-
Yeremiya 21:7Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 ‘Yehova wanena kuti: “Kenako Zedekiya mfumu ya Yuda, atumiki ake ndi anthu amumzindawu, onse amene adzapulumuke ku mliri, lupanga ndi njala yaikulu, ndidzawapereka mʼmanja mwa Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo. Ndidzawapereka mʼmanja mwa adani awo komanso mʼmanja mwa amene akufuna kuchotsa moyo wawo.+ Nebukadinezara adzawapha ndi lupanga ndipo sadzawamvera chisoni, kuwakomera mtima kapena kuwachitira chifundo.”’+
-
-
Ezekieli 12:12, 13Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Mtsogoleri amene ali pakati pawo adzanyamula katundu wake paphewa nʼkuchoka kuli mdima. Adzabowola khoma nʼkutulutsirapo katundu wake.+ Iye adzaphimba nkhope kuti asaone pansi. 13 Ine ndidzamuponyera ukonde wanga ndipo iye adzakodwa mu ukonde wanga wosakira.+ Kenako ndidzamupititsa ku Babulo, kudziko la Akasidi. Koma iye sadzaliona dzikolo ndipo adzafera komweko.+
-