1Awa ndi mawu a Nehemiya*+ mwana wa Hakaliya. Mʼmwezi wa Kisilevi,* mʼchaka cha 20, ine ndinali kunyumba ya mfumu yokhala ndi mpanda wolimba kwambiri ya ku Susani.*+
2 Ndikuona masomphenyawo ndinapezeka kuti ndili kunyumba yachifumu* ku Susani,+ imene ili mʼchigawo cha Elamu.+ Ndinaona masomphenyawa kuti ndinali mʼmphepete mwa mtsinje wa Ulai.