1 Mafumu 10:22 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 22 Zinali choncho chifukwa mfumuyo inali ndi zombo za ku Tarisi+ zomwe zinkayenda panyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu. Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombozo zinkabweretsa golide, siliva, minyanga ya njovu,+ anyani ndi mbalame zotchedwa pikoko. Ezekieli 27:15 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 15 Anthu a ku Dedani+ ankachita nawe malonda. Iwe unalemba ntchito anthu oti azikuchitira malonda mʼzilumba zambiri. Anthuwo ankakupatsa minyanga+ komanso mitengo ya phingo ngati mphatso.*
22 Zinali choncho chifukwa mfumuyo inali ndi zombo za ku Tarisi+ zomwe zinkayenda panyanja pamodzi ndi zombo za Hiramu. Kamodzi pa zaka zitatu zilizonse, zombozo zinkabweretsa golide, siliva, minyanga ya njovu,+ anyani ndi mbalame zotchedwa pikoko.
15 Anthu a ku Dedani+ ankachita nawe malonda. Iwe unalemba ntchito anthu oti azikuchitira malonda mʼzilumba zambiri. Anthuwo ankakupatsa minyanga+ komanso mitengo ya phingo ngati mphatso.*