-
Deuteronomo 7:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Iye adzakukondani, kukudalitsani komanso kukuchulukitsani. Adzakudalitsani ndithu pokupatsani ana ambiri,*+ adzadalitsa zokolola za nthaka yanu, mbewu zanu, vinyo wanu watsopano, mafuta anu,+ ana a ngʼombe zanu ndi ana a nkhosa zanu, mʼdziko limene analumbira kwa makolo anu kuti adzakupatsani.+ 14 Inu mudzakhala odalitsika kwambiri mwa anthu onse.+ Pakati panu sipadzapezeka mwamuna, mkazi kapena chiweto chosabereka.+
-