Watchtower LAIBULALE YA PA INTANETI
Watchtower
LAIBULALE YA PA INTANETI
Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • BAIBULO
  • MABUKU
  • Misonkhano
  • Yeremiya 14:13
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 13 Nditamva zimenezi ndinanena kuti: “Mayo ine! Inu Yehova Ambuye Wamkulu Koposa. Aneneri akuuza anthuwo kuti, ‘Simudzawonongedwa ndi lupanga ndipo njala yaikulu sidzakugwerani, koma Mulungu adzakupatsani mtendere weniweni mʼmalo ano.’”+

  • Yeremiya 23:16, 17
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 16 Yehova wa magulu ankhondo akumwamba wanena kuti:

      “Musamvere mawu a aneneri amene akulosera kwa inu.+

      Iwo akungokupusitsani.*

      Iwo akulankhula masomphenya amumtima mwawo,+

      Osati ochokera mʼkamwa mwa Yehova.+

      17 Mobwerezabwereza iwo akuuza anthu amene sakundilemekeza kuti,

      ‘Yehova wanena kuti: “Inu mudzakhala pa mtendere.”’+

      Ndipo aliyense amene amatsatira mtima wake woipawo akumuuza kuti,

      ‘Tsoka silidzakugwerani.’+

  • Yeremiya 27:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Musamvere mawu a aneneri amene akukuuzani kuti, ‘Simudzatumikira mfumu ya Babulo,’+ chifukwa zimene akulosera kwa inuzo ndi zabodza.+

  • Yeremiya 28:1, 2
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 28 Ndiyeno mʼchaka chomwecho, chaka cha 4, mʼmwezi wa 5, kumayambiriro kwa ulamuliro wa Zedekiya+ mfumu ya Yuda, mneneri Hananiya mwana wa Azuri, wa ku Gibiyoni,+ anauza Yeremiya mʼnyumba ya Yehova pamaso pa ansembe ndi anthu onse kuti: 2 “Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli, wanena kuti, ‘Ndithyola goli la mfumu ya Babulo.+

  • Maliro 2:14
    Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
    • 14 Masomphenya amene aneneri anu anaona ndi abodza komanso achabechabe,+

      Ndipo sanaulule zolakwa zanu nʼcholinga choti musatengedwe kupita ku ukapolo,+

      Koma ankaona masomphenya abodza komanso okusocheretsani.+

Mabuku a Chinenero Chamanja cha ku Malawi (1993-2025)
Tulukani
Lowani
  • Chinenero Chamanja cha ku Malawi
  • tumizirani
  • Zimene Mumakonda
  • Copyright © 2025 Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania
  • Zoyenera Kutsatira
  • Nkhani Yosunga Chinsinsi
  • zachinsinsi
  • JW.ORG
  • Lowani
tumizirani