-
Numeri 20:11Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
11 Mose atatero, anakweza dzanja lake nʼkumenya thanthwelo kawiri ndi ndodo yake. Ndiyeno madzi ambiri anayamba kutuluka ndipo gulu lonselo linayamba kumwa madziwo limodzi ndi ziweto zawo.+
-
-
Deuteronomo 8:14, 15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
14 musakalole kuti mtima wanu ukayambe kunyada+ nʼkukuchititsani kuiwala Yehova Mulungu wanu amene anakutulutsani mʼdziko la Iguputo, mʼnyumba yaukapolo,+ 15 amene anakuyendetsani mʼchipululu chachikulu ndi chochititsa mantha,+ chokhala ndi njoka zapoizoni, zinkhanira ndiponso nthaka youma yopanda madzi. Iye anachititsa kuti madzi atuluke pamwala wolimba,+
-
-
Salimo 107:35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
35 Chipululu amachisandutsa dambo la madzi,
Ndipo dziko louma amalisandutsa dera la akasupe amadzi.+
-