7Zimenezi zitachitika, mu ulamuliro wa mfumu Aritasasita+ ya ku Perisiya, Ezara*+ anabwera ku Yerusalemu kuchokera ku Babulo. Iye anali mwana wa Seraya.+ Seraya anali mwana wa Azariya, Azariya anali mwana wa Hilikiya,+
6 Nthawi yonseyi ine sindinali ku Yerusalemu, chifukwa mʼchaka cha 32+ cha ulamuliro wa Aritasasita+ mfumu ya Babulo, ndinabwerera kwa mfumu. Ndiyeno patapita nthawi, ndinapempha mfumuyo kuti ndichoke kwakanthawi.