-
Deuteronomo 29:24, 25Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
24 ana anu ndi alendo komanso mitundu yonse adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova wachitira dzikoli zimenezi?+ Nʼchiyani chachititsa kuti mkwiyo wake uyake kwambiri chonchi?’ 25 Ndiyeno iwo adzanena kuti, ‘Nʼchifukwa chakuti anaphwanya pangano la Yehova,+ Mulungu wa makolo awo, limene anapangana nawo pamene ankawatulutsa mʼdziko la Iguputo.+
-
-
2 Mbiri 7:21, 22Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
21 Ndipo nyumbayi idzakhala bwinja. Aliyense wodutsa pafupi adzaiyangʼana modabwa,+ ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chiyani Yehova anachitira zimenezi dzikoli komanso nyumbayi?’+ 22 Ndipo adzati, ‘Nʼchifukwa chakuti anasiya Yehova+ Mulungu wa makolo awo amene anawatulutsa mʼdziko la Iguputo+ ndipo anatenga milungu ina nʼkumaigwadira ndi kuitumikira.+ Nʼchifukwa chake iye anawabweretsera tsoka lonseli.’”+
-