18 Ndiyeno Samueli ankatumikira+ pamaso pa Yehova ndipo ankavala efodi wansalu,+ ngakhale kuti anali mwana. 19 Komanso chaka chilichonse amayi ake ankamusokera kamkanjo kodula manja. Iwo ankamupititsira kamalayako akapita ndi amuna awo kukapereka nsembe yapachaka.+