-
Yeremiya 18:7-10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
7 Nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndizula, kugwetsa ndi kuwononga mtundu uliwonse wa anthu kapena ufumu,+ 8 ndiyeno mtundu wa anthuwo nʼkusiya zoipa zimene ndinawadzudzula nazo, inenso ndidzasintha maganizo anga okhudza tsoka limene ndimafuna kuwagwetsera.+ 9 Koma nthawi iliyonse imene ndinganene kuti ndimanga ndi kudzala mtundu wa anthu kapena ufumu, 10 ndiyeno mtundu wa anthuwo nʼkumachita zoipa pamaso panga ndiponso osamvera mawu anga, inenso ndidzasintha maganizo anga okhudza zinthu zabwino zimene ndinkafuna kuwachitira.’
-
-
Yeremiya 24:5, 6Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
5 “Yehova Mulungu wa Isiraeli wanena kuti, ‘Anthu amene anatengedwa ku Yuda kupita ku ukapolo, amene ndinawachotsa mʼdziko lino nʼkuwatumiza kudziko la Akasidi ali ngati nkhuyu zabwino zimenezi. Ndidzawaona kuti ndi anthu abwino. 6 Maso anga adzakhala pa iwo kuti ndiwachitire zabwino ndipo ndidzachititsa kuti abwerere mʼdziko lino.+ Ndidzachititsa kuti zinthu ziziwayendera bwino ndipo sindidzawawononga. Ndidzawadzala ndipo sindidzawazula.+
-