-
Nehemiya 6:10-12Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kenako ndinapita kunyumba kwa Semaya mwana wa Delaya, mwana wa Mehetabele, amene anali atadzitsekera mʼnyumba. Iye anandiuza kuti: “Tiye tigwirizane nthawi yoti tikakumane kunyumba ya Mulungu woona, mʼkachisi ndipo tikatseke zitseko za kachisiyo. Chifukwa akubwera kudzakupha, akubwera kudzakupha usiku.” 11 Koma ndinamuyankha kuti: “Kodi mwamuna ngati ine ndingathawe? Kodi munthu ngati ine angalowe mʼkachisi nʼkukhala ndi moyo?+ Ine sindikalowamo!” 12 Kenako ndinazindikira kuti sanatumidwe ndi Mulungu, koma Tobia ndi Sanibalati+ ndi amene anamulemba ganyu kuti andinamize ndi ulosi wabodzawu.
-