-
2 Mafumu 24:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 Mfumuyo inatenga anthu onse a ku Yerusalemu, akalonga onse,+ asilikali onse amphamvu, amisiri onse ndiponso anthu osula zitsulo*+ nʼkupita nawo ku Babulo. Anthu onse amene inawatenga analipo 10,000. Palibe amene anatsala, kupatulapo anthu osauka kwambiri a mʼdzikolo.+ 15 Choncho iye anatenga Yehoyakini+ nʼkupita naye ku Babulo.+ Ku Yerusalemu anatenganso mayi a mfumuyo, akazi ake, nduna za panyumba yake komanso akuluakulu a mʼdzikolo, nʼkupita nawo ku Babulo.
-
-
1 Mbiri 3:16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Mwana wa Yehoyakimu+ anali Yekoniya. Yekoniya anabereka Zedekiya.
-
-
2 Mbiri 36:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Yehoyakini+ anayamba kulamulira ali ndi zaka 18 ndipo analamulira miyezi itatu ndi masiku 10 ku Yerusalemu. Iye ankachita zoipa pamaso pa Yehova.+ 10 Chakumayambiriro kwa chaka, Mfumu Nebukadinezara inatuma asilikali ake omwe anakamutenga nʼkubwera naye ku Babulo+ limodzi ndi zinthu zabwino zamʼnyumba ya Yehova.+ Komanso Nebukadinezara anasankha Zedekiya, yemwe anali mʼbale wa bambo ake a Yehoyakini, kuti akhale mfumu ya Yuda ndi Yerusalemu.+
-
-
Yeremiya 22:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Kodi munthu uyu Koniya, wangokhala chiwiya chonyozeka komanso chophwanyika,
Chiwiya chimene palibe amene akuchifuna?
Nʼchifukwa chiyani iyeyu ndi ana ake agwetsedwa pansi
Nʼkuponyedwa mʼdziko limene sakulidziwa?’+
-
-
Yeremiya 24:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 Kenako Yehova anandionetsa madengu awiri a nkhuyu amene anali patsogolo pa kachisi wa Yehova. Anandionetsa madenguwo pambuyo poti Nebukadinezara* mfumu ya Babulo watenga Yekoniya*+ mwana wa Yehoyakimu,+ mfumu ya Yuda, pamodzi ndi akalonga a Yuda, amisiri komanso anthu osula zitsulo,* kuchoka ku Yerusalemu nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo.+
-