-
Salimo 139:15, 16Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
15 Mafupa anga sanali obisika kwa inu
Pa nthawi imene ndinkapangidwa kumalo amene aliyense sakanatha kuona,
Pamene munkandiwomba ngati nsalu mʼmalo apansi kwambiri padziko lapansi.+
16 Maso anu anandiona ngakhale pamene ndinali mluza.*
Ziwalo zanga zonse zinalembedwa mʼbuku lanu
Mʼbukumo munalembedwa za masiku amene zinapangidwa,
Zinalembedwa chiwalo chilichonse chisanapangidwe.
-