-
Yeremiya 39:9, 10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 Nebuzaradani+ mkulu wa asilikali olondera mfumu, anatenga anthu ena onse otsala mumzindamo, anthu amene anathawira kwa mfumu ya Babulo ndi anthu ena onse amene anapulumuka nʼkupita nawo ku ukapolo ku Babulo.
10 Koma Nebuzaradani mkulu wa asilikali olondera mfumu, anasiya mʼdziko la Yuda ena mwa anthu amene anali osauka kwambiri omwe analibe kalikonse. Pa tsiku limenelo anawapatsanso minda ndi minda ya mpesa kuti azilima.*+
-