-
2 Mbiri 28:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Yehova anatsitsa Ayuda chifukwa cha Ahazi mfumu ya Isiraeli, popeza analekerera Ayuda kuchita makhalidwe oipa zomwe zinachititsa kuti achite zinthu zambiri zosakhulupirika kwa Yehova.
20 Patapita nthawi, Tigilati-pilenesere+ mfumu ya Asuri anabwera kwa iye ndipo anangomuwonjezera mavuto+ mʼmalo momulimbikitsa.
-
-
Yesaya 10:28-32Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
29 Iwo adutsa powolokera mtsinje.
Usiku agona ku Geba.+
30 Iwe mwana wamkazi wa Galimu, lira ndi kufuula kwambiri.
Khala tcheru iwe Laisa,
Iwenso Anatoti womvetsa chisoni!+
31 Madimena wathawa.
Anthu okhala ku Gebimu abisala.
32 Tsiku lomwelo iye akaima ku Nobu.+
Iye akuopseza ndi chibakera phiri la mwana wamkazi wa Ziyoni,*
Phiri limene pali Yerusalemu.
-