2 Samueli 6:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Davide ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli ankasangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Ankaimbanso zeze, zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana. 1 Mbiri 15:19 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 19 Hemani,+ Asafu+ ndi Etani anawasankha kuti aziimba ndi zinganga zakopa.*+ 1 Mbiri 16:5 Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika 5 Mtsogoleri wawo anali Asafu,+ wachiwiri wake anali Zekariya. Ndipo Yeyeli, Semiramoti, Yehiela, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obedi-edomu ndi Yeyeli+ ankaimba ndi zoimbira za zingwe ndiponso azeze.+ Asafu ankaimba zinganga.+
5 Davide ndi anthu onse a nyumba ya Isiraeli ankasangalala pamaso pa Yehova, akuimba mitundu yonse ya zoimbira za mtengo wofanana ndi mtengo wa mkungudza. Ankaimbanso zeze, zoimbira za zingwe,+ zinganga+ ndi maseche+ osiyanasiyana.
5 Mtsogoleri wawo anali Asafu,+ wachiwiri wake anali Zekariya. Ndipo Yeyeli, Semiramoti, Yehiela, Matitiya, Eliyabu, Benaya, Obedi-edomu ndi Yeyeli+ ankaimba ndi zoimbira za zingwe ndiponso azeze.+ Asafu ankaimba zinganga.+