-
2 Mbiri 20:35-37Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Kenako Yehosafati mfumu ya Yuda anachita mgwirizano ndi Ahaziya mfumu ya Isiraeli amene ankachita zoipa.+ 36 Choncho anayamba kugwira naye ntchito yopanga zombo zopita ku Tarisi.+ Zombozo anazipangira ku Ezioni-geberi.+ 37 Koma Eliezere mwana wa Dodavahu wa ku Maresa analosera zinthu zotsutsana ndi Yehosafati kuti: “Chifukwa chakuti mwachita mgwirizano ndi Ahaziya, Yehova awononga ntchito yanu.”+ Choncho zombozo zinasweka+ ndipo sizinathenso kupita ku Tarisi.
-