-
Yeremiya 9:2, 3Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
2 Ndikanakonda ndikanakhala ndi malo ogona anthu apaulendo mʼchipululu.
Zikanatero, ndikanasiya anthu a mtundu wanga nʼkuwachokera,
Chifukwa onse ndi achigololo,+
Gulu la anthu ochita zachinyengo.
3 Iwo ndi okonzeka kunama ngati uta umene wakungidwa.
Dzikolo ladzaza ndi chinyengo ndipo palibe amene ali wokhulupirika.+
“Iwo akuchita zoipa motsatizanatsatizana,
Ndipo akundinyalanyaza,”+ akutero Yehova.
-