-
2 Mafumu 8:20-22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
20 Mʼmasiku a Yehoramu, Aedomu anagalukira Yuda+ ndipo kenako anasankha mfumu yoti iziwalamulira.+ 21 Choncho Yehoramu anapita ku Zairi pamodzi ndi magaleta ake onse. Kumeneko, iye ananyamuka usiku nʼkukapha Aedomu amene anamuzungulira. Anaphanso atsogoleri a asilikali okwera magaleta ndipo asilikali ena onse anathawira kumatenti awo. 22 Koma Aedomu anapitirizabe kugalukira Yuda mpaka lero. Pa nthawi imeneyi mʼpamenenso Libina+ anagalukira Yuda.
-