-
Yobu 30:23Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
23 Chifukwa ndikudziwa kuti mudzandipereka ku imfa,
Kunyumba imene aliyense wamoyo adzapitako.
-
-
Mlaliki 8:8Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
8 Palibe munthu amene ali ndi mphamvu pa mzimu* kapena amene angaletse mzimuwo kuti usachoke. Mofanana ndi zimenezi palibenso amene ali ndi mphamvu pa tsiku la imfa.+ Palibe amene amaloledwa kuchoka kunkhondo ndipo mofanana ndi zimenezi, anthu amene amachita zoipa, kuipako sikudzawalola kuti athawe.*
-
-
Mlaliki 9:2Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Anthu onse mapeto awo ndi ofanana,+ munthu wolungama komanso munthu woipa,+ munthu wabwino ndi woyera komanso munthu wodetsedwa, munthu amene amapereka nsembe komanso amene sapereka nsembe. Munthu wabwino nʼchimodzimodzi ndi munthu wochimwa. Munthu amene amachita lumbiro nʼchimodzimodzi ndi amene amaganiza kaye asanachite lumbiro.
-