-
Yeremiya 25:9Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
9 ndikuitana mafuko onse akumpoto,”+ akutero Yehova, “ndikuitananso Mfumu Nebukadinezara* ya ku Babulo, mtumiki wanga.+ Ndibweretsa anthu amenewa kuti aukire dziko lino+ ndi anthu amene akukhala mmenemo komanso mitundu yonse imene yakuzungulirani.+ Ndidzakuwonongani inuyo ndi mitundu yonse yokuzungulirani ndipo ndidzakusandutsani chinthu chochititsa mantha chimene anthu azidzachiimbira mluzu ndipo malo anu adzakhala mabwinja mpaka kalekale.
-
-
Yeremiya 43:10Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika
-
-
10 Kenako ukawauze kuti, ‘Yehova wa magulu ankhondo akumwamba, Mulungu wa Isiraeli wanena kuti: “Ine ndikuitana Nebukadinezara* mfumu ya Babulo mtumiki wanga,+ ndipo ndidzaika mpando wake wachifumu pamwamba penipeni pa miyala imene ndaibisayi. Iye adzamanga tenti yake yachifumu pamwamba pa miyala imeneyi.+
-