-
Yeremiya 6:12-15Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
12 Nyumba zawo limodzi ndi minda yawo komanso akazi awo,
Zidzaperekedwa kwa anthu ena.+
Chifukwa ndidzatambasula dzanja langa nʼkuwononga anthu okhala mʼdzikolo,” akutero Yehova.
13 “Chifukwa aliyense kuyambira wamngʼono mpaka wamkulu, akupeza phindu mwachinyengo.+
Kuyambira mneneri mpaka wansembe, aliyense akuchita zachinyengo.+
14 Iwo akuyesa kuchiritsa mwachinyengo kuwonongeka kwa anthu anga* ponena kuti,
‘Kuli mtendere! Kuli mtendere!’
Pamene kulibe mtendere.+
15 Kodi iwo amachita manyazi ndi zinthu zonyansa zimene achita?
Iwo sachita manyazi ngakhale pangʼono,
Ndipo sadziwa nʼkomwe kuchita manyazi.+
Choncho iwo adzagwa pamodzi ndi anthu amene akugwa.
Ndikamadzawapatsa chilango, iwo adzapunthwa,” akutero Yehova.
-
-
Yeremiya 27:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 ‘Choncho musamvere aneneri, anthu ochita zamaula, olota maloto, ochita zamatsenga ndi obwebweta amene ali pakati panu ndipo akukuuzani kuti: “Simudzatumikira mfumu ya Babulo.”
-
-
Ezekieli 22:28Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
28 Koma aneneri amʼdzikomo apaka laimu zochita za akalongawo. Iwo amaona masomphenya onama ndipo amalosera zinthu zabodza.+ Aneneriwo amanena kuti: “Yehova, Ambuye Wamkulu Koposa, wanena kuti,” pamene Yehova sananene chilichonse.
-