-
Deuteronomo 12:31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
31 Musamalambire Yehova Mulungu wanu mwa njira imeneyi, chifukwa iwo amachitira milungu yawo zinthu zonse zonyansa zimene Yehova amadana nazo. Iwo amafika ngakhale powotcha ana awo aamuna ndi aakazi pamoto kuti ikhale nsembe kwa milungu yawo.+
-
-
2 Mafumu 16:1Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
16 Ahazi+ mwana wa Yotamu mfumu ya Yuda anakhala mfumu mʼchaka cha 17 cha Peka mwana wa Remaliya.
-
-
Yeremiya 7:30, 31Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
30 ‘Chifukwa mbadwa za Yuda zachita zinthu zoipa mʼmaso mwanga,’ akutero Yehova. ‘Aika mafano awo onyansa mʼnyumba imene imadziwika ndi dzina langa nʼcholinga choti aidetse.+ 31 Iwo amanga malo okwera ku Tofeti, mʼChigwa cha Mwana wa Hinomu,*+ kuti aziwotcha ana awo aamuna ndi ana awo aakazi pamoto,+ chinthu chimene sindinawalamule kuti azichita ndiponso chimene sindinachiganizirepo mumtima mwanga.’*+
-