-
Levitiko 21:6-8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
6 Azikhala oyera kwa Mulungu wawo+ ndipo asamadetse dzina la Mulungu wawo,+ chifukwa iwowa amapereka kwa Yehova nsembe zowotcha pamoto, zomwe ndi chakudya cha Mulungu wawo, choncho azikhala oyera.+ 7 Wansembe asamakwatire hule+ kapena mkazi amene wataya unamwali wake. Asamakwatirenso mkazi amene mwamuna wake anamusiya ukwati,+ chifukwa wansembeyo ndi woyera kwa Mulungu wake. 8 Muzimuona kuti ndi woyera+ chifukwa ndi amene amapereka chakudya cha Mulungu wanu. Azikhala woyera kwa inu, chifukwa ine Yehova, amene ndikukupatulani, ndine woyera.+
-