-
2 Mafumu 18:13, 14Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
13 Mʼchaka cha 14 cha Mfumu Hezekiya, Senakeribu mfumu ya Asuri+ anabwera kudzaukira mizinda yonse ya Yuda yokhala ndi mipanda yolimba kwambiri ndipo analanda mizindayo.+ 14 Choncho Hezekiya mfumu ya Yuda anatumiza uthenga kwa mfumu ya Asuri ku Lakisi, wakuti: “Wolakwa ndine. Siyani kundiukira. Ndikupatsani chilichonse chimene mungandilamule.” Zitatero mfumu ya Asuri inalamula Hezekiya mfumu ya Yuda kuti apereke matalente* 300 a siliva ndi matalente 30 a golide.
-
-
2 Mbiri 28:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Yehova anatsitsa Ayuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Isiraeli, popeza analekerera Ayuda kuchita makhalidwe oipa zomwe zinachititsa kuti achite zinthu zambiri zosakhulupirika kwa Yehova.
20 Patapita nthawi, Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri anabwera kwa iye ndipo anangomuwonjezera mavuto+ mʼmalo momulimbikitsa.
-