-
2 Mbiri 7:19, 20Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
19 Koma inuyo mukadzatembenuka nʼkusiya kutsatira malamulo anga amene ndakupatsani, komanso mukadzapita kukatumikira milungu ina ndi kuigwadira,+ 20 ineyo ndidzachotsa Aisiraeli mʼdziko limene ndawapatsa+ ndipo nyumba iyi yomwe ndaiyeretsa chifukwa cha dzina langa, ndidzaichotsa pamaso panga. Ndidzachititsa anthu kuinyoza ndiponso kuinenera mawu achipongwe pakati pa mitundu yonse ya anthu.+
-