-
Miyambo 6:32-35Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
32 Aliyense wochita chigololo ndi mkazi ndi wopanda nzeru.*
Amene amachita zimenezi amadzibweretsera mavuto aakulu pa moyo wake.+
34 Chifukwa nsanje imachititsa kuti mwamuna wake akwiye kwambiri.
Pomubwezera sadzamva chisoni.+
35 Iye sadzavomera chipukuta misozi chilichonse,*
Ndipo sadzapepeseka ngakhale utapereka mphatso yaikulu bwanji.
-