isiraeli pamalo olumikizira a chovala chake chokhala ndi mamba achitsulo. Choncho mfumuyo inauza woyendetsa galeta lake kuti: “Bwera udzanditulutse mʼbwalo lankhondoli chifukwa ndavulala kwambiri.”+ 34 Nkhondoyo inafika poopsa tsiku limenelo ndipo mfumuyo anaiimiritsa mʼgaleta nʼkuitsamiritsa kugaletalo moyangʼanizana ndi Asiriya mpaka madzulo. Mfumuyo inafa pamene dzuwa linkalowa.+
-